Categories
MASALIMO

MASALIMO 74

Malo oyera adetsedwa. Apempha Mulungu akumbuke chipangano chao

Chilangizo cha Asafu.

1 Mulungu, munatitayiranji chitayire?

Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?

2 Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale,

umene munauombola ukhale fuko la cholowa chanu;

Phiri laZiyonilimene mukhalamo.

3 Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha,

zoipa zonse adazichita mdani m’malo opatulika.

4 Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu;

aika mbendera zao zikhale zizindikiro.

5 Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.

6 Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zake zonse

ndi nkhwangwa ndi nyundo.

7 Anatentha malo anu opatulika;

anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.

8 Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi;

anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m’dzikomo.

9 Sitiziona zizindikiro zathu;

palibensomneneri;

ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.

10 Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu?

Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?

11 Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu?

Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu.

12 Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale,

wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi.

13 Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu;

mudaswa mitu ya zoopsa za m’madzi.

14 Mudaphwanya mitu yaLeviyatani;

mudampereka akhale chakudya cha zilombo za m’chipululu.

15 Mudagawa kasupe ndi mtsinje;

mudaphwetsa mitsinje yaikulu.

16 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu,

munakonza kuunika ndi dzuwa.

17 Munaika malekezero onse a dziko lapansi;

munalenga dzinja ndi malimwe.

18 Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza,

ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

19 Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo;

musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.

20 Samalirani chipanganocho;

pakuti malo a mdima a m’dziko adzala ndi zokhalamo chiwawa.

21 Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi;

wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu.

22 Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha;

kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.

23 Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu;

kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/74-f6b2ca6dd029419aab82d250c90fd897.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 75

Mulungu woweruza asiyanitsa pakati pa odzikuza ndi olungama

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Altasyeti. Salimo la Asafu. Nyimbo.

1 Tikuyamikani Inu, Mulungu;

tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi;

afotokozera zodabwitsa zanu.

2 Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika.

3 Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;

ndinachirika mizati yake.

4 Ndinati kwa odzitamandira,

musamachita zodzitamandira;

ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;

5 musamakwezetsa nyanga yanu;

musamalankhula ndi khosi louma.

6 Pakuti kukuzaku sikuchokera kum’mawa,

kapena kumadzulo, kapena kuchipululu.

7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza;

achepsa wina, nakuza wina.

8 Pakuti m’dzanja la Yehova muli chikho;

ndi vinyo wake achita thovu;

chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako.

Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa

nadzagugudiza nsenga zake.

9 Koma ine ndidzalalikira kosalekeza,

ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.

10 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa;

koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/75-52b7b03dd59f18d15cd25d480b6410d9.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 76

Ulemerero ndi mphamvu ya Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Asafu. Nyimbo.

1 Mulungu adziwika mwa Yuda,

dzina lake limveka mwa Israele.

2 Msasa wake unali mu Salemu,

ndipo pokhala Iye muZiyoni.

3 Pomwepo anathyola mivi ya pauta;

chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.

4 Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka

wakuposa mapiri muli achifwamba.

5 Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao;

amuna onse amphamvu asowa manja ao.

6 Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,

galeta ndi kavalo yemwe anagwa m’tulo.

7 Inu ndinu woopsa;

ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?

8 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba;

dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,

9 pakuuka Mulungu kuti aweruze,

kuti apulumutse ofatsa onse a padziko lapansi.

10 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani;

chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.

11 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;

onse akumzinga abwere nacho chopereka

cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.

12 Iye adzadula mzimu wa akulu;

akhala woopsa kwa mafumu a padziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/76-6d49cd8d3a95a8d09509157e28fcb6e7.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 77

Achita nkhawa pokumbuka zochita Mulungu, koma alimbika mtima pokumbuka zina adazichita Iye

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Yedutuni. Salimo la Asafu.

1 Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga;

kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu.

2 Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye.

Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka;

mtima wanga unakana kutonthozedwa.

3 Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika;

ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.

4 Mundikhalitsa maso;

ndigwidwa mtima wosanena kanthu.

5 Ndinaganizira masiku akale,

zaka zakalekale.

6 Ndikumbukira nyimbo yanga usiku;

ndilingalira mumtima mwanga;

mzimu wanga unasanthula.

7 Kodi Ambuye adzataya nthawi yonse?

Osabwerezanso kukondwera nafe.

8 Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi?

Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?

9 Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo?

Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?

10 Ndipo ndinati, Chindiwawa ichi;

koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam’mwambamwamba.

11 Ndidzakumbukira zimene adazichita Yehova;

inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale.

12 Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse,

ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.

13 Mulungu, m’malo opatulika muli njira yanu;

Mulungu wamkulu ndani monga Mulungu?

14 Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa;

munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.

15 Munaombola anthu anu ndi mkono wanu,

ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.

16 Madziwo anakuonani Mulungu;

anakuonani madziwo; anachita mantha,

zozama zomwe zinanjenjemera.

17 Makongwa anatsanula madzi;

thambo lidamvetsa liu lake;

mivi yanu yomwe inatulukira.

18 Liu la bingu lanu linatengezanatengezana;

mphezi zinaunikira ponse pali anthu;

dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.

19 Njira yanu inali m’nyanja,

koyenda Inu nkumadzi aakulu,

ndipo mapazi anu sanadziwike.

20 Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa,

ndi dzanja la Mose ndi Aroni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/77-d06cca7a2d01417e2d34d1e031c85145.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 78

Chikondi ndi chipiriro cha Mulungu cha pa Aisraele osakhulupirika

Chilangizo cha Asafu.

1 Tamverani, anthu anga, chilamulo changa;

tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.

2 Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira;

ndidzatchula zinsinsi zoyambira kale.

3 Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa,

ndipo makolo athu anatifotokozera.

4 Sitidzazibisira ana ao,

koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova,

ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.

5 Anakhazika mboni mwa Yakobo,

naika chilamulo mwa Israele,

ndizo analamulira atate athu,

akazidziwitse ana ao;

6 kuti mbadwo ukudzawo udziwe,

ndiwo ana amene akadzabadwa;

amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao.

7 Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu,

osaiwala zochita Mulungu,

koma kusunga malamulo ake ndiko.

8 Ndi kuti asange makolo ao,

ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu;

mbadwo wosakonza mtima wao,

ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu.

9 Ana a Efuremu okhala nazo zida, oponya nao mauta,

anabwerera m’mbuyo tsiku la nkhondo.

10 Sanasungachipanganocha Mulungu,

nakana kuyenda m’chilamulo chake.

11 Ndipo anaiwala zochita Iye,

ndi zodabwitsa zake zimene anawaonetsa.

12 Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao,

m’dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.

13 Anagawa nyanja nawapititsapo;

naimitsa madziwo ngati khoma.

14 Ndipo msana anawatsogolera ndi mtambo

ndi usiku wonse ndi kuunika kwa moto.

15 Anang’alula thanthwe m’chipululu,

ndipo anawamwetsa kochuluka monga m’madzi ozama.

16 Anatulukitsa mitsinje m’thanthwe,

inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje.

17 Koma anaonjeza kumchimwira Iye,

kupikisana ndi Wam’mwambamwamba m’chipululu.

18 Ndipo anayesa Mulungu mumtima mwao

ndi kupempha chakudya monga mwa kulakalaka kwao.

19 Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu;

anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m’chipululu?

20 Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako

ndi mitsinje inasefuka;

kodi adzakhozanso kupatsa mkate?

Kodi adzafunira anthu ake nyama?

21 Chifukwa chake Yehova anamva, nakwiya;

ndipo anayatsa moto pa Yakobo,

ndiponso mkwiyo unakwera pa Israele.

22 Popeza sanakhulupirire Mulungu,

osatama chipulumutso chake.

23 Koma analamulira mitambo ili m’mwamba,

natsegula m’makomo a kumwamba.

24 Ndipo anawavumbitsiramana, adye,

nawapatsa tirigu wa kumwamba.

25 Yense anadya mkate wa angelo,

anawatumizira chakudya chofikira.

26 Anaombetsa m’mwamba mphepo ya kum’mawa,

natsogoza mwera ndi mphamvu yake.

27 Ndipo anawavumbitsira nyama ngati fumbi,

ndi mbalame zouluka ngati mchenga wa kunyanja.

28 Ndipo anazigwetsa pakati pa misasa yao,

pozungulira pokhala iwo.

29 Potero anadya nakhuta kwambiri;

ndipo anawapatsa chokhumba iwo.

30 Asanathe nacho chokhumba chao,

chakudya chao chili m’kamwa mwao,

31 pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira,

ndipo anapha mwa onenepa ao,

nagwetsa osankhika a Israele.

32 Chingakhale ichi chonse anachimwanso,

osavomereza zodabwitsa zake.

33 Potero anathera masiku ao ndi zopanda pake,

ndi zaka zao mwa mantha.

34 Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye;

nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.

35 Ndipo anakumbukira kuti Mulungu ndiye thanthwe lao,

ndi Mulungu Wam’mwambamwamba Mombolo wao.

36 Koma anamsyasyalika pakamwa pao,

namnamiza ndi lilime lao.

37 Popeza mtima wao sunakonzekere Iye,

ndipo sanakhazikike m’chipangano chake.

38 Koma Iye pokhala ngwa chifundo,

anakhululukira choipa, osawaononga;

nabweza mkwiyo wake kawirikawiri,

sanautse ukali wake wonse.

39 Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu;

mphepo yopita yosabweranso.

40 Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako,

nammvetsa chisoni m’chipululu.

41 Pakuti anabwerera m’mbuyo, nayesa Mulungu,

nachepsa Woyerayo wa Israele.

42 Sanakumbukire dzanja lake,

tsikuli anawaombola kwa msautsi.

43 Amene anaika zizindikiro zake mu Ejipito,

ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani.

44 Nasanduliza nyanja yao mwazi,

ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.

45 Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha;

ndi achule akuwaononga.

46 Ndipo anapatsa mphuchi dzinthu dzao,

ndi dzombe ntchito yao.

47 Anapha mphesa zao ndi matalala,

ndi mikuyu yao ndi chisanu.

48 Naperekanso zoweta zao kwa matalala,

ndi ng’ombe zao kwa mphezi.

49 Anawatumizira mkwiyo wake wotentha,

kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso,

ndizo gulu la amithenga ochita zoipa.

50 Analambulira mkwiyo wake njira;

sanalekerere moyo wao usafe,

koma anapereka moyo wao kumliri.

51 Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito,

ndiwo oyamba a mphamvu yao m’mahema a Hamu.

52 Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa,

nawatsogoza ngati gulu la zoweta m’chipululu.

53 Ndipo anawatsogolera mokhulupirika,

kotero kuti sanaope;

koma nyanja inamiza adani ao.

54 Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera,

kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula.

55 Ndipo anapirikitsaamitundupamaso pao,

nawagawira cholowa chao, ndi muyeso,

nakhalitsa mafuko a Israele m’mahema mwao.

56 Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam’mwambamwamba,

osasunga mboni zake;

57 koma anabwerera m’mbuyo,

nachita zosakhulupirika monga makolo ao,

anapatuka ngati uta wolenda.

58 Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao,

namchititsa nsanje ndi mafano osema.

59 Pakumva ichi Mulungu, anakwiya,

nanyozatu Israele;

60 ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo,

chihemacho adachimanga mwa anthu;

61 napereka mphamvu yake mu ukapolo,

ndi ulemerero wake m’dzanja la msautsi.

62 Naperekanso anthu ake kwa lupanga;

nakwiya nacho cholowa chake.

63 Moto unapsereza anyamata ao;

ndi anamwali ao sanalemekezeke.

64 Ansembe ao anagwa ndi lupanga;

ndipo amasiye ao sanachite maliro.

65 Pamenepo Ambuye anauka ngati wam’tulo;

ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo.

66 Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo;

nawapereka akhale otonzeka kosatha.

67 Tero anakana hema wa Yosefe;

ndipo sanasankhe fuko la Efuremu;

68 koma anasankha fuko la Yuda,

Phiri laZiyonilimene analikonda.

69 Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri,

monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.

70 Ndipo anasankha Davide mtumiki wake,

namtenga kumakola a nkhosa.

71 Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa,

awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.

72 Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro;

nawatsogolera ndi luso la manja ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/78-e2156f04bd933a25a0454c3bfa7e9aca.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 79

Yerusalemu apasuka, apempha Mulungu awathandize

Salimo la Asafu.

1 Mulungu, akunja alowa m’cholowa chanu;

anaipsa Kachisi wanu woyera;

anachititsaYerusalemubwinja.

2 Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale

chakudya cha mbalame za mlengalenga,

nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zilombo za m’dziko.

3 Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;

ndipo panalibe wakuwaika.

4 Takhala chotonza cha anansi athu,

ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.

5 Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?

Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?

6 Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,

ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.

7 Pakuti anathera Yakobo,

napasula pokhalira iye.

8 Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu;

nsoni zokoma zanu zitipeze msanga,

pakuti tafooka kwambiri.

9 Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu,

chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;

ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu,

chifukwa cha dzina lanu.

10 Anenerenjiamitundu, Ali kuti Mulungu wao?

Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa

kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.

11 Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu;

monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.

12 Ndipo anansi athu amene anatonza Inu

muwabwezere chotonza chao,

kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.

13 Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu

tidzakuyamikani kosatha;

tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/79-e2d05ecb3a115be44ba2d6c2838e09ec.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 80

Apempha Mulungu alanditse anthu ake m’chisautso chao

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Syosyanimu; lochita mboni. Salimo la Asafu.

1 Mbusa wa Israele, tcherani khutu;

inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa;

inu wokhala paakerubi, walitsani.

2 Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase,

ndipo mutidzere kutipulumutsa.

3 Mutibweze, Mulungu;

nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

4 Yehova, Mulungu wa makamu,

mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?

5 Munawadyetsa mkate wa misozi,

ndipo munawamwetsa misozi yambiri.

6 Mutiika kuti atilimbirane anzathu;

ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha.

7 Mulungu wa makamu, mutibweze;

nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

8 Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito,

munapirikitsaamitundundi kuuoka uwu.

9 Mudasoseratu pookapo,

idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.

10 Mthunzi wake unaphimba mapiri,

ndi nthambi zake zikunga mikungudza ya Mulungu.

11 Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja,

ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje.

12 Munapasuliranji maphambo ake,

kotero kuti onse akupita m’njira atcherako?

13 Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba,

ndi nyama za kuchidikha ziudya.

14 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu;

suzumirani muli m’mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

15 ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka,

ndi mphanda munadzilimbikitsira.

16 Unapserera ndi moto, unadulidwa;

aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa padzanja lamanja lanu;

pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

18 Potero sitidzabwerera m’mbuyo kukusiyani;

titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.

19 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu;

nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/80-f7f6ebf5a67b2478f0a50131ab76fbd1.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 81

Mulungu atonza Aisraele pa kusamvera kwao

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Gititi. Salimo la Asafu.

1 Imbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu;

fuulirani kwa Mulungu wa Yakobo.

2 Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka,

zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa.

3 Ombani lipenga, pokhala mwezi,

utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.

4 Pakuti ichi ndi cholemba cha kwa Israele,

chiweruzo cha Mulungu wa Yakobo.

5 Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe,

pakutuluka iye kudziko la Ejipito.

Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.

6 Ndinamchotsera katundu paphewa pake,

manja ake anamasuka ku chotengera.

7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;

ndinakuvomereza mobisalika m’bingu;

ndinakuyesa kumadzi a Meriba.

8 Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni;

Israele, ukadzandimvera!

9 Kwanu kusakhale mulungu wofuma kwina;

nusagwadire mulungu wachilendo.

10 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza

kukuchotsa kudziko la Ejipito;

yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.

11 Koma anthu anga sanamvere mau anga;

ndipo Israele sanandivomere.

12 Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,

ayende monga mwa uphungu waowao.

13 Ha! Akadandimvera anthu anga,

akadayenda m’njira zanga Israele!

14 Ndikadagonjetsa adani ao msanga,

ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

15 Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga,

koma nyengo yao ikadakhala yosatha.

16 Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa,

ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m’thanthwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/81-7a6d9c36607a2edf7841f2afaaa781b5.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 82

Oweruza aweruza bwino

Salimo la Asafu.

1 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,

aweruza pakati pa milungu.

2 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,

ndi kusamalira nkhope ya oipa?

3 Weruzani osauka ndi amasiye;

weruzani molungama ozunzika ndi osowa.

4 Pulumutsani osauka ndi aumphawi;

alanditseni m’dzanja la oipa.

5 Sadziwa, ndipo sazindikira;

amayendayenda mumdima;

maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

6 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,

ndi ana a Wam’mwambamwamba nonsenu.

7 Komatu mudzafa monga anthu,

ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.

8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;

pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/82-51f5963a0b1ec07d9942f2c0062d9534.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 83

Amitundu apangana kuononga Aisraele. Apempha Mulungu awalanditse

Nyimbo. Salimo la Asafu.

1 Mulungu musakhale chete;

musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.

2 Pakuti taonani, adani anu apokosera,

ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.

3 Apangana mochenjerera pa anthu anu,

nakhalira upo pa obisika anu.

4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;

ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.

5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;

anachitachipanganocha pa Inu.

6 Mahema a Edomu ndi a Aismaele;

Mowabu ndi Ahagiri;

7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleke;

Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.

8 Asiriya anaphatikana nao;

anakhala dzanja la ana a Loti.

9 Muwachitire monga munachitira Midiyani;

ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,

10 amene anaonongeka ku Endori;

anakhala ngati ndowe ya kumunda.

11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;

mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,

12 amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.

13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;

ngati ziputu zomka ndi mphepo.

14 Monga moto upsereza nkhalango,

ndi monga lawi liyatsa mapiri.

15 Momwemo muwatsate ndi namondwe,

nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.

16 Achititseni manyazi pankhope pao;

kuti afune dzina lanu, Yehova.

17 Achite manyazi, naopsedwe kosatha;

ndipo asokonezeke, naonongeke.

18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,

ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/83-d2cdb0eba6aa3310d96e8863b2c3cdf6.mp3?version_id=1068—