Categories
EKSODO

EKSODO 29

Mapatulidwe a ansembe

1 Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng’ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,

2 ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.

3 Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng’ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.

4 Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo lachihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m’madzi.

5 Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am’kati, ndi mwinjiro waefodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m’chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;

6 ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.

7 Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.

8 Ndipo ubwere nao ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya am’kati.

9 Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m’chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna.

10 Ndipo ubwere nayo ng’ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa ng’ombe yamphongoyo.

11 Nuphe ng’ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako.

12 Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng’ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.

13 Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.

14 Koma nyama ya ng’ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.

15 Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

16 Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira.

17 Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m’ziwalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziwalo zake, ndi pamutu pake.

18 Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

19 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

20 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.

21 Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.

22 Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam’mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;

23 ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;

24 ndipo uike zonsezi m’manja a Aroni, ndi m’manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

25 Pamenepo uzilandire m’manja mwao, ndi kuzipsereza paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

26 Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.

27 Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam’mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;

28 ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.

29 Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake aamuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala;

30 mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m’malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m’chihema chokomanako kutumikira m’malo opatulika.

31 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nyama yake m’malo opatulika.

32 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mudengu, pa khomo la chihema chokomanako.

33 Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.

34 Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m’mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi.

35 Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake aamuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.

36 Nukonze ng’ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.

37 Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.

Nsembe ya masiku onse

38 Koma izi ndizo uzikonza paguwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.

39 Mwanawankhosawina ukonze m’mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo;

40 ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.

41 Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m’mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

42 Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.

43 Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.

44 Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.

45 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele, ndi kukhala Mulungu wao.

46 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/29-93258c3d3ed363f80d63cca94d51cbc5.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 30

Za guwa la nsembe lofukizapo

1 Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wakasiya.

2 Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zituluke m’mwemo.

3 Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.

4 Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.

5 Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.

6 Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.

7 Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m’mawa ndi m’mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize.

8 Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu.

9 Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa; musathirepo nsembe yothira.

10 Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m’chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.

Ndalama za chiombolo

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12 Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.

13 Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.

14 Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova.

15 Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

16 Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito yachihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

Za mkhate wakusambiramo

17 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,

18 Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

19 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;

20 pakulowa iwo m’chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

21 asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.

Za mafuta odzoza opatulika

22 Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,

23 Udzitengerenso zonunkhira zomveka,murewoyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

24 ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;

25 ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osakanizika monga mwa machitidwe a wosakaniza; akhale mafuta odzoza opatulika.

26 Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni,

27 ndi guwalo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikaponyali ndi zipangizo zake,

28 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake.

29 Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.

30 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake aamuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.

31 Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.

32 Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.

33 Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.

Za chofukiza

34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndilubaniloona; miyeso yofanana;

35 ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosakaniza mwa machitidwe a wosakaniza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika;

36 nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m’chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.

37 Koma za chofukizacho uchikonze, musadzikonzere nokha china, mwa makonzedwe ake amene; muchiyese chopatulika cha Yehova.

38 Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/30-c25c7d78d3908644122c0a69ae6bd9de.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 31

Za amisiri opanga ntchitoyi

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Taona ndaitana ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;

3 ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m’ntchito zilizonse,

4 kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide ndisilivandi mkuwa,

5 ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kozokota mtengo, kuchita ntchito zilizonse.

6 Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m’mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;

7 chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chili pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho;

8 ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikaponyali choona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo;

9 ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake;

10 ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe;

11 ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe.

Masungidwe a tsiku la Sabata

12 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

13 Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.

14 Ndipo muzisungaSabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m’mwemo, munthu ameneyo achotsedwe mwa anthu a mtundu wake.

15 Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.

16 Chifukwa chake ana a Israele azisunga Sabata, kuchita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;

17 ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.

18 Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/31-cf42ebddb65ecda68aa3385c9fbd3bff.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 32

Fano la mwanawang’ombe

1 Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m’phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

2 Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m’makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine.

3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m’makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni

4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang’ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m’dziko la Ejipito.

5 Pakuchiona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pake; ndipo Aroni anafuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.

6 Ndipo m’mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.

7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m’dziko la Ejipito wadziipsa;

8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang’ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m’dziko la Ejipito.

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;

10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu.

11 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?

12 Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m’mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.

13 Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.

14 Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake.

Mose atsikira anthu opembedza fanolo

15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m’phirimo, magome awiri a mboni ali m’dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe.

16 Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.

17 Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono.

18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa ogonjetsa, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang’ombe.

19 Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang’ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m’manja mwake, nawaswa m’tsinde mwa phiri.

20 Ndipo anatenga mwanawang’ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele.

21 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?

22 Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba choipa.

23 Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

24 Ndipo ndinanena nao, Aliyense ali naye golide amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m’moto, ndimo anatulukamo mwanawang’ombe uyu.

Alangidwa anthuwo

25 Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,

26 Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana aamuna onse a Levi anasonkhana kwa iye.

27 Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m’chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake.

28 Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu.

29 Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino.

Mose atetezera anthu kwa Mulungu

30 Ndipo kunali m’mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu.

31 Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide.

32 Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m’buku lanu limene munalembera,

33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m’buku langa.

34 Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.

35 Ndipo Yehova anakantha anthu, chifukwa anapanga mwanawang’ombe amene Aroni anapanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/32-0c2c04628693ed7e83ec8132501396db.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 33

Mulungu akuti sadzawaperekezanso

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m’dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;

2 ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

3 kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.

4 Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake.

5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni.

6 Ndipo ana a Israele anazichotsera zokometsera zao kuyambira paphiri la Horebu.

7 Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha,Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.

8 Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m’chihemacho.

9 Ndipo kunali, pakulowa Mose m’chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.

10 Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m’chihemamo.

Mose apeza ufulu pamaso pa Mulungu

12 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitse amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga.

13 Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.

14 Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.

15 Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kuchokera kuno.

16 Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?

17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako.

18 Ndipo anati, Ndionetsenitu ulemerero wanu.

19 Ndipo Iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo.

20 Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.

21 Ndipo Yehova anati, Taona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe;

22 ndipo kudzakhala, pakupitira ulemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitirira;

23 ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzaona m’mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/33-ebfaed38c0ce2d565d85ee98b1242b97.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 34

Magome atsopano a Malamulowo

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.

2 Nukonzekeretu m’mawa, nukwere m’mawa m’phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba paphiri.

3 Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m’phiri monse; ndi zoweta zazing’ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno.

4 Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m’phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m’dzanja mwake magome awiri amiyala.

5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, nafuula dzina la Yehova.

6 Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;

7 wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

8 Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi nalambira.

9 Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.

10 Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitike zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.

11 Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

12 Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;

13 koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

14 pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

15 ungachite pangano ndi iwo okhala m’dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;

16 ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.

17 Usadzipangire milungu yoyenga.

18 Uzisungachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m’mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.

19 Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng’ombe ndi za nkhosa.

20 Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndimwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu aamuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.

21 Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.

22 Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.

23 Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi.

24 Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.

25 Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero chaPaskaasaisiye kufikira m’mawa.

26 Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.

27 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.

28 Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.

Nkhope ya Mose inyezimira

29 Ndipo kunali pakutsika Mose paphiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m’dzanja lake la Mose, pakutsika iye m’phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye.

30 Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israele anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yake linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza.

31 Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.

32 Ndipo atatero, ana onse a Israele anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m’phiri la Sinai.

33 Ndipo Mose atatha kulankhula nao, anaika chophimba pankhope pake.

34 Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza.

35 Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/34-281fb80b1270fb8040054bccb19e26d6.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 35

Zopereka zofunika za pa chihemacho

1 Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.

2 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika,Sabatalakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.

3 Musamasonkha moto m’nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata.

4 Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova analamula ndi kuti,

5 Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; golide, ndisiliva, ndi mkuwa;

6 ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

7 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;

8 ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma;

9 ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika yaefodi, ndi ya chapachifuwa.

Zipangizo za m’malo opatulika

10 Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova analamula;

11 chihema, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao;

12 likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka;

13 gome, ndi mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;

14 ndi choikaponyali cha kuunika, ndi zipangizo zake, ndi nyali zake, ndi mafuta a kuunika;

15 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la chihema;

16 guwa la nsembe yopsereza, ndi sefa wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;

17 nsalu zotchingira za kubwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo;

18 zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zao;

19 zovala za kutumikira nazo m’malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe.

Anthu abwera ndi zopereka mwaufulu

20 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka pamaso pa Mose.

21 Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito yachihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.

22 Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m’makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.

23 Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.

24 Yense wakupereka chopereka cha siliva ndi mkuwa, anabwera nacho chopereka cha Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wakasiya wa ku machitidwe onse a ntchitoyi, anabwera nao.

25 Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

26 Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

27 Ndi akulu anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kuchapachifuwa;

28 ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma.

29 Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.

Za amisiri opanga ntchitoyi

30 Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;

31 ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m’ntchito zilizonse;

32 kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa;

33 ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mitengo, kuchita m’ntchito zilizonse zaluso.

34 Ndipo anaika m’mtima mwake kuti alangize ena, iye ndi Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani.

35 Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/35-3d8f746aa0121f7f9936cf9c6ca936fe.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 36

1 Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m’mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.

Amisiri alandira zopereka za anthu

2 Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m’mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.

3 Ndipo analandira kwa Mose chopereka chonse, chimene ana a Israele adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zaufulu, m’mawa ndi m’mawa.

4 Ndipo aluso onse, akuchita ntchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya ntchito yao analinkuchita;

5 nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova analamula ichitike.

6 Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mu chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.

7 Popeza zipangizo zinakwanira ntchito yonse ichitike, zinatsalakonso.

Mapangidwe a chihemacho

8 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndiakerubi, ntchito ya mmisiri.

9 Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inai; nsalu zonse zinafanana muyeso wao.

10 Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake.

11 Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m’mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m’mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri.

12 Anaika magango makumi asanu pansalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m’mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake.

13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo chihema chinakhala chimodzi.

14 Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi.

15 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.

16 Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha.

17 Ndipo anapanga magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china.

18 Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.

19 Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.

20 Ndipo anapanga matabwa a chihema, oimirika, a mtengo wakasiya.

21 Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu.

22 Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a chihema.

23 Ndipo anapanga matabwa a chihema; matabwa makumi awiri a ku mbali ya kumwera, kumwera;

24 napanga makamwa makumi anai asilivapansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri.

25 Ndi ku mbali ina ya chihema, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi awiri, ndi makamwa ao makumi anai asiliva;

26 makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.

27 Ndi ku mbali ya kumbuyo ya chihema kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi.

28 Anapanganso matabwa awiri a kungodya za chihema, m’mbali zake ziwiri.

29 Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizika pamodzi pamutu pake ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pangodya ziwiri.

30 Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu. Ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi.

31 Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya chihema,

32 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzake ya chihema, ndi mitanda isanu ya matabwa a chihema ali pa mbali ya kumadzulo.

33 Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo.

34 Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide.

35 Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.

36 Ndipo anaipangira mizati inai ya kasiya, nazikuta ndi golide; zokowera zao zinali zagolide; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.

37 Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula;

38 ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/36-4c189ebe90c4ff6fb9c2fc97ca738c37.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 37

Mapangidwe a likasa

1 Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;

2 ndipo analikuta ndi golide woona m’kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake.

3 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina.

4 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide.

5 Ndipo anapisa mphiko m’mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.

6 Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.

7 Anapangansoakerubiawiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo;

8 kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m’chotetezerapo, pa mathungo ake awiri.

9 Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m’mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao.

Gome la mkate woonekera

10 Ndipo anapanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;

11 ndipo analikuta ndi golide woona, nalipangira mkombero wagolide pozungulira pake.

12 Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m’kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolide.

13 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide, naika mphetezo pangodya zake zinai zokhala pa miyendo yake inai.

14 Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo.

15 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide, kunyamulira nazo gomelo.

16 Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golide woona.

Choikaponyali

17 Ndipo anapanga choikaponyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikaponyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m’mwemo;

18 ndi m’mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikaponyali zotuluka m’mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikaponyali zotuluka m’mbali yake ina;

19 pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m’choikaponyali.

20 Ndipo pa choikaponyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;

21 ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m’mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m’mwemo.

22 Mitu yao ndi mphanda zao zinatuluka m’mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golide woona.

23 Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.

24 Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golide woona.

Guwa lofukizapo

25 Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m’mwemo.

26 Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake.

27 Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake, pangodya zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.

28 Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide.

29 Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/37-cfce4ddd7aa618987444fc998efb0a7a.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 38

Mapangidwe a guwa la nsembe yopsereza

1 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu.

2 Ndipo anapanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zinakhala zotuluka m’mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.

3 Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.

4 Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake.

5 Ndipo anayengera mathungo anai a sefa wamkuwayo mphete zinai, zikhale zopisamo mphiko.

6 Napanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi mkuwa.

7 Ndipo anapisa mphikozo mu mphetezo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.

Za mkhate wakusambiramo

8 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo lachihema chokomanako.

Bwalo la chihema

9 Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

10 nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva.

11 Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ake makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.

12 Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsalu zotchingira za mikono makumi asanu, nsichi zake khumi, ndi makamwa ake khumi; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.

13 Ndi pa mbali ya kum’mawa, kum’mawa, mikono makumi asanu.

14 Nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu;

15 momwemonso pa mbali ina: pa mbali ino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu.

16 Nsalu zotchingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa.

17 Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.

18 Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zotchingira za pabwalo.

19 Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva.

20 Ndi zichiri zonse za chihema, ndi za bwalo lake pozungulira, nza mkuwa.

Mawerengo a zopereka za pa chihema

21 Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.

22 Ndipo Bezalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, anapanga zonse zimene Yehova adauza Mose.

23 Ndi pamodzi naye Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

24 Golide yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golide wa choperekacho, ndicho matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

25 Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli chikwi chimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

26 Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.

27 Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.

28 Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizanitsa pamodzi.

29 Ndi mkuwa wa choperekacho ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai.

30 Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,

31 ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/38-8143c5d1aa71ad453b45692cb442e49f.mp3?version_id=1068—