Categories
MASALIMO

MASALIMO 64

Davide apempha Mulungu amtchinjirize pa omlalira

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Imvani Mulungu, mau anga, m’kudandaula kwanga;

sungani moyo wanga angandiopse mdani.

2 Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa;

pa phokoso la ochita zopanda pake.

3 Amene anola lilime lao ngati lupanga,

napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;

4 kuponyera wangwiro mobisika:

Amponyera modzidzimutsa, osaopa.

5 Alimbikitsana m’chinthu choipa;

apangana za kutchera misampha mobisika;

akuti, Adzaiona ndani?

6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha;

chingakhale cha m’kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.

7 Koma Mulungu adzawaponyera muvi;

adzalaswa modzidzimutsa.

8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;

onse akuwaona adzawathawa.

9 Ndipo anthu onse adzachita mantha;

nadzabukitsa chochita Mulungu,

nadzasamalira ntchito yake.

10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova,

nadzakhulupirira Iye;

ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/64-f8cb3fc909cb65eb3e048846840dd693.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 65

Davide alemekeza Mulungu pa madalitso ochuluka

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide. Nyimbo.

1 MuZiyoniakulemekezani Inu mwachete, Mulungu,

adzakuchitirani Inu chowindachi.

2 Wakumva pemphero Inu,

zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.

3 Mphulupulu zinandipambana;

koma mudzafafaniza zolakwa zathu.

4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,

akhale m’mabwalo anu.

Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu,

za m’malo oyera a Kachisi wanu.

5 Mudzatiyankha nazo zoopsa m’chilungamo,

Mulungu wa chipulumutso chathu;

ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi,

ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.

6 Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;

pozingidwa nacho chilimbiko.

7 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja,

kukuntha kwa mafunde ake,

ndi phokoso la mitundu ya anthu.

8 Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha

chifukwa cha zizindikiro zanu;

mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.

9 Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira,

mulilemeretsa kwambiri;

mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi,

muwameretsera tirigu m’mene munakonzera nthaka.

10 Mukhutitsa nthaka yake yolima;

mufafaniza nthumbira zake;

muiolowetsa ndi mvumbi;

mudalitsa mmera wake.

11 Muveka chakachi ndi ukoma wanu;

ndipo mabande anu akukha zakucha.

12 Akukha pa mabusa a m’chipululu;

ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe.

13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;

ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;

zifuula mokondwera, inde ziimbira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/65-b7355099f446294b6dd7e354ffe4751b.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 66

Achenjeza onse alemekeze Mulungu pa ntchito zake zodabwitsa

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Nyimbo, Salimo.

1 Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.

2 Imbirani ulemerero wa dzina lake;

pomlemekeza mumchitire ulemerero.

3 Nenani kwa Mulungu, Ha,

ntchito zanu nzoopsa nanga!

Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.

4 Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,

ndipo lidzakuimbirani;

ndzaimbira dzina lanu.

5 Idzani, muone ntchito za Mulungu;

zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.

6 Anasanduliza nyanja ikhale mtunda.

Anaoloka mtsinje choponda pansi,

apo tinakondwera mwa Iye.

7 Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha;

maso ake ayang’aniraamitundu;

opikisana ndi Iye asadzikuze.

8 Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,

ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake.

9 Iye amene asunga moyo wathu tingafe,

osalola phazi lathu literereke.

10 Pakuti munatiyesera, Mulungu,

munatiyenga monga ayengasiliva.

11 Munapita nafe kuukonde;

munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.

12 Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;

tinapyola moto ndi madzi;

koma munatifikitsa potitsitsimutsa.

13 Ndidzalowa m’nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,

ndidzakuchitirani zowinda zanga,

14 zimene inazitchula milomo yanga,

ndinazinena pakamwa panga posautsika ine.

15 Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona,

pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa;

ndidzakonza ng’ombe pamodzi ndi mbuzi.

16 Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,

ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.

17 Ndinamfuulira Iye pakamwa panga,

ndipo ndinamkuza ndi lilime langa.

18 Ndikadasekera zopanda pake m’mtima mwanga,

Ambuye sakadamvera.

19 Koma Mulungu anamvadi;

anamvera mau a pemphero langa.

20 Wolemekezeka Mulungu,

amene sanandipatutsire ine pemphero langa,

kapena chifundo chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/66-cd2c9e7202df993c36a1484f8905c376.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 67

Amitundu alemekeze Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Neginoto. Salimo. Nyimbo.

1 Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa,

atiwalitsire nkhope yake;

2 kuti njira yanu idziwike padziko lapansi,

chipulumutso chanu mwaamitunduonse.

3 Anthu akuyamikeni, Mulungu;

anthu onse akuyamikeni.

4 Anthu akondwere, nafuule mokondwera;

pakuti mudzaweruza anthu molunjika,

ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi.

5 Anthu akuyamikeni, Mulungu;

anthu onse akuyamikeni.

6 Dziko lapansi lapereka zipatso zake,

Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.

7 Mulungu adzatidalitsa;

ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/67-029d8e9e029b86de068d98b51bdff7f7.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 68

Mau akuyamikira Mulungu wa chipulumutso chonse

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo.

1 Auke Mulungu, abalalike adani ake;

iwonso akumuda athawe pamaso pake.

2 Muwachotse monga utsi uchotseka;

monga phula lisungunuka pamoto,

aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.

3 Koma olungama akondwere;

atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu;

ndipo asekere nacho chikondwerero.

4 Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake;

undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha;

dzina lake ndiye Yehova;

ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.

5 Mulungu, mokhala mwake moyera,

ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

6 Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha;

atulutsa am’ndende alemerere;

koma opikisana naye akhala m’dziko lopanda madzi.

7 Pakutuluka paja, Inu Mulungu, ndi kutsogolera anthu anu,

pakuyenda paja Inu m’chipululu.

8 Dziko lapansi linagwedezeka,

inde thambo linakha pamaso pa Mulungu;

Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu,

Mulungu wa Israele.

9 Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula,

munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.

10 Gulu lanu linakhala m’dziko muja.

Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.

11 Ambuye anapatsa mau,

akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.

12 Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa,

ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.

13 Pogona inu m’makola a zoweta,

mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndisiliva,

ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.

14 Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m’dzikomo,

munayera ngati matalala mu Zalimoni.

15 Phiri la Basani ndilo phiri la Mulungu;

Phiri la Basani ndilo phiri la mitumitu.

16 Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu,

ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko?

Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.

17 Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri,

inde zikwi zowirikizawirikiza,

Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m’malo opatulika.

18 Munakwera kunka kumwamba,

munapita nao undende kuuyesa ndende;

munalandira zaufulu mwa anthu,

ngakhale mwa opikisana nanu,

kuti Yehova Mulungu akakhale nao.

19 Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu,

ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.

20 Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso;

ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.

21 Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake,

pakati pamutu pa iye woyendabe m’kutsutsika kwake.

22 Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basani,

ndidzawatenganso kozama kwa nyanja,

23 kuti uviike phazi lako m’mwazi,

kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.

24 Anapenya mayendedwe anu, Mulungu,

mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m’malo oyera.

25 Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m’mbuyo,

pakatipo anamwali oimba mangaka.

26 Lemekezani Mulungu m’misonkhano,

ndiye Yehova, inu a gwero la Israele.

27 Apo pali Benjamini wamng’ono, wakuwachita ufumu,

akulu a Yuda, ndi a upo wao,

akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.

28 Mulungu wako analamulira mphamvu yako,

Limbitsani, Mulungu, chimene munatichitira.

29 Chifukwa cha Kachisi wanu wa muYerusalemu

mafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani.

30 Dzudzulani chilombo cha m’bango,

khamu la mphongo ndi ng’ombe za anthu,

yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva;

anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

31 Akulu adzafumira ku Ejipito;

Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.

32 Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;

imbirani Ambuye zomlemekeza.

33 Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba,

oyambira kale lomwe;

taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.

34 Vomerezani kuti mphamvu nja Mulungu;

ukulu wake uli pa Israele,

ndi mphamvu yake m’mitambo.

35 Inu Mulungu, ndinu woopsa m’malo oyera anu;

Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake

mphamvu ndi chilimbiko.

Alemekezeke Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/68-1abf2ff8650099a7f9c68dc73b8fe592.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 69

Davide adandaulira kwa Mulungu chifukwa cha zowawa azimva

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Pa Syosyanimu. Salimo la Davide.

1 Ndipulumutseni Mulungu;

pakuti madzi afikira moyo wanga.

2 Ndamira m’thope lozama, lopanda poponderapo;

ndalowa m’madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.

3 Ndalema ndi kufuula kwanga; kum’mero kwauma gwaa!

M’maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

4 Ondida kopanda chifukwa achuluka

koposa tsitsi la pamutu panga;

ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu.

Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.

5 Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;

ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.

6 Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye, Yehova wa makamu,

asachite manyazi chifukwa cha ine,

iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele,

asapepulidwe chifukwa cha ine.

7 Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu,

chimpepulo chakuta nkhope yanga.

8 Abale anga andiyesa mlendo,

ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.

9 Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya;

ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.

10 Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,

koma uku kunandikhalira chotonza.

11 Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli,

koma amandiphera mwambi.

12 Okhala pachipata akamba za ine;

ndipo oledzera andiimba.

13 Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu,

Yehova, m’nyengo yolandirika;

Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu,

mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.

14 Mundilanditse kuthope, ndisamiremo,

ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.

15 Chigumula chisandifotsere,

ndipo chakuya chisandimize;

ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.

16 Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma;

munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.

17 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;

pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.

18 Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;

ndipulumutseni chifukwa cha adani anga.

19 Mudziwa chotonza changa, ndi manyazi anga,

ndi chimpepulo changa.

Akundisautsa ali pamaso panu.

20 Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine;

ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe;

ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.

21 Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa;

nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.

22 Gome lao likhale msampha pamaso pao;

pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe.

23 M’maso mwao mude, kuti asapenye;

ndipo munjenjemeretse m’chuuno mwao kosalekeza.

24 Muwatsanulire mkwiyo wanu,

ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.

25 Pokhala pao pakhale bwinja;

m’mahema mwao musakhale munthu.

26 Pakuti alondola amene Inu munampanda;

ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.

27 Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao;

ndipo asafikire chilungamo chanu.

28 Afafanizidwe m’buku lamoyo,

ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

29 Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa;

chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje.

30 Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira,

ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.

31 Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng’ombe,

inde mphongo za nyanga ndi ziboda.

32 Ofatsa anachiona, nakondwera,

ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.

33 Pakuti Yehova amvera aumphawi,

ndipo sapeputsa am’ndende ake.

34 Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze,

nyanja ndi zonse zoyenda m’mwemo.

35 Pakuti Mulungu adzapulumutsaZiyoni,

nadzamanga mizinda ya Yuda;

ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao.

36 Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira;

ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m’mwemo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/69-f68152a569022f718108a6f7b543097b.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 70

Davide apempha Mulungu amlanditse msanga

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, la chikumbutso.

1 Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu!

Fulumirani kundithandiza, Yehova.

2 Achite manyazi, nadodome

amene afuna moyo wanga.

Abwezedwe m’mbuyo, napepulidwe

amene akonda kundichitira choipa.

3 Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao

amene akuti, Hede, hede.

4 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;

nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu,

abuke Mulungu.

5 Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi;

mundifulumirire, Mulungu.

Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga;

musachedwe, Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/70-251047a461c8e820f60f8ead5989c355.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 71

Nkhalamba idzaponya kwa Mulungu amene anamkhulupirira kuyambira ubwana wake

1 Ndikhulupirira Inu, Yehova.

Ndisachite manyazi nthawi zonse.

2 Ndikwatuleni m’chilungamo chanu, ndi kundilanditsa,

nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.

3 Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;

mwalamulira kundipulumutsa;

popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.

4 Ndilanditseni, Mulungu wanga, m’dzanja la woipa,

m’dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.

5 Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova;

mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

6 Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe,

kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu;

ndidzakulemekezani kosalekeza.

7 Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri;

koma Inu ndinu pothawira panga polimba.

8 M’kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu,

ndi ulemu wanu tsiku lonse.

9 Musanditaye mu ukalamba wanga;

musandisiye, pakutha mphamvu yanga.

10 Pakuti adani anga alankhula za ine;

ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,

11 ndi kuti, Wamsiya Mulungu.

Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa.

12 Musandikhalire kutali, Mulungu;

fulumirani kundithandiza, Mulungu.

13 Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe;

chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.

14 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,

ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.

15 Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu,

ndi chipulumutso chanu tsiku lonse;

pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.

16 Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova;

ndidzatchula chilungamo chanu, inde chanu chokha.

17 Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga;

ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.

18 Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu;

kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu,

mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.

19 Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo;

Inu amene munachita zazikulu,

akunga Inu ndani, Mulungu?

20 Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa,

mudzatipatsanso moyo,

ndi kutitenganso munsi mwa dziko.

21 Mundionjezere ukulu wanga,

ndipo munditembenukire kundisangalatsa.

22 Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa,

kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga;

ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze,

ndinu Woyerayo wa Israele.

23 Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo;

inde, moyo wanga umene munaombola.

24 Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse,

pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/71-0771d2c3ef063cd4dd268f590b828ffa.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 72

Za ufumu wa Mfumu yokoma

Salimo la Solomoni.

1 Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,

ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.

2 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m’chilungamo,

ndi ozunzika anu ndi m’chiweruzo.

3 Mapiri adzatengera anthu mtendere,

timapiri tomwe, m’chilungamo.

4 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,

adzapulumutsa ana aumphawi,

nadzaphwanya wosautsa.

5 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,

kufikira mibadwomibadwo.

6 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga,

monga mvula yothirira dziko.

7 Masiku ake wolungama adzakhazikika;

ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.

8 Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja,

ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.

9 Okhala m’chipululu adzagwadira pamaso pake;

ndi adani ake adzaluma nthaka.

10 Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka;

mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.

11 Inde mafumu onse adzamgwadira iye,

amitunduonse adzamtumikira.

12 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo;

ndi wozunzika amene alibe mthandizi.

13 Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi,

nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.

14 Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa;

ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.

15 Ndipo iye adzakhala ndi moyo;

ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba;

nadzampempherera kosalekeza;

adzamlemekeza tsiku lonse.

16 M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka

pamwamba pa mapiri;

zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni,

ndipo iwo a m’mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.

17 Dzina lake lidzakhala kosatha,

momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu.

Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;

amitundu onse adzamutcha wodala.

18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele,

amene achita zodabwitsa yekhayo.

19 Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha;

ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake.

Amen, ndi Amen.

20 Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/72-afe1e9589ee32599b3e095cbb851cd4d.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 73

Kupindula kwa oipa kumakayikitsa pa chilungamo cha Mulungu, koma chitsiriziro chao chitivomerezetsa chilungamocho

Salimo la Asafu.

1 Indedi Mulungu achitira Israele zabwino,

iwo a mtima wa mbee.

2 Koma ine, ndikadagwa;

mapazi anga akadaterereka.

3 Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira,

pakuona mtendere wa oipa.

4 Pakuti palibe zomangira pakufa iwo,

ndi mphamvu yao njolimba.

5 Savutika monga anthu ena;

sasautsika monga anthu ena.

6 Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao;

achivala chiwawa ngati malaya.

7 Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao,

malingaliro a mitima yao asefukira.

8 Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa,

alankhula modzitama.

9 Pakamwa pao anena zam’mwamba,

ndipo lilime lao liyendayenda m’dziko lapansi.

10 Chifukwa chake anthu ake amabwera kudza kuno,

ndipo chikho chodzala ndi madzi achigugudiza.

11 Namati, Akachidziwa bwanji Mulungu?

Kodi Wam’mwambamwamba ali nayo nzeru?

12 Tapenyani, oipa ndi awa;

ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao.

13 Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe,

ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa.

14 Popeza andisautsa tsiku lonse,

nandilanga mamawa monse,

15 ndikadati, Ndidzafotokozera chotere,

taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.

16 Pamene ndinayesa kudziwitsa ichi,

ndinavutika nacho;

17 mpaka ndinalowa m’zoyera za Mulungu,

ndi kulingalira chitsiriziro chao.

18 Indedi muwaika poterera,

muwagwetsa kuti muwaononge.

19 Ha? M’kamphindi ayesedwa bwinja;

athedwa konse ndi zoopsa.

20 Monga anthu atauka, apepula loto;

momwemo, Inu Ambuye, pakuuka

mudzapeputsa chithunzithunzi chao.

21 Pakuti mtima wanga udawawa,

ndipo ndinalaswa mu impso zanga;

22 ndinali wam’thengo, wosadziwa kanthu;

ndinali ngati nyama pamaso panu.

23 Koma ndikhala ndi Inu chikhalire,

mwandigwira dzanja langa la manja.

24 Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu,

ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.

25 Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu?

Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.

26 Likatha thupi langa ndi mtima wanga,

Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga,

ndi cholandira changa chosatha.

27 Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka;

muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.

28 Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.

Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine,

kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/73-83b70a1219340538ba838677699ab073.mp3?version_id=1068—