Categories
MASALIMO

MASALIMO 44

Anthu a Mulungu akumbuke zithandizo zakale popempha chipulumutso m’tsoka lao

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora.

1 Mulungu, tidamva m’makutu mwathu, makolo athu anatisimbira,

za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.

2 Inu munapirikitsaamitundundi dzanja lanu,

koma iwowa munawaoka;

munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.

3 Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao,

ndipo mkono wao sunawapulumutse.

Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu,

ndi kuunika kwa nkhope yanu.

Popeza munakondwera nao,

4 Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu;

lamulirani chipulumutso cha Yakobo.

5 Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe,

m’dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.

6 Pakuti uta wanga,

ndipo lupanga langa silingandipulumutse.

7 Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe,

ndipo akudana nafe, mudawachititsa manyazi.

8 Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse,

ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.

9 Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa;

ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.

10 Mutibwereretsa kuthawa otisautsa,

ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.

11 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya;

ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.

12 Mugulitsa anthu anu kwachabe,

ndipo mtengo wake simupindula nao.

13 Mutisandutsa chotonza kwa anzathu,

ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.

14 Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,

ndi kuti anthu atipukusire mitu.

15 Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga,

ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.

16 Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano;

chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango.

17 Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,

ndipo sitinachite monyenga m’pangano lanu.

18 Mtima wathu sunabwerere m’mbuyo,

ndipo m’mayendedwe athu sitinapatuke m’njira yanu;

19 mungakhale munatithyola mokhala zilombo,

ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.

20 Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,

ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo;

21 Mulungu sakadasanthula ichi kodi?

Pakuti adziwa zinsinsi za mtima.

22 Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse;

tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.

23 Galamukani, mugoneranji, Ambuye?

Ukani, musatitaye chitayire.

24 Mubisiranji nkhope yanu,

ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?

25 Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi,

pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.

26 Ukani, tithandizeni,

tiomboleni mwa chifundo chanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/44-de9af6db6f1f40d0e02f99000a4b2758.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 45

Nyimbo yoimbira ukwati wa mfumu

Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Syosyanimu. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Nyimbo ya chikondi.

1 Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma.

Ndinena zopeka ine za mfumu,

lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.

2 Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu;

anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu,

chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.

3 Dzimangireni lupanga lanu m’chuuno mwanu,

wamphamvu inu,

ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.

4 Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani,

kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo;

ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.

5 Mivi yanu njakuthwa;

mitundu ya anthu igwa pansi pa inu;

iwalasa mumtima adani a mfumu.

6 Mpando wachifumu wanu,

Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya.

Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.

7 Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa,

chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu

ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.

8 Zovala zanu zonse nzamure, ndi khonje, ndi kasiya;

m’zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu

mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.

9 Mwa omveka anu muli ana aakazi a mafumu;

ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu

wovala golide wa ku Ofiri.

10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako;

uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;

11 potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako,

pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.

12 Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso;

achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.

13 Mwana wamkazi wa mfumu

ngwa ulemerero wonse m’kati mwa nyumba,

zovala zake nza malukidwe agolide.

14 Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga,

anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.

15 Adzawatsogolera ndi chimwemwe ndi kusekerera,

adzalowa m’nyumba ya mfumu.

16 M’malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako,

udzawaika akhale mafumu m’dziko lonse lapansi.

17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m’mibadwomibadwo;

chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu

kunthawi za nthawi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/45-ceb1eb564497f56d68a77058a8f45072.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 46

Mulungu ndiye pothawirapo anthu ake

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Pa Alamot. Nyimbo.

1 Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,

thandizo lopezekeratu m’masautso.

2 Chifukwa chake sitidzachita mantha,

lingakhale lisandulika dziko lapansi,

angakhale mapiri asunthika, nakhala m’kati mwa nyanja.

3 Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu,

nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.

4 Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu.

Malo oyera okhalamo Wam’mwambamwamba.

5 Mulungu ali m’kati mwake, sudzasunthika,

Mulungu adzauthandiza mbandakucha.

6 Amitunduanapokosera, maufumu anagwedezeka,

ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.

7 Yehova wa makamu ali ndi ife;

Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

8 Idzani, penyani ntchito za Yehova,

amene achita zopululutsa padziko lapansi.

9 Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;

athyola uta, nadula nthungo;

atentha magaleta ndi moto.

10 Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu,

Ndidzabuka mwa amitundu,

ndidzabuka padziko lapansi.

11 Yehova wa makamu ali ndi ife,

Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/46-bca78a4e765d1c318275c4da76140e29.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 47

Mau a kulemekeza Mulungu mwini dziko lonse lapansi

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Ombani m’manja, mitundu yonse ya anthu;

fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.

2 Pakuti Yehova Wam’mwambamwamba ndiye woopsa;

ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.

3 Atigonjetsera anthu,

naikaamitundupansi pa mapazi athu.

4 Atisankhira cholowa chathu,

chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda.

5 Mulungu wakwera ndi mfuu,

Yehova ndi liu la lipenga.

6 Imbirani Mulungu, imbirani;

imbirani mfumu yathu, imbirani.

7 Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi;

imbirani ndi chilangizo.

8 Mulungu ndiye mfumu ya amitundu,

Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.

9 Akulu a anthu asonkhana

akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu,

pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;

akwezeka kwakukulu Iyeyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/47-3f699d23b0b2fdb809c608e8b2a6d8f4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 48

Ukoma ndi ulemerero wa Ziyoni

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,

m’mzinda wa Mulungu wathu, m’phiri lake loyera.

2 Phiri laZiyoni, chikhalidwe chake nchokoma

kumbali zake za kumpoto,

ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi,

mzinda wa mfumu yaikulu.

3 Mulungu adziwika m’zinyumba zake ngati msanje.

4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,

anapitira pamodzi.

5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;

anaopsedwa, nathawako.

6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;

anamva chowawa, ngati wam’chikuta.

7 Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum’mawa.

8 Monga tidamva, momwemo tidapenya

m’mzinda wa Yehova wa makamu, m’mzinda wa Mulungu wathu,

Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.

9 Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu,

m’kati mwa Kachisi wanu.

10 Monga dzina lanu, Mulungu,

momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi;

m’dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.

11 Likondwere phiri la Ziyoni,

asekere ana aakazi a Yuda,

chifukwa cha maweruzo anu.

12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge,

werengani nsanja zake.

13 Penyetsetsani malinga ake,

yesetsani zinyumba zake;

kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m’mbuyo.

14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu

kunthawi za nthawi,

adzatitsogolera kufikira imfa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/48-ba5befffea5b0683b72b66ebb5cb961c.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 49

Za pansi pano nza chabe

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Dzamveni kuno, anthu inu nonse;

tcherani khutu, inu nonse amakono,

2 awamba ndi omveka omwe,

achuma ndi aumphawi omwe.

3 Pakamwa panga padzanena zanzeru;

ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso.

4 Ndidzatchera khutu kufanizo,

ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.

5 Ndidzaoperanji masiku oipa,

pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene?

6 Iwo akutama kulemera kwao;

nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao;

7 kuombola mbale sangadzamuombole,

kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.

8 Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali,

ndipo chilekeke nthawi zonse.

9 Kuti akhale ndi moyo osafa,

osaona chivundi.

10 Pakuti aona anzeru amafa,

monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,

nasiyira ena chuma chao.

11 Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire,

ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo;

atchapo dzina lao padziko pao.

12 Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa,

afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.

13 Njira yao ino ndiyo kupusa kwao,

koma akudza m’mbuyo avomereza mau ao.

14 Aikidwa m’manda ngati nkhosa;

mbusa wao ndi imfa.

Ndipo m’mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao;

ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda,

kuti pokhala pake padzasowa.

15 Koma Mulungu adzaombola moyo wanga

kumphamvu ya manda.

Pakuti adzandilandira ine.

16 Usaope polemezedwa munthu,

pochuluka ulemu wa nyumba yake;

17 pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse;

ulemu wake sutsika naye kumtsata m’mbuyo.

18 Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo,

ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma.

19 Adzamuka kumbadwo wa makolo ake;

sadzaona kuunika nthawi zonse.

20 Munthu waulemu, koma wosadziwitsa,

afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/49-63177fae33b2620218f9b42ce5891658.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 50

Mulungu woweruza wa dziko lapansi

Salimo la Asafu.

1 Mulungu wa milungu, Yehova, wanena,

aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa

kufikira kulowa kwake.

2 Mulungu awalira muZiyoni, mokongola mwangwiro.

3 Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete.

Moto udzanyeka pankhope pake,

ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.

4 Kumwamba adzaitana zakumwamba,

ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ake.

5 Mundisonkhanitsire okondedwa anga,

amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.

6 Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake;

pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.

7 Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena;

Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe,

Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.

8 Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako;

popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire.

9 Sindidzatenga ng’ombe m’nyumba mwako,

kapena mbuzi m’makola mwako.

10 Pakuti zamoyo zonse zakuthengo ndi zanga,

ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi.

11 Ndidziwa mbalame zonse za m’mapiri,

ndipo nyama zakuthengo zili ndi Ine.

12 Ndikamva njala, sindidzakuuza,

pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.

13 Kodi ndidzadya nyama ya ng’ombe,

kapena kumwa mwazi wa mbuzi?

14 Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko;

numchitire Wam’mwambamwamba chowinda chako.

15 Ndipo undiitane tsiku la chisautso,

ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

16 Koma kwa woipa Mulungu anena,

Uli nao chiyani malemba anga kulalikira,

ndi kutchula pangano langa pakamwa pako?

17 Popeza udana nacho chilangizo,

nufulatira mau anga.

18 Pakuona mbala, uvomerezana nayo,

nuchita nao achigololo.

19 Pakamwa pako mpochita zochimwa,

ndipo lilime lako likonza chinyengo.

20 Ukhala, nuneneza mbale wako;

usinjirira mwana wa mai wako.

21 Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine;

unayesa kuti ndifanana nawe,

ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.

22 Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu,

kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.

23 Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine;

ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake

ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/50-560e40fe908a0fdfb883d26be90e44ef.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 51

Davide avomereza kuchimwa kwake, apempha Mulungu amkhululukire, asamchotsere Mzimu Woyera

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide; m’mene anamdzera Natani mneneriyo atalowa iye kwa Bateseba.

1 Mundichitire ine chifundo, Mulungu,

monga mwa kukoma mtima kwanu;

monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma

mufafanize machimo anga.

2 Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga,

ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.

3 Chifukwa ndazindikira machimo anga;

ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.

4 Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa,

ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu;

kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu,

mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.

5 Onani, ndinabadwa m’mphulupulu,

ndipo mai wanga anandilandira m’zoipa.

6 Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m’malo a m’katimo;

ndipo m’malo a m’tseri mudzandidziwitsa nzeru.

7 Mundiyeretse ndihisopendipo ndidzayera;

munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.

8 Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera,

kuti mafupawo munawathyola akondwere.

9 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,

ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.

10 Mundilengere mtima woyera, Mulungu;

mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.

11 Musanditaye kundichotsa pamaso panu;

musandichotsere Mzimu wanu Woyera.

12 Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu;

ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

13 Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu;

ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.

14 Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu,

ndinu Mulungu wa chipulumutso changa;

lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.

15 Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;

ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.

16 Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;

nsembe yopsereza simuikonda.

17 Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;

Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

18 ChitiraniZiyonichokoma monga mwa kukondwera kwanu;

mumange malinga a miyala aYerusalemu.

19 Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo,

ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu;

pamenepo adzapereka

ng’ombe paguwa lanu la nsembe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/51-301c95ad4d072dd3013079c69eead3fa.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 52

Davide aneneratu za chionongeko cha oipa, iye nakhulupirira Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha Davide; muja analowa Doegi Mwedomu nauza Saulo nati kwa iye, Davide walowa m’nyumba ya Ahimeleki.

1 Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe?

Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.

2 Lilime lako likupanga zoipa;

likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga.

3 Ukonda choipa koposa chokoma;

ndi bodza koposa kunena chilungamo,

4 ukonda mau onse akuononga,

lilime lachinyengo, iwe.

5 Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse,

adzakuchotsa nadzakukwatula m’hema mwako,

nadzakuzula, kukuchotsa m’dziko la amoyo.

6 Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa,

nadzamseka, ndi kuti,

7 Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake;

amene anatama kuchuluka kwa chuma chake,

nadzilimbitsa m’kuipsa kwake.

8 Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi waazitona

m’nyumba ya Mulungu.

Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.

9 Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi,

ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma,

pamaso pa okondedwa anu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/52-714c69d5d39300a0a025329eac12d0ed.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 53

Kupusa ndi kuipa kwa anthu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Mahalati. Chilangizo cha Davide.

1 Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.

Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa;

kulibe wakuchita bwino.

2 Mulungu m’mwamba anaweramira pa ana a anthu,

kuti aone ngati aliko wanzeru,

wakufuna Mulungu.

3 Onse anabwerera; anavunda mtima pamodzi;

palibe mmodzi wakuchita bwino, nnena mmodzi.

4 Kodi ochita zopanda pake sadziwa?

Pomadya anthu anga monga akudya mkate;

ndipo saitana Mulungu.

5 Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa,

pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe;

unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.

6 Ha, chipulumutso cha Israele chichokere muZiyoni!

Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m’ndende,

Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/53-f695e745f1b28f07ca0f2bd5d9677d56.mp3?version_id=1068—