Aneneratu za kupasuka kwa mafano a ku Babiloni
1 Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng’ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.
2 Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m’ndende.
3 Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m’mimba, ndi kukusenzani chibadwire;
4 ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.
5 Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?
6 Amene ataya golide, namtulutsa m’thumba, ndi kuyesasilivandi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
7 Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m’malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m’zovuta zake.
8 Kumbukirani ichi, nimuchilimike, mudzikumbutsenso, olakwa inu.
9 Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine;
10 ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;
11 ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum’mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.
12 Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutali ndi chilungamo;
13 ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m’Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/46-28fb4dd565eb6de3d8fcb10f8bd0b881.mp3?version_id=1068—