Israele akonzedwanso napulumutsidwa
1 Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang’anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.
2 Yang’anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa.
3 Pakuti Yehova watonthoza mtima waZiyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m’menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
4 Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu.
5 Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.
6 Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang’ane pansi padziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m’menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.
7 Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.
8 Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.
9 Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?
10 Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?
11 Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m’kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.
12 Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
13 waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m’mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza?
14 Wam’nsinga wowerama adzamasulidwa posachedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, chakudya chake sichidzasowa.
15 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ake akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lake.
16 Ndipo ndaika mau anga m’kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
Agalamuke Yerusalemu
17 Galamuka, galamuka, imiriraYerusalemuamene unamwa m’dzanja la Yehova chikho cha ukali wake; iwe wamwa mbale ya chikho chonjenjemeretsa ndi kuchigugudiza.
18 Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana aamuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.
19 Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? Bwinja ndi chipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji?
20 Ana ako aamuna akomoka; agona pamutu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako.
21 Chifukwa chake imva ichi tsopano, iwe wovutidwa ndi woledzera koma si ndi vinyo ai;
22 atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ake, Taona, ndachotsa m’dzanja mwako chikho chonjenjemeretsa, ngakhale mbale ya chikho cha ukali wanga; iwe sudzamwa icho kawirinso.
23 Ndidzachiika m’dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/51-5daa0348e0c8f93bb18d0417b932ae4d.mp3?version_id=1068—