Categories
MASALIMO

MASALIMO 94

Mulungu wolungama adzaweruza oipa

1 Mulungu wakubwezera chilango,

Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.

2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi:

Bwezerani odzikuza choyenera iwo.

3 Oipa adzatumpha ndi chimwemwe kufikira liti, Yehova?

Oipa adzatero kufikira liti?

4 Anena mau, alankhula zowawa;

adzitamandira onse ochita zopanda pake.

5 Aphwanya anthu anu, Yehova,

nazunza cholowa chanu.

6 Amapha wamasiye ndi mlendo,

nawapha ana amasiye.

7 Ndipo amati, Yehova sachipenya,

ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira.

8 Zindikirani, opulukira inu mwa anthu;

ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?

9 Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva?

Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?

10 Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula?

Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru?

11 Yehova adziwa zolingalira za munthu,

kuti zili zachabe.

12 Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;

ndi kumphunzitsa m’chilamulo chanu;

13 kuti mumpumitse masiku oipa;

kufikira atakumbira woipa mbuna.

14 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake,

ndipo sadzataya cholowa chake.

15 Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo,

ndipo oongoka mtima onse adzachitsata.

16 Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa?

Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?

17 Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,

moyo wanga ukadakhala kuli chete.

18 Pamene ndinati, Literereka phazi langa,

chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.

19 Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga,

zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

20 Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza,

wakupanga chovuta chikhale lamulo?

21 Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama,

namtsutsa wa mwazi wosachimwa.

22 Koma Yehova wakhala msanje wanga;

ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

23 Ndipo anawabwezera zopanda pake zao,

nadzawaononga m’choipa chao;

Yehova Mulungu wathu adzawaononga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/94-5b364ab52b3af2c250190f9d84302da4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 95

Adandaulira anthu alemekeze namvere Mulungu wao wamkulu

1 Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera;

tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.

2 Tidze nacho chiyamiko pamaso pake,

timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.

3 Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu;

ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse.

4 Malo ozama a dziko lapansi ali m’dzanja lake;

chuma cha m’mapiri chomwe ndi chake.

5 Nyanja ndi yake, anailenga;

ndipo manja ake anaumba dziko louma.

6 Tiyeni, tipembedze tiwerame;

tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.

7 Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,

ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,

ndi nkhosa za m’dzanja mwake.

Lero, mukamva mau ake!

8 Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba,

ngati tsiku la ku Masa m’chipululu.

9 Pamene makolo anu anandisuntha,

anandiyesa, anapenyanso chochita Ine.

10 Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni,

ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima,

ndipo sadziwa njira zanga.

11 Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga,

ngati adzalowa mpumulo wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/95-34c60166f30781937b950777181dfa92.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 96

Onse a pansi pano ndi am’mwamba omwe alemekeze Mulungu

1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;

muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.

2 Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake;

lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

3 Fotokozerani ulemerero wake mwaamitundu;

zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.

4 Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;

ayenera amuope koposa milungu yonse.

5 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano,

koma Yehova analenga zakumwamba.

6 Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu.

M’malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.

7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,

mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

8 Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake;

bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.

9 Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa,

njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.

10 Nenani mwaamitundu, Yehova achita ufumu;

dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;

adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.

11 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;

nyanja ibume mwa kudzala kwake.

12 Munda ukondwerere ndi zonse zili m’mwemo;

pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera.

13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;

pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi

Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,

ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/96-3de72cfe218307b222ad2e70bf7c0450.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 97

Ulemerero wa ufumu wa Mulungu

1 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere;

zisumbu zambiri zikondwerere.

2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;

chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa

mpando wake wachifumu.

3 Moto umtsogolera,

nupsereza otsutsana naye pozungulirapo.

4 Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu;

dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.

5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,

pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6 Kumwamba kulalikira chilungamo chake,

ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.

7 Onse akutumikira fano losema,

akudzitamandira nao mafano, achite manyazi:

Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

8 Ziyonianamva nakondwera,

nasekerera ana aakazi a Yuda;

chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.

9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi,

ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.

10 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa:

Iye asunga moyo wa okondedwa ake;

awalanditsa m’manja mwa oipa.

11 Kuunika kufesekera wolungama,

ndi chikondwerero oongoka mtima.

12 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;

ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/97-6c65878c73f9e757113cb19d347e9fb8.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 98

Alemekeze Mulungu pa chifundo ndi choonadi chao

Salimo.

1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;

popeza anachita zodabwitsa:

Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera,

zinamchitira chipulumutso.

2 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake;

anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu.

3 Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake

kunyumba ya Israele;

malekezero onse a dziko lapansi

anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

4 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;

kuwitsani ndi kufuulira mokondwera;

inde, imbirani zomlemekeza.

5 Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze;

ndi zeze ndi mau a salimo.

6 Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova,

ndi mbetete ndi liu la lipenga.

7 Nyanja ifuule ndi kudzala kwake;

dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;

8 mitsinje iombe m’manja;

mapiri afuule pamodzi mokondwera.

9 Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;

adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,

ndipo mitundu ya anthu molunjika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/98-ac8f04ab9533726087f9e969fcb70cf5.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 99

Mulungu wamkulu wachifundo alemekezedwe

1 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;

Iye akhala pakati paakerubi; dziko lapansi ligwedezeke.

2 Yehova ndiye wamkulu muZiyoni;

ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

3 Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa.

Ili ndilo loyera.

4 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo;

Inu mukhazikitsa zolunjika,

muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.

5 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,

ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake:

Iye ndiye Woyera.

6 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni,

ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake;

anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

7 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo:

Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.

8 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:

munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,

mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.

9 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,

ndipo gwadirani paphiri lake loyera;

pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/99-77e66ae4cdf6bfda694f115ffc645d1e.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 100

Olengedwa ndi Mulungu amlemekeze

Salimo la Chiyamiko.

1 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.

2 Tumikirani Yehova ndi chikondwerero:

Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.

3 Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu;

Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake;

ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.

4 Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko,

ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo:

Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.

5 Pakuti Yehova ndiye wabwino;

chifundo chake chimanka muyaya;

ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/100-aa94a0038194128acb99efca962c0162.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 101

Davide akuti adzasamala okhulupirika nadzachotsa oipa

Salimo la Davide.

1 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo;

ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.

2 Ndidzachita mwanzeru m’njira yangwiro;

mudzandidzera liti?

Ndidzayenda m’nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.

3 Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga;

chochita iwo akupatuka padera chindiipira;

sichidzandimamatira.

4 Mtima wopulukira udzandichokera;

sindidzadziwana naye woipa.

5 Wakuneneza mnzake m’tseri ndidzamdula;

wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

6 Maso anga ayang’ana okhulupirika m’dziko, kuti akhale ndi Ine;

iye amene ayenda m’njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.

7 Wakuchita chinyengo sadzakhala m’kati mwa nyumba yanga;

wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.

8 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m’dziko;

kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/101-c79d9d75fa245d4b3f9ed3cd86427ff4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 102

Wopsinjika apempha Mulungu achitire anthu ake chifundo, amitundu nammverenso

Pemphero la Wozunzika, m’mene anakomoka natsanulira cholingalira chake pamaso pa Yehova.

1 Yehova, imvani pemphero langa,

ndipo mfuu wanga ufikire Inu.

2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;

munditchereze khutu lanu;

tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.

3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,

ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.

4 Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota;

popeza ndiiwala kudya mkate wanga.

5 Chifukwa cha liu la kubuula kwanga

mnofu wanga umamatika kumafupa anga.

6 Ndikunga vuwo m’chipululu;

ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.

7 Ndidikira, ndikhala ngati mbalame

ili yokha pamwamba pa tsindwi.

8 Adani anga anditonza tsiku lonse;

akundiyalukirawo alumbirira ine.

9 Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,

ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi,

10 chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu;

popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.

11 Masiku anga akunga mthunzi womka m’tali;

ndipo ine ndauma ngati udzu.

12 Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse;

ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.

13 Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoniZiyoni;

popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.

14 Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake,

nachitira chifundo fumbi lake.

15 Pamenepoamitunduadzaopa dzina la Yehova,

ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.

16 Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,

anaoneka mu ulemerero wake;

17 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,

osapepula pemphero lao.

18 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza;

ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.

19 Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ake opatulika;

Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;

20 kuti amve kubuula kwa wandende;

namasule ana a imfa.

21 Kuti anthu alalikire dzina la Yehova mu Ziyoni,

ndi chilemekezo chake muYerusalemu;

22 Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,

ndi maufumu kuti atumikire Yehova.

23 Iye analanda mphamvu yanga panjira;

anachepsa masiku anga.

24 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga:

Zaka zanu zikhalira m’mibadwomibadwo.

25 Munakhazika dziko lapansi kalelo;

ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.

26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala:

Inde, zidzatha zonse ngati chovala;

mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:

27 Koma Inu ndinu yemweyo,

ndi zaka zanu sizifikira kutha.

28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa,

ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/102-49465b440a1a1f3bc67c9b0b36b64c7c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 103

Alemekeze Yehova pa chifundo chake chachikulu

Salimo la Davide.

1 Lemekeza Yehova, moyo wanga;

ndi zonse za m’kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.

2 Lemekeza Yehova, moyo wanga,

ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:

3 Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;

nachiritsa nthenda zako zonse;

4 amene aombola moyo wako ungaonongeke;

nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:

5 Amene akhutitsa m’kamwa mwako ndi zabwino;

nabweza ubwana wako unge mphungu.

6 Yehova achitira onse osautsidwa

chilungamo ndi chiweruzo.

7 Analangiza Mose njira zake,

ndi ana a Israele machitidwe ake.

8 Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo,

wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka.

9 Sadzatsutsana nao nthawi zonse;

ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.

10 Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu,

kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.

11 Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi,

motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.

12 Monga kum’mawa kutanimpha ndi kumadzulo,

momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.

13 Monga atate achitira ana ake chifundo,

Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.

14 Popeza adziwa mapangidwe athu;

akumbukira kuti ife ndife fumbi.

15 Koma munthu, masiku ake akunga udzu;

aphuka monga duwa lakuthengo.

16 Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe:

Ndi malo ake salidziwanso.

17 Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba

kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye,

ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

18 kwa iwo akusungachipanganochake,

ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.

19 Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba;

ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.

20 Lemekezani Yehova, inuangeloake;

a mphamvu zolimba, akuchita mau ake,

akumvera liu la mau ake.

21 Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse;

inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.

22 Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse,

ponseponse pali ufumu wake:

Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/103-bb77833f2fd6c75b7d2f1ad734162366.mp3?version_id=1068—