Categories
MASALIMO

MASALIMO 34

Davide alemekeza Yehova womlanditsa, nafulumiza ena amtame

Salimo la Davide; muja anasintha makhalidwe ake pamaso pa Abimeleki, amene anampirikitsa, ndipo anachoka.

1 Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse;

kumlemekeza kwake kudzakhala m’kamwa mwanga kosalekeza.

2 Moyo wanga udzatamanda Yehova;

ofatsa adzakumva nadzakondwera.

3 Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova,

ndipo tikweze dzina lake pamodzi.

4 Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera,

nandilanditsa m’mantha anga onse.

5 Iwo anayang’ana Iye nasanguluka;

ndipo pankhope pao sipadzachita manyazi.

6 Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva,

nampulumutsa m’masautso ake onse.

7 Mngelowa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye,

nawalanditsa iwo.

8 Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;

wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

9 Opani Yehova, inu oyera mtima ake;

chifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

10 Misona ya mkango isowa nimva njala,

koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

11 Idzani ananu ndimvereni ine,

ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

12 Munthu wokhumba moyo ndani,

wokonda masiku, kuti aone zabwino?

13 Uletse lilime lako lisatchule zoipa,

ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.

14 Futuka pazoipa, nuchite zabwino,

funa mtendere ndi kuulondola.

15 Maso a Yehova ali pa olungama mtima,

ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.

16 Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa,

kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.

17 Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva,

nawalanditsa kumasautso ao onse.

18 Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka,

apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

19 Masautso a wolungama mtima achuluka,

koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.

20 Iye asunga mafupa ake onse;

silinathyoke limodzi lonse.

21 Mphulupulu idzamupha woipa;

ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

22 Yehova aombola moyo wa anyamata ake,

ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/34-fddb50ecc3982b4253380c39b2d29221.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 35

Davide apempha Mulungu alange oipa

Salimo la Davide.

1 Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova;

limbanani nao iwo akulimbana nane.

2 Gwirani chikopa chotchinjiriza,

ukani kundithandiza.

3 Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola.

Nenani ndi moyo wanga,

Chipulumutso chako ndine.

4 Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga;

abwezedwe m’mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.

5 Akhale monga mungu kumphepo,

ndipomngelowa Yehova awapirikitse.

6 Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera,

ndipo mngelo wa Yehova awalondole.

7 Pakuti ananditchera ukonde wao m’mbunamo kopanda chifukwa,

anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa.

8 Chimgwere modzidzimutsa chionongeko;

ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini,

agwemo, naonongeke m’mwemo.

9 Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova;

udzasekera mwa chipulumutso chake.

10 Mafupa anga onse adzanena,

Yehova, afanana ndi Inu ndani,

wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu,

ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?

11 Mboni za chiwawa ziuka,

zindifunsa zosadziwa ine.

12 Andibwezera choipa m’malo mwa chokoma,

inde, asaukitsa moyo wanga.

13 Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli.

Ndinazunza moyo wanga ndi kusala;

ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa.

14 Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa,

kapena mbale wanga;

polira ndinaweramira pansi,

monga munthu wakulira maliro amai wake.

15 Ndipo pakutsimphina ine anakondwera,

nasonkhana pamodzi;

akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe,

ananding’amba osaleka.

16 Pakati pa onyodola pamadyerero,

anandikukutira mano.

17 Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji?

Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao,

wanga wa wokha kwa misona ya mkango.

18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;

m’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.

19 Adani anga asandikondwerere ine monyenga;

okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.

20 Pakuti salankhula zamtendere,

koma apangira chiwembu odekha m’dziko.

21 Ndipo andiyasamira m’kamwa mwao;

nati, Hede, Hede, diso lathu lidachipenya.

22 Yehova, mudazipenya; musakhale chete,

Ambuye, musakhale kutali ndi ine.

23 Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga,

Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.

24 Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu,

Yehova Mulungu wanga;

ndipo asandisekerere ine.

25 Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo!

Asanene, Tammeza iye.

26 Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera

chifukwa cha choipa chidandigwera.

Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.

27 Afuule mokondwera nasangalale

iwo akukondwera nacho chilungamo changa,

ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova,

amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.

28 Ndipo lilime langa lilalikire chilungamo chanu,

ndi lemekezo lanu tsiku lonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/35-5ad349840a1959a8937cc9073d44af98.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 36

Kuipitsitsa kwa anthu, kukometsetsa kwa Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

1 Cholakwa cha woipayo chimati m’kati mwa mtima wanga,

palibe kuopa Mulungu pamaso pake.

2 Pakuti adzidyoletsa yekha m’kuona kwake,

kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.

3 Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga,

waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.

4 Alingirira zopanda pake pakama pake;

adziika panjira posati pabwino;

choipa saipidwa nacho.

5 Yehova, m’mwamba muli chifundo chanu;

choonadi chanu chifikira kuthambo.

6 Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu;

maweruzo anu akunga chozama chachikulu,

Yehova, musunga munthu ndi nyama.

7 Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi!

Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.

8 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m’nyumba mwanu,

ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

9 Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu,

M’kuunika kwanu tidzaona kuunika.

10 Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu;

ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima.

11 Phazi la akudzikuza lisandifikire ine,

ndi dzanja la oipa lisandichotse.

12 Pomwepo padagwera ochita zopanda pake.

Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/36-41066793019d717dbea4c3065b406512.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 37

Kusangalala kwa ochimwa kudzatha, olungama akhalitsa nathandizidwa ndi Mulungu

Salimo la Davide.

1 Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa,

usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.

2 Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,

ndipo adzafota monga msipu wauwisi.

3 Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma;

khala m’dziko, ndipo tsata choonadi.

4 Udzikondweretsenso mwa Yehova;

ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

5 Pereka njira yako kwa Yehova;

khulupiriranso Iye, adzachichita.

6 Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika,

ndi kuweruza kwako monga usana.

7 Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye;

usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m’njira yake,

chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

8 Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo;

usavutike mtima ungachite choipa.

9 Pakuti ochita zoipa adzadulidwa;

koma iwo akuyembekeza Yehova,

iwowa adzalandira dziko lapansi.

10 Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti;

inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.

11 Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;

nadzakondwera nao mtendere wochuluka.

12 Woipa apangira chiwembu wolungama,

namkukutira mano.

13 Ambuye adzamseka,

popeza apenya kuti tsiku lake likudza.

14 Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;

alikhe ozunzika ndi aumphawi,

aphe amene ali oongoka m’njira.

15 Lupanga lao lidzalowa m’mtima mwao momwe,

ndipo mauta ao adzathyoledwa.

16 Zochepa zake za wolungama zikoma

koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.

17 Pakuti manja a oipa adzathyoledwa,

koma Yehova achirikiza olungama.

18 Yehova adziwa masiku a anthu angwiro;

ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha.

19 Sadzachita manyazi m’nyengo yoipa,

ndipo m’masiku a njala adzakhuta.

20 Pakuti oipa adzatayika,

ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa;

adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.

21 Woipa akongola, wosabweza,

koma wolungama achitira chifundo, napereka.

22 Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;

koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.

23 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;

ndipo akondwera nayo njira yake.

24 Angakhale akagwa, satayikiratu,

pakuti Yehova agwira dzanja lake.

25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba;

ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa,

kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

26 Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa;

ndipo mbumba zake zidalitsidwa.

27 Siyana nacho choipa, nuchite chokoma,

nukhale nthawi zonse.

28 Pakuti Yehova akonda chiweruzo,

ndipo sataya okondedwa ake.

Asungika kosatha,

koma adzadula mbumba za oipa.

29 Olungama adzalandira dziko lapansi,

nadzakhala momwemo kosatha.

30 Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,

ndi lilime lake linena chiweruzo.

31 Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake;

pakuyenda pake sadzaterereka.

32 Woipa aunguza wolungama,

nafuna kumupha.

33 Yehova sadzamsiya m’dzanja lake;

ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.

34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yake,

ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.

Pakudulidwa oipa udzapenya.

35 Ndapenya woipa, alikuopsa,

natasa monga mtengo wauwisi wanzika.

36 Koma anapita ndipo taona, kwati zii;

ndipo ndinampwaira osampeza.

37 Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!

Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.

38 Koma olakwa adzaonongeka pamodzi;

matsiriziro a oipa adzadulidwa.

39 Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova,

Iye ndiye mphamvu yao m’nyengo ya nsautso.

40 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa;

awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa,

chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/37-b05a1f859375b97fcce3087bbc69abe3.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 38

Davide awulula zoipa zake, apempha Mulungu amkhululukire namthandize

Salimo la Davide, lakukumbutsa.

1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu,

ndipo musandilange moopsa m’mtima mwanu.

2 Pakuti mivi yanu yandilowa,

ndi dzanja lanu landigwera.

3 Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu;

ndipo m’mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.

4 Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga;

ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.

5 Mabala anga anunkha, adaola,

chifukwa cha kupusa kwanga.

6 Ndapindika, ndawerama kwakukulu;

ndimayenda woliralira tsiku lonse.

7 Pakuti m’chuuno mwanga mutentha kwambiri;

palibe pamoyo m’mnofu mwanga.

8 Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa,

ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.

9 Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu;

ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.

10 Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka,

ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera.

11 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;

ndipo anansi anga aima patali.

12 Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga;

ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga,

nalingirira zonyenga tsiku lonse.

13 Koma ine, monga gonthi, sindimva;

ndipo monga munthu wosalankhula,

sinditsegula pakamwa panga.

14 Inde ndikunga munthu wosamva,

ndipo m’kamwa mwanga mulibe makani.

15 Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova;

Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.

16 Pakuti ndinati, Asakondwerere ine;

pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.

17 Ndafikana potsimphina,

ndipo chisoni changa chili pamaso panga chikhalire.

18 Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga;

nditenga nkhawa chifukwa cha tchimo langa.

19 Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu,

ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.

20 Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino

atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.

21 Musanditaye, Yehova,

Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.

22 Fulumirani kundithandiza,

Ambuye, chipulumutso changa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/38-7b3dae37b413a81d84a084883bd1d0e0.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 39

Kupepuka kwa moyo uno

Kwa Mkulu wa Nyimbo, kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

1 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,

kuti ndingachimwe ndi lilime langa.

Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham’kamwa,

pokhala woipa ali pamaso panga.

2 Ndinatonthola osanena mau,

ndinakhala chete osalawa chokoma;

ndipo chisoni changa chinabuka.

3 Mtima wanga unatentha m’kati mwa ine;

unayaka moto pakulingirira ine.

Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa,

4 Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa,

ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;

ndidziwe malekezero anga.

5 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;

ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu,

Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.

6 Indedi munthu ayenda ngati mthunzi;

Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma,

ndipo sadziwa adzachilandira ndani?

7 Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani?

Chiyembekezo changa chili pa Inu.

8 Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse,

musandiike ndikhale chotonza cha wopusa.

9 Ndinakhala duu, sindinatsegule pakamwa panga;

chifukwa inu mudachichita.

10 Mundichotsere chovutitsa chanu;

pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu.

11 Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu,

mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete.

Indedi, munthu aliyense ali chabe.

12 Imvani pemphero langa, Yehova,

ndipo tcherani khutu kulira kwanga;

musakhale chete pa misozi yanga;

Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu,

wosakhazikika, monga makolo anga onse.

13 Ndiloleni, kuti nditsitsimuke,

ndisanamuke ndi kukhala kuli zii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/39-1e42e71a4b9cc5abcfdee62c5502a571.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 40

Alemekeza chipulumutso cha Mulungu, alalikira poyera chilungamo cha Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;

ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.

2 Ndipo anandikweza kunditulutsa m’dzenje la chitayiko,

ndi m’thope la pachithaphwi;

nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

3 Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,

chilemekezo cha kwa Mulungu wanga;

ambiri adzachiona, nadzaopa,

ndipo adzakhulupirira Yehova.

4 Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;

wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.

5 Inu, Yehova, Mulungu wanga,

zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri,

ndipo zolingirira zanu za pa ife;

palibe wina wozifotokozera Inu;

ndikazisimba ndi kuzitchula,

zindichulukira kuziwerenga.

6 Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo;

mwanditsegula makutu.

Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.

7 Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza;

m’buku mwalembedwa za Ine,

8 kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga;

ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.

9 Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu;

onani, sindidzaletsa milomo yanga,

mudziwa ndinu Yehova.

10 Chilungamo chanu sindinachibise m’kati mwamtima mwanga;

chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena;

chifundo chanu ndi choonadi chanu

sindinachibisire msonkhano waukulu.

11 Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu,

chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.

Pemphero lopempha chithandizo

12 Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,

zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;

ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.

13 Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni;

fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

14 Achite manyazi nadodome

iwo akulondola moyo wanga kuti auononge.

Abwerere m’mbuyo, nachite manyazi

iwo okondwera kundichitira choipa.

15 Apululuke, mobwezera manyazi ao

amene anena nane, Hede, hede.

16 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;

iwo akukonda chipulumutso chanu

asaleke kunena, Abuke Yehova.

17 Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi;

koma Ambuye andikumbukira ine.

Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga,

musamachedwa, Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/40-d3f26f2ab09029c80757c98a1bc7ef02.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 41

Mulungu adalitsa wosamalira osauka. Adani ndi mabwenzi amchitira Davide zoipa, Mulungu amlanditse

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Wodala iye amene asamalira wosauka!

Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo,

ndipo adzadalitsika padziko lapansi,

ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.

3 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;

podwala iye mukonza pogona pake.

4 Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova;

Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu.

5 Adani anga andinenera choipa, ndi kuti,

adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?

6 Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;

mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake,

akanka nayenda namakanena.

7 Onse akudana nane andinong’onezerana;

apangana chondiipsa ine.

8 Chamgwera chinthu choopsa, ati;

popeza ali gonire sadzaukanso.

9 Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira,

ndiye amene adadyako mkate wanga,

anandikwezera chidendene chake.

10 Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse,

kuti ndiwabwezere.

11 Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine,

popeza mdani wanga sandiseka.

12 Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga,

ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.

13 Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele,

kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.

Amen, ndi Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/41-537b08f0cc93ae7eeaae58059123a735.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 42

Mtima wolira kuyanjana ndi Mulungu mu Kachisi

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora.

1 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;

motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

2 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu,

la kwa Mulungu wamoyo.

Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?

3 Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa,

usana ndi usiku;

pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,

Mulungu wako ali kuti?

4 Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m’kati mwa ine,

pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu,

ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu,

ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika,

ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso

chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

6 Mulungu wanga, moyo wanga

udziweramira m’kati mwanga;

chifukwa chake ndikumbukira Inu m’dziko la Yordani,

ndi mu Aheremoni, m’kaphiri ka Mizara.

7 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,

pa mkokomo wa matiti anu;

mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.

8 Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake,

ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine.

Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.

9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa,

mwandiiwala chifukwa ninji?

Ndimayenderanji wakulira

chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?

10 Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga;

pakunena ndine dzuwa lonse,

Mulungu wako ali kuti?

11 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,

ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/42-ae42dc50afb061e3a3a74ad4c3630ce9.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 43

Davide alira akhale ku Kachisi

1 Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo.

Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.

2 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?

Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?

3 Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere;

zindifikitse kuphiri lanu loyera,

kumene mukhala Inuko.

4 Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,

kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni,

ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,

ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/43-8197488d3ef56fba8d833b7567548e6e.mp3?version_id=1068—