Categories
MASALIMO

MASALIMO 84

Okhala m’nyumba ya Yehova ndiwo amwai

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Gititi; Salimo la ana a Kora.

1 Pokhala Inu mpotikonda ndithu,

Yehova wa makamu!

2 Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova;

mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.

3 Mbawanso inapeza nyumba,

ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake,

pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,

mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

4 Odala iwo akugonera m’nyumba mwanu;

akulemekezani chilemekezere.

5 Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu;

mumtima mwake muli makwalala a kuZiyoni.

6 Popyola chigwa cha kulira misozi achiyesa cha akasupe;

inde mvula ya chizimalupsa ichidzaza ndi madalitso.

7 Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,

aoneka pamaso pa Mulungu muZiyoni.

8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa.

Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo.

9 Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu;

ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.

10 Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma

koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.

Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga,

kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.

11 Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa;

Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero;

sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

12 Yehova wa makamu,

wodala munthu wakukhulupirira Inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/84-e7d9f9ab67bd1354cd497363362f5251.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 85

Akumbutsa Mulungu madalitso akale, apempha awabwereze

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la ana a Kora.

1 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova;

munabweza ukapolo wa Yakobo.

2 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu,

munafotsera zolakwa zao zonse.

3 Munabweza kuzaza kwanu konse;

munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.

4 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu,

nimuletse udani wanu wa pa ife.

5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?

Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?

6 Kodi simudzatipatsanso moyo,

kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?

7 Tionetseni chifundo chanu, Yehova,

tipatseni chipulumutso chanu.

8 Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova;

pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake,

ndi okondedwa ake;

koma asabwererenso kuchita zopusa.

9 Indedi chipulumutso chake chili pafupi

ndi iwo akumuopa Iye;

kuti m’dziko mwathu mukhale ulemu.

10 Chifundo ndi choonadi zakomanizana;

chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.

11 Choonadi chiphukira m’dziko;

ndi chilungamo chasuzumira chili m’mwamba.

12 Inde Yehova adzapereka zokoma;

ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.

13 Chilungamo chidzamtsogolera;

ndipo chidzamkonzera mapazi ake njira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/85-c4c844fc1b8f723f7281b828236e7378.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 86

Davide apempha Mulungu kolimba amlanditse

Pemphero la Davide.

1 Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;

pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.

2 Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;

Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.

3 Mundichitire chifundo, Ambuye;

pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.

4 Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;

pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.

5 Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,

ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.

6 Tcherani khutu pemphero langa, Yehova;

nimumvere mau a kupemba kwanga.

7 Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;

popeza mudzandivomereza.

8 Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;

ndipo palibe ntchito zonga zanu.

9 Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye;

nadzalemekeza dzina lanu.

10 Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa;

Inu ndinu Mulungu, nokhanu.

11 Mundionetse njira yanu, Yehova;

ndidzayenda m’choonadi chanu,

muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

12 Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga,

ndi mtima wanga wonse;

ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.

13 Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu;

ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.

14 Mulungu, odzikuza andiukira,

ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,

ndipo sanaike Inu pamaso pao.

15 Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo,

wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.

16 Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo;

mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,

ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

17 Mundichitire chizindikiro choti chabwino;

kuti ondida achione, nachite manyazi,

popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/86-c3329e477997094a5e689f1421a56f9d.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 87

Yehova akonda Ziyoni

Salimo la ana a Kora. Nyimbo.

1 Maziko ake ali m’mapiri oyera.

2 Yehova akonda zipata zaZiyoni

koposa zokhalamo zonse za Yakobo.

3 Mzinda wa Mulungu, inu,

akunenerani zakukulemekezani.

4 Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine;

taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi;

uyu anabadwa komweko.

5 Ndipo adzanena za Ziyoni,

uyu ndi uyo anabadwa m’mwemo;

ndipo Wam’mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.

6 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu,

uyu anabadwa komweko.

7 Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati,

akasupe anga onse ali mwa inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/87-8028e33da24193bb61a5791c0db3b52c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 88

Wa Salimo atchula masautso ake, napempha Mulungu amdalitse kuimfa

Nyimbo, Salimo la ana a Kora. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Mahalati Leanoti. Chilangizo cha Hemani Mwezara.

1 Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,

ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.

2 Pemphero langa lidze pamaso panu;

munditcherere khutu kukuwa kwanga.

3 Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto,

ndi moyo wanga wayandikira kumanda.

4 Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;

ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu.

5 Wotayika pakati pa akufa,

ngati ophedwa akugona m’manda,

amene simuwakumbukiranso;

ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.

6 Munandiika kunsi kwa dzenje,

kuli mdima, kozama.

7 Mkwiyo wanu utsamira pa ine,

ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.

8 Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;

munandiika ndiwakhalire chonyansa.

Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.

9 Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga:

Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;

nditambalitsira manja anga kwa Inu.

10 Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa?

Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?

11 Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi,

chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?

12 Zodabwitsa zanu zidzadziwika mumdima kodi,

ndi chilungamo chanu m’dziko la chiiwaliko?

13 Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova,

ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.

14 Yehova mutayiranji moyo wanga?

Ndi kundibisira nkhope yanu?

15 Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;

posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.

16 Kuzaza kwanu kwandimiza;

zoopsa zanu zinandiononga.

17 Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;

zinandizinga pamodzi.

18 Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,

odziwana nane akhala kumdima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/88-c65f8280cc82f24316af7a4b441cf06d.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 89

Pangano la Mulungu ndi Davide Mulungu adzapulumutsa anthu ake

Chilangizo cha Etani Mwezara.

1 Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse,

pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu

ku mibadwomibadwo.

2 Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka;

mudzakhazika chikhulupiriko chanu mu Mwamba mwenimweni.

3 Ndinachita chipangano ndi wosankhika wanga,

ndinalumbirira Davide mtumiki wanga.

4 Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse,

ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.

5 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova;

chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.

6 Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?

Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?

7 Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima,

ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.

8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?

Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.

9 Inu ndinu wakuchita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;

pakuuka mafunde ake muwachititsa bata.

10 Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;

munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.

11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu;

munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.

12 Munalenga kumpoto ndi kumwera;

Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m’dzina lanu.

13 Muli nao mkono wanu wolimba;

m’dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.

14 Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu;

chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.

15 Odala anthu odziwa liu la lipenga;

ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

16 Akondwera m’dzina lanu tsiku lonse;

ndipo akwezeka m’chilungamo chanu.

17 Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;

ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.

18 Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova;

ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.

19 Pamenepo munalankhula m’masomphenya ndi okondedwa anu,

ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona;

ndakweza wina wosankhika mwa anthu.

20 Ndapeza Davide mtumiki wanga;

ndamdzoza mafuta anga oyera.

21 Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;

inde mkono wanga udzalimbitsa.

22 Mdani sadzamuumira mtima;

ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza.

23 Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pake;

ndidzapandanso odana naye.

24 Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa

zidzakhala naye;

ndipo nyanga yake idzakwezeka m’dzina langa.

25 Ndipo ndidzaika dzanja lake panyanja,

ndi dzanja lamanja lake pamitsinje.

26 Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,

Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.

27 Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,

womveka wa mafumu a padziko lapansi.

28 Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse,

ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye.

29 Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire,

ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m’mwamba.

30 Ana ake akataya chilamulo changa,

osayenda m’maweruzo anga,

31 nakaipsa malembo anga;

osasunga malamulo anga.

32 Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,

ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.

33 Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse,

ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa.

34 Sindidzaipsa chipangano changa,

kapena kusintha mau otuluka m’milomo yanga.

35 Ndinalumbira kamodzi m’chiyero changa;

sindidzanamizira Davide.

36 Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse,

ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.

37 Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse,

ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.

38 Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,

munakwiya naye wodzozedwa wanu.

39 Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu;

munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.

40 Munapasula makoma ake onse;

munagumula malinga ake.

41 Onse opita panjirapa amfunkhira,

akhala chotonza cha anansi ake.

42 Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;

munakondweretsa adani ake onse.

43 Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake,

osamuimika kunkhondo.

44 Munaleketsa kuwala kwake,

ndipo munagwetsa pansi mpando wachifumu wake.

45 Munafupikitsa masiku a mnyamata wake;

munamkuta nao manyazi.

46 Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;

ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?

47 Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi;

munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?

48 Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?

Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?

49 Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye,

munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu?

50 Kumbukirani, Ambuye, chotonzera atumiki anu;

ndichisenza m’chifuwa mwanga

chochokera kumitundu yonse yaikulu ya anthu.

51 Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho;

chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu.

52 Wodalitsika Yehova kunthawi yonse.

Amen ndi Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/89-440e7f8cad219e8890e8f4ad568878c7.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 90

Mulungu ndiye wachikhalire, munthu ndiye wakutha msanga

Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.

1 Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo

m’mibadwomibadwo.

2 Asanabadwe mapiri,

kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu,

inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha,

Inu ndinu Mulungu.

3 Mubweza munthu akhale fumbi;

nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.

4 Pakuti pamaso panu zaka zikwi

zikhala ngati dzulo, litapita,

ndi monga ulonda wa usiku.

5 Muwatenga ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo;

mamawa akhala ngati msipu wophuka.

6 Mamawa uphuka bwino;

madzulo ausenga, nuuma.

7 Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu;

ndipo m’kuzaza kwanu tiopsedwa.

8 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu,

ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.

9 Pakuti masiku athu onse apitirira mu ukali wanu;

titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.

10 Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri,

kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu;

koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake;

pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.

11 Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,

ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?

12 Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,

kuti tikhale nao mtima wanzeru.

13 Bwerani, Yehova; kufikira liti?

Ndipo alekeni atumiki anu.

14 Mutikhutitse nacho chifundo chanu m’mawa;

ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.

15 Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzawa,

ndi zaka tidaona choipa.

16 Chochita Inu chioneke kwa atumiki anu,

ndi ulemerero wanu pa ana ao.

17 Ndipo chisomo chake cha Ambuye Mulungu wathu chikhalire pa ife;

ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu;

inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/90-f23d46ae4557ce62afa33168355e0332.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 91

Mulungu asungadi wodzipereka kwa Iye

1 Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba

adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

2 Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;

Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

3 Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi,

kumliri wosakaza.

4 Adzakufungatira ndi nthenga zake,

ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake;

choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

5 Sudzaopa choopsa cha usiku,

kapena muvi wopita usana;

6 kapena mliri woyenda mumdima,

kapena chionongeko chakuthera usana.

7 Pambali pako padzagwa chikwi,

ndi zikwi khumi padzanja lamanja lako;

sichidzakuyandikiza iwe.

8 Koma udzapenya ndi maso ako,

nudzaona kubwezera chilango oipa.

9 Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga!

Udaika Wam’mwambamwamba chokhalamo chako;

10 palibe choipa chidzakugwera,

ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.

11 Pakuti adzalamuliraangeloake za iwe,

akusunge m’njira zako zonse.

12 Adzakunyamula pa manja ao,

ungagunde phazi lako pamwala.

13 Udzaponda mkango ndi mphiri;

udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.

14 Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;

ndidzamkweza m’mwamba, popeza adziwa dzina langa.

15 Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha;

kunsautso ndidzakhala naye pamodzi;

ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

16 Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri,

ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/91-f6c6a65bedf2646c3fe08f32811e404e.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 92

Anthu onse ayamike Mulungu chifukwa cha ntchito zake, chilungamo chake, ndi chifundo chake

Salimo, Nyimbo ya pa Sabata.

1 Nkokoma kuyamika Yehova,

ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu.

2 Kuonetsera chifundo chanu mamawa,

ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.

3 Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa;

pazeze ndi kulira kwake.

4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu,

ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.

5 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova,

zolingalira zanu nzozama ndithu.

6 Munthu wopulukira sachidziwa;

ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;

7 chakuti pophuka oipa ngati msipu,

ndi popindula ochita zopanda pake;

chitero kuti adzaonongeke kosatha.

8 Koma Inu, Yehova, muli m’mwamba kunthawi yonse.

9 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,

pakuti, taonani, adani anu adzatayika;

ochita zopanda pake onse adzamwazika.

10 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;

anandidzoza mafuta atsopano.

11 Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira,

m’makutu mwanga ndamva chokhumba ine

pa iwo akuchita zoipa akundiukira.

12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;

adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

13 Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova,

adzaphuka m’mabwalo a Mulungu wathu.

14 Atakalamba adzapatsanso zipatso;

adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,

15 kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;

Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/92-932cff6c0bcd754f622cfa753d8f06fc.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 93

Ufumu wa Mulungu ndiwo wa ulemerero, mphamvu, ndi chiyero

1 Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu;

wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m’chuuno;

dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.

2 Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;

Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe.

3 Mitsinje ikweza, Yehova,

mitsinje ikweza mkokomo wao;

mitsinje ikweza mafunde ao.

4 Yehova Wam’mwamba ndiye wamphamvu,

wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,

ndi mafunde olimba a nyanja.

5 Mboni zanu zivomerezeka ndithu;

chiyero chiyenera nyumba yanu,

Yehova, kunthawi za muyaya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/93-31e10020bca2d40d7747c9da21afd644.mp3?version_id=1068—