Categories
YESAYA

YESAYA 34

Yehova aipidwa ndi amitundu

1 Idzani pafupi,amitunduinu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.

2 Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa.

3 Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.

4 Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.

5 Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.

6 Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira, ndi ophedwa ambiri m’dziko la Edomu.

7 Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng’ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta.

8 Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu waZiyoni.

9 Ndipo mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi fumbilo lidzasandukasulufure, ndi dziko lakelo lidzasanduka matope oyaka moto.

10 Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wake udzakwera nthawi zonse; m’mibadwomibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi.

11 Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khwangwala adzakhala m’menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.

12 Iwo adzaitana mfulu zake zilowe mu ufumu, koma sizidzaonekako; ndi akalonga ake onse adzakhala chabe.

13 Ndipo minga idzamera m’nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m’malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.

14 Ndipo zilombo za m’chipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzake; inde manchichi adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.

15 Kumeneko kadzidzi adzapanga chisa chake, naikira, naumatira, naswa mumthunzi mwake; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzake.

16 Funani inu m’buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo.

17 Ndipo Iye wachita maere, chifukwa cha zilombozi, ndipo dzanja lake lazigawira dzikolo ndi chingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwomibadwo, zidzakhala m’menemo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/34-55cbd2d4a1b6d597e31c867817d41ce5.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *