Mulungu alamulira anthu za ku Sinai
1 Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m’dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m’chipululu cha Sinai.
2 Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m’chipululu cha Sinai, namanga tsasa m’chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji paphirilo.
3 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m’phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,
4 Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.
5 Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusungachipanganochanga, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.
7 Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.
8 Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.
11 Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m’phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;
13 dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m’phirimo.
14 Ndipo Mose anatsika m’phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.
15 Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.
16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m’mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
17 Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde paphiri.
18 Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m’moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m’ng’anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
19 Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.
20 Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.
21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.
22 Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova.
23 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m’phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m’phirimo, ndi kulipatula.
24 Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.
25 Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/19-7b37211ef39c25bbca9628a4716d8952.mp3?version_id=1068—