Categories
MASALIMO

MASALIMO 54

Davide apempha Mulungu amlanditse

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Chilangizo cha Davide. Muja Azifi anamuka nauza Saulo, kuti, Kodi Davide sabisala kwathu nanga?

1 Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,

ndipo mundiweruze ndi mphamvu yanu.

2 Imvani pemphero langa, Mulungu;

tcherani khutu mau a pakamwa panga.

3 Pakuti alendo andiukira,

ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;

sadziikira Mulungu pamaso pao.

4 Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga,

Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.

5 Adzabwezera choipa adani anga,

aduleni m’choonadi chanu.

6 Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu,

ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.

7 Pakuti anandilanditsa m’nsautso yonse;

ndipo ndapenya ndi diso langa icho ndakhumbira pa adani anga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/54-7e0db2663d17ad9db483aea5e9664885.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 55

Davide adandaula pa kuipa kwa adani, adziponya kwa Mulungu, nalangiza ena azitero iwo omwe

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Chilangizo cha Davide.

1 Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu;

ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.

2 Mverani, ndipo mundiyankhe,

ndiliralira m’kudandaula kwanga ndi kubuula;

3 chifukwa cha mau a mdani,

chifukwa cha kundipsinja woipa;

pakuti andisenza zopanda pake,

ndipo adana nane mumkwiyo.

4 Mtima wanga uwawa m’kati mwanga;

ndipo zoopsa za imfa zandigwera.

5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,

ndipo zoopsetsa zandikuta.

6 Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa!

Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.

7 Onani, ndikadathawira kutali,

ndikadagona m’chipululu.

8 Ndikadafulumira ndipulumuke

kumphepo yolimba ndi namondwe.

9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao,

pakuti ndaona chiwawa ndi ndeu m’mzindamo.

10 Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku;

ndipo m’kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta.

11 M’kati mwake muli kusakaza,

chiwawa ndi chinyengo sizichoka m’makwalala ake.

12 Pakuti si mdani amene ananditonzayo;

pakadatero ndikadachilola,

amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;

pakadatero ndikadambisalira:

13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,

tsamwali wanga, wodziwana nane.

14 Tinapangirana upo wokoma,

tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu.

15 Imfa iwagwere modzidzimutsa,

atsikire kumanda ali amoyo,

pakuti m’mokhala mwao muli zoipa pakati pao.

16 Koma ine ndidzafuulira kwa Mulungu;

ndipo Yehova adzandipulumutsa.

17 Madzulo, m’mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,

ndipo adzamva mau anga.

18 Anaombola moyo wanga kunkhondo,

ndikhale mumtendere,

pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa,

ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe.

Popeza iwowa sasinthika konse,

ndipo saopa Mulungu.

20 Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye,

anaipsa pangano lake.

21 Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka,

koma mumtima mwake munali nkhondo,

mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga,

koma anali malupanga osololasolola.

22 Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza,

nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

23 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko.

Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu;

koma ine ndidzakhulupirira Inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/55-f6f43717a2860f3b667923d0cea61273.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 56

Davide apempha Mulungu amlanditse; ayamika atamlanditsa

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Yonat-Elem-Rekokimu. Mikitamu wa Davide; muja Afilisti anamgwira mu Gati.

1 Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza.

Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.

2 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse,

pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.

3 Tsiku lakuopa ine,

ndidzakhulupirira Inu.

4 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake,

ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;

anthu adzandichitanji?

5 Tsiku lonse atenderuza mau anga,

zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.

6 Amemezana, alalira,

atchereza mapazi anga,

popeza alindira moyo wanga.

7 Kodi adzapulumuka ndi zopanda pake?

Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.

8 Muwerenga kuthawathawa kwanga,

sungani misozi yanga m’nsupa yanu;

kodi siikhala m’buku mwanu?

9 Pamenepo adani anga adzabwerera m’mbuyo tsiku lakuitana ine.

Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.

10 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake,

mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.

11 Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;

munthu adzandichitanji?

12 Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine,

ndidzakuchitirani zoyamika.

13 Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa,

simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?

Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu

m’kuunika kwa amoyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/56-87c25ca541a0a6dc7b071d0a07c0ab37.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 57

Davide apempha Mulungu amtchinjirize, namlemekezapo

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Altasheti. Mikitamu wa Davide; muja anathawa Saulo, ali m’phanga.

1 Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo;

pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu,

ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu,

kufikira zosakazazo zidzapita.

2 Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam’mwambamwamba;

ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.

3 Adzanditumizira m’mwamba, nadzandipulumutsa

ponditonza wofuna kundimeza;

Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.

4 Moyo wanga uli pakati pa mikango;

ndigona pakati pa oyaka moto,

ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi,

ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.

5 Mukwezeke m’mwambamwamba, Mulungu;

ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.

6 Ananditchera ukonde apo ndiyenda;

moyo wanga wawerama.

Anandikumbira mbuna patsogolo panga;

anagwa m’kati mwake iwo okha.

7 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;

ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.

8 Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze!

Ndidzauka ndekha mamawa.

9 Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye,

ndidzakuimbirani mwa mitundu.

10 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m’mwamba,

ndi choonadi chanu kufikira mitambo.

11 Kwezekani m’mwambamwamba, Mulungu;

ulemerero wanu ukhale pamwamba m’dziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/57-b8e32b44aecaea2420ecc0fbf388b73f.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 58

Davide adzudzula oipa Mulungu awalange

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Altasyeti. Mikitamu wa Davide.

1 Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama?

Muweruza ana anthu molunjika kodi?

2 Inde, mumtima muchita zosalungama;

padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m’manja mwanu.

3 Oipa achita chilendo chibadwire,

asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.

4 Ululu wao ukunga wa njoka;

akunga mphiri yogontha m’khutu, itseka m’khutu mwake.

5 Imene siimvera liu la oitana,

akuchita matsenga mochenjeratu.

6 Thyolani mano ao m’kamwa mwao, Mulungu,

zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.

7 Apitetu ngati madzi oyenda;

popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.

8 Apite ngati nkhono yosungunuka;

asaone dzuwa monga mtayo.

9 Miphika yanu isanagwire moto waminga,

adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.

10 Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango,

adzasamba mapazi ake m’mwazi wa woipa.

11 Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama.

Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/58-b824fc7f69079b8cbb5de62ba641a2a6.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 59

Davide apempha Mulungu amlanditse, nadzinenera wosalakwa

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Altasheti. Mikitamu wa Davide; muja Saulo anatuma anthu adikire nyumba yake, kuti amuphe.

1 Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga,

ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.

2 Mundilanditse kwa ochita zopanda pake,

ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.

3 Pakuti onani, alalira moyo wanga;

amphamvu andipangira chiwembu,

osachimwa, osalakwa ine, Yehova,

4 osawapatsa chifukwa ine, athamanga nadzikonza.

Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.

5 Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele.

Ukani kukazondaamitunduonse,

musachitire chifundo mmodzi yense

wakuchita zopanda pake monyenga.

6 Abwera madzulo, auwa ngati galu,

nazungulira mzinda.

7 Onani abwetuka pakamwa pao;

m’milomo mwao muli lupanga,

pakuti amati, Amva ndani?

8 Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;

mudzalalatira amitundu onse.

9 Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani;

pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.

10 Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira,

adzandionetsa tsoka la adani anga.

11 Musawapheretu, angaiwale anthu anga,

muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,

Ambuye, ndinu chikopa chathu.

12 Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao,

potero akodwe m’kudzitamandira kwao,

ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.

13 Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti.

Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo,

kufikira malekezero a dziko la pansi.

14 Ndipo abwere madzulo, auwe ngati galu,

nazungulire mzinda.

15 Ayendeyende ndi kufuna chakudya,

nachezere osakhuta.

16 Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu;

inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa,

pakuti Inu mwakhala msanje wanga,

ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.

17 Ndidzaimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga;

pakuti Mulungu ndiye msanje wanga,

Mulungu wa chifundo changa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/59-e89d78b60b007ab882f1c5c2366da500.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 60

Madandaulo ndi pempho la Davide

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri.

1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;

mwakwiya; tibwezereni.

2 Mwagwedeza dziko, mwaling’amba.

Konzani ming’alu yake; pakuti ligwedezeka.

3 Mwaonetsa anthu anu zowawa,

mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.

4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,

aikweze chifukwa cha choonadi.

5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,

pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.

6 Mulungu walankhula m’chiyero chake; ndidzakondwerera,

ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.

7 Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;

ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga;

Yuda ndiye wolamulira wanga.

8 Mowabu ndiye mkhate wanga;

pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga.

Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.

9 Adzandifikitsa ndani m’mzinda wa m’linga?

Adzanditsogolera ndani ku Edomu?

10 Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya?

Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.

11 Tithandizeni kunsautso;

kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.

12 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima,

ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/60-396c9720e403cdadaf93d7346d326fac.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 61

Poopsedwa Davide athamangira Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide.

1 Imvani mfuu wanga, Mulungu;

mverani pemphero langa.

2 Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu,

pomizika mtima wanga.

Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m’kutalika kwake.

3 Pakuti munakhala pothawirapo panga;

nsanja yolimba pothawa mdani ine.

4 Ndidzagoneragonerabe m’chihema mwanu;

ndidzathawira mobisalamo m’mapiko anu.

5 Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;

munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu.

6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.

Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo.

7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;

mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.

8 Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse,

kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/61-1e56a0cd41ef1a4cbbcc64d8486c8292.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 62

Posautsidwa Davide athamangira Mulungu yekha

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Yedutuni. Salimo la Davide.

1 Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha;

chipulumutso changa chifuma kwa Iye.

2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;

msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

3 Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti,

kumupha iye, nonsenu,

monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?

4 Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake;

akondwera nao mabodza;

adalitsa ndi m’kamwa mwao,

koma atemberera mumtima.

5 Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha;

pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.

6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa,

msanje wanga, sindidzagwedezeka.

7 Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga.

Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.

8 Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu,

tsanulirani mitima yanu pamaso pake.

Mulungu ndiye pothawirapo ife.

9 Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza,

pakuwayesa apepuka;

onse pamodzi apepuka koposa mpweya.

10 Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba;

chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

11 Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri,

kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu.

12 Chifundonso ndi chanu, Ambuye,

Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense

monga mwa ntchito yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/62-1668ff3568829050b8ae71291efba225.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 63

Mtima woliralira kuyanjana ndi Mulungu

Salimo la Davide; muja anakhala m’chipululu cha Yuda.

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga;

ndidzakufunani m’matanda kucha.

Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu,

thupi langa lilirira Inu,

m’dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,

monga ndinakuonani m’malo oyera.

3 Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake;

milomo yanga idzakulemekezani.

4 Potero ndidzakuyamikani m’moyo mwanga;

ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;

ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani

ndi milomo yakufuula mokondwera.

6 Pokumbukira Inu pa kama wanga,

ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7 Pakuti munakhala mthandizi wanga;

ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8 Moyo wanga uumirira Inu.

Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,

adzalowa m’munsi mwake mwa dziko.

10 Adzawapereka kumphamvu ya lupanga;

iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;

yense wakulumbirira iye adzatamandira;

pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/63-dd5022b579c322c447c9f170e2fa695e.mp3?version_id=1068—