Categories
MASALIMO

MASALIMO 24

Ulemerero wa Yehova

Salimo la Davide.

1 Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe,

dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m’mwemo.

2 Pakuti Iye analimanga pazinyanja,

nalikhazika pamadzi.

3 Adzakwera ndani m’phiri la Yehova?

Nadzaima m’malo ake oyera ndani?

4 Woyera m’manja, ndi woona m’mtima, ndiye;

iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe,

ndipo salumbira monyenga.

5 Iye adzalandira dalitso kwa Yehova,

ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.

6 Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,

iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.

7 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;

ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha,

kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.

8 Mfumu imene ya ulemerero ndani?

Yehova wamphamvu ndi wolimba,

Yehova wolimba kunkhondo.

9 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;

inde weramutsani, zitseko zosatha inu,

kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.

10 Mfumu imene ya ulemerero ndani?

Yehova wa makamumakamu,

ndiye Mfumu ya ulemerero.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/24-0f47e0f7343c5bc9f37210a8a529040a.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 25

Davide apempha Mulungu amlanditse kwa adani

Salimo la Davide.

1 Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova.

2 Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu,

ndisachite manyazi;

adani anga asandiseke ine.

3 Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi;

adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.

4 Mundidziwitse njira zanu,

Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.

5 Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse;

pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa;

Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

6 Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu;

pakuti izi nza kale lonse.

7 Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga

kapena zopikisana nanu.

Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu,

chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

8 Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima,

chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira.

9 Adzawatsogolera ofatsa m’chiweruzo;

ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.

10 Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi,

kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.

11 Chifukwa cha dzina lanu, Yehova,

ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.

12 Munthuyo wakuopa Yehova ndani?

Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.

13 Moyo wake udzakhala mokoma;

ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.

14 Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye;

ndipo adzawadziwitsa pangano lake.

15 Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka;

pakuti Iye adzaonjola mapazi anga mu ukonde.

16 Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo;

pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika.

17 Masautso a mtima wanga akula,

munditulutse m’zondipsinja.

18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga;

ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.

19 Penyani adani anga, popeza achuluka;

ndipo andida ndi udani wachiwawa.

20 Sungani moyo wanga, ndilanditseni,

ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.

21 Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,

pakuti ndayembekezera Inu.

22 Ombolani Israele, Mulungu,

m’masautso ake onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/25-6c03c4b9e544cdd9107e6f76a782fa68.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 26

Davide popempha Mulungu amweruze, atchula zokoma zake

Salimo la Davide.

1 Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga,

ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.

2 Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;

yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.

3 Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga;

ndipo ndayenda m’choona chanu.

4 Sindinakhala pansi ndi anthu achabe;

kapena kutsagana nao anthu othyasika.

5 Ndidana nao msonkhano wa ochimwa,

ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa.

6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;

kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;

7 kuti ndimveketse mau a chiyamiko,

ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.

8 Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu,

ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.

9 Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,

kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;

10 amene m’manja mwao muli mphulupulu,

ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.

11 Koma ine, ndidzayenda mu ungwiro wanga;

mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.

12 Phazi langa liponda pachidikha,

m’misonkhano ndidzalemekeza Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/26-98dd20ba10f08be410bb9361a3194952.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 27

Davide atamadi Yehova, naliradi kuyanjana ndi Mulungu

Salimo la Davide.

1 Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

2 Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga,

inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.

3 Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,

mtima wanga sungachite mantha;

ingakhale nkhondo ikandiukira,

inde pomweponso ndidzakhulupirira.

4 Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,

ndidzachilondola ichi,

Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,

kupenya kukongola kwake kwa Yehova

ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.

5 Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake,

adzandibisa mkati mwa chihema chake;

pathanthwe adzandikweza.

6 Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka

pamwamba pa adani anga akundizinga;

ndipo ndidzapereka m’chihema mwake

nsembe za kufuula mokondwera;

ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.

7 Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine;

mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze.

8 Pamene munati, Funani nkhope yanga;

mtima wanga unati kwa Inu.

Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.

9 Musandibisire ine nkhope yanu;

musachotse kapolo wanu ndi kukwiya.

Inu munakhala thandizo langa;

musanditaye, ndipo musandisiye

Mulungu wa chipulumutso changa.

10 Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,

koma Yehova anditola.

11 Mundiphunzitse njira yanu, Yehova,

munditsogolere panjira yachidikha,

chifukwa cha adani anga.

12 Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa,

chifukwa zinandiukira mboni zonama

ndi iwo akupumira zachiwawa.

13 Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova

m’dziko la amoyo, ndikadatani!

14 Yembekeza Yehova,

limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako;

inde, yembekeza Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/27-def2c9f5a95c37697f91c2701787cbe3.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 28

Apempha chipulumutso, ayamika populumutsidwa

Salimo la Davide.

1 Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira;

thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva;

pakuti ngati munditontholera ine,

ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.

2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,

pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.

3 Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa,

ndi ochita zopanda pake;

amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,

koma mumtima mwao muli choipa.

4 Muwapatse monga mwa ntchito zao,

ndi monga mwa choipa chochita iwo;

muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao;

muwabwezere zoyenera iwo.

5 Pakuti sasamala ntchito za Yehova,

kapena machitidwe a manja ake,

adzawapasula, osawamanganso.

6 Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.

7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa;

mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza,

chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu;

ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

8 Yehova ndiye mphamvu yao,

inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.

9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu;

muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/28-18f7c07f0c5a257e43abf9589f958ea2.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 29

Achenjeza akulu alemekeze Mulungu

Salimo la Davide.

1 Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

2 Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake,

gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.

3 Liu la Yehova lili pamadzi;

Mulungu wa ulemerero agunda,

ndiye Yehova pamadzi ambiri.

4 Liu la Yehova ndi lamphamvu;

liu la Yehova ndi lalikulukulu.

5 Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;

inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.

6 Aitumphitsa monga mwanawang’ombe;

Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.

7 Liu la Yehova ligawa malawi a moto.

8 Liu la Yehova ligwedeza chipululu;

Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi.

9 Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,

ndipo lipulula nkhalango;

ndipo mu Kachisi mwake zonse zili m’mwemo zimati, Ulemerero.

10 Yehova anakhala pa chigumula,

inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya.

11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu,

Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/29-11d4e31f4df43387d25d187297c4fd77.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 30

Mkwiyo wa Mulungu ukhala kanthawi, kuyanja kwao ndi kosatha

Salimo la Davide. Nyimbo yakuperekera nyumba kwa Mulungu.

1 Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa,

ndipo simunandikondwetsere adani anga.

2 Yehova, Mulungu wanga,

ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.

3 Yehova munabweza moyo wanga kumanda,

munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.

4 Imbirani Yehova, inu okondedwa ake,

ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.

5 Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha;

koma kuyanja kwake moyo wonse.

Kulira kuchezera,

koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

6 Ndipo ine, ndinanena m’phindu langa,

sindidzagwedezeka nthawi zonse.

7 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu;

munabisa nkhope yanu; ndinaopa.

8 Ndinafuulira kwa Inu, Yehova;

kwa Ambuye ndinapemba,

9 M’mwazi mwanga muli phindu lanji,

potsikira ine kudzenje?

Ngati fumbi lidzayamika Inu?

Ngati lidzalalikira choonadi chanu?

10 Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo,

Yehova, mundithandize ndi Inu.

11 Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera;

munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,

12 kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete.

Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/30-94c410991fb6fa5a91232c2b3b49d4ac.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 31

Davide apempha kolimba Mulungu amlanditse, natama chifundo chao, nauzitsa anthu a Mulungu amtame

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Ndakhulupirira Inu, Yehova,

ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse,

mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.

2 Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga.

Mundikhalire ine thanthwe lolimba,

nyumba yamalinga yakundisunga.

3 Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa;

ndipo chifukwa cha dzina lanu

ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.

4 Mundionjole mu ukonde umene ananditchera mobisika.

Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.

5 Ndipereka mzimu wanga m’dzanja lanu;

mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa choonadi.

6 Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama,

koma ndikhulupirira Yehova.

7 Ndidzakondwera ndi kusangalala m’chifundo chanu,

pakuti mudapenya zunzo langa;

ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.

8 Ndipo simunandipereke m’dzanja la mdani;

munapondetsa mapazi anga pali malo.

9 Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine.

Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga,

zapuwala ndi mavuto.

10 Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni,

ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo.

Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga,

ndi mafupa anga apuwala.

11 Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse,

inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa;

iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

12 Ndaiwalika m’mtima monga wakufa,

ndikhala monga chotengera chosweka.

13 Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri,

mantha andizinga.

Pondipangira chiwembu,

anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

14 Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova,

ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.

15 Nyengo zanga zili m’manja mwanu,

mundilanditse m’manja a adani anga,

ndi kwa iwo akundilondola ine.

16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu,

mundipulumutse ndi chifundo chanu.

17 Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu,

oipa achite manyazi, atonthole m’manda.

18 Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza,

imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima,

ndi kudzikuza ndi kunyoza.

19 Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga,

kumene munasungira iwo akuopa Inu,

kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu,

pamaso pa ana a anthu!

20 Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu,

mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse

pa kutetana kwa malilime.

21 Wolemekezeka Yehova,

pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa

m’mzinda walinga.

22 Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati,

Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu.

Komatu munamva mau a kupemba kwanga

pamene ndinafuulira kwa Inu.

23 Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake,

Yehova asunga okhulupirika,

ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.

24 Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu,

inu nonse akuyembekeza Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/31-95e6f9d75c35ecc2076f587382352d82.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 32

Mwai wa munthu amene Mulungu wamkhululukira

Salimo la Davide. Chilangizo.

1 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake;

wokwiriridwa choipa chake.

2 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake;

ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.

3 Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba

ndi kubuula kwanga tsiku lonse.

4 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;

uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

5 Ndinavomera choipa changa kwa Inu;

ndipo mphulupulu yanga sindinaibise.

Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga;

ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.

6 Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu,

pa nthawi ya kupeza Inu;

indetu pakusefuka madzi aakulu

sadzamfikira iye.

7 Inu ndinu mobisalira mwanga;

m’nsautso mudzandisunga;

mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.

8 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;

ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.

9 Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru;

zomangira zao ndizo cham’kamwa ndi chapamutu zakuwakokera,

pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.

10 Zisoni zambiri zigwera woipa;

koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.

11 Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;

ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/32-8b62cf41b1629155077301dc08c38e74.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 33

Alemekeza Mulungu wolenga, wosunga zonse

1 Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima,

oongoka mtima ayenera kulemekeza.

2 Yamikani Yehova ndi zeze;

muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.

3 Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano;

muimbe mwaluso kumveketsa mau.

4 Pakuti mau a Yehova ali olunjika;

ndi ntchito zake zonse zikhulupirika.

5 Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo,

dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova.

6 Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova;

ndipo ndi mpweya wa m’kamwa mwake khamu lao lonse.

7 Amaunjika madzi a m’nyanja monga mulu,

amakundika zakudya mosungiramo.

8 Dziko lonse lapansi liope Yehova,

ponse pali anthu achite mantha chifukwa cha Iye.

9 Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa;

analamulira, ndipo chinakhazikika.

10 Yehova aphwanya upo waamitundu,

asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11 Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire,

zolingirira za m’mtima mwake ku mibadwomibadwo.

12 Wodalitsika mtundu wa anthu

umene Yehova ndiye Mulungu wao;

mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.

13 Yehova apenyerera m’mwamba;

aona ana onse a anthu.

14 M’malo akhalamo Iye, amapenya pansi

pa onse akukhala m’dziko lapansi.

15 Iye amene akonza mitima ya iwo onse,

amene azindikira zochita zao zonse.

16 Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa,

mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona.

17 Kavalo safikana kupulumuka naye,

chinkana mphamvu yake njaikulu sapulumutsa.

18 Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye,

pa iwo akuyembekeza chifundo chake.

19 Kupulumutsa moyo wao kwa imfa,

ndi kuwasunga ndi moyo m’nyengo ya njala.

20 Moyo wathu walindira Yehova;

Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu.

21 Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye,

chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.

22 Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife,

monga takuyembekezani Inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/33-290a5e48f820310e3fb6c329165e9f93.mp3?version_id=1068—