Categories
YESAYA

YESAYA 37

Mwa mantha Hezekiya aitana mneneri Yesaya

1 Ndipo panali pamene mfumu Hezekiya anamva, anang’amba zovala zake, navala chiguduli, nalowa m’nyumba ya Yehova.

2 Ndipo anatumiza Eliyakimu, wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi akulu a nsembe, atafunda chiguduli, kwa Yesaya,mneneri, mwana wa Amozi.

3 Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la vuto, ndi lakudzudzula ndi chitonzo; pakuti nthawi yake yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.

4 Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asiriya mbuyake inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; chifukwa chake, kweza pemphero lako chifukwa cha otsala osiyidwa.

5 Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya.

6 Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asiriya andilalatira Ine.

7 Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka kudziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m’dziko la kwao.

Uthenga wa Sanakeribu wa kwa Hezekiya

8 Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asiriya ilikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inachoka ku Lakisi.

9 Ndipo anamva anthu alinkunena za Tirihaka, mfumu ya Kusi, Iye watuluka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,

10 Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti,Yerusalemusadzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asiriya.

11 Taona, iwe wamva chimene mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?

12 Kodi milungu yaamitunduyaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefe ndi ana a Edeni amene anali mu Telasara.

13 Ili kuti mfumu ya ku Hamati, ndi mfumu ya ku Aripadi, ndi mfumu yamzinda wa ku Sefaravaimu, ya ku Hena, ndi Iva?

Pemphero la Hezekiya

14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m’manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova, nati,

16 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala paakerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

17 Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.

18 Zoonadi, Yehova, mafumu a Asiriya anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.

19 Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.

20 Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m’manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.

Kuyankha kwa Yehova mwa Yesaya

21 Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Popeza wandipemphera za Senakeribu mfumu ya Asiriya,

22 awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi waZiyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.

23 Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.

24 Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa.

25 Ine ndakumba ndi kumwa madzi, ndidzaumitsa mitsinje yonse ya Ejipito ndi kuphazi kwanga.

26 Kodi iwe sunamve, kuti ndinachita ichi kale, ndi kuchikonza nthawi zakale? Tsopano Ine ndachikwaniritsa, kuti iwe ukapasule mizinda yamalinga, isanduke miunda.

27 Chifukwa chake okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa m’munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamatsindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.

28 Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.

29 Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m’makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m’mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m’milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m’njira yomwe unadzerayo.

30 Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yampesa ndi kudya chipatso chake.

31 Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala chipatso pamwamba.

32 Pakuti mudzaoneka mu Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m’phiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.

33 Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzafika mu mzinda muno, ngakhale kuponyapo muvi, ngakhale kufika patsogolo pake ndi chikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.

34 Pa njira yomwe anadzerayo, abwerera yomweyo, ndipo sadzafika mu mzinda uno, ati Yehova.

35 Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno, kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.

36 Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m’zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.

37 Ndipo Senakeribu, mfumu ya Asiriya, anachoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Ninive.

38 Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m’nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere, ana ake anamupha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake, analamulira m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/37-760756ba4c9a11a4fd1e122154e4f05b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *