Categories
MASALIMO

MASALIMO 4

Pemphero posautsidwa

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide.

1 Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa;

pondichepera mwandikulitsira malo.

Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.

2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?

Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?

3 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo,

adzamva Yehova m’mene ndimfuulira Iye.

4 Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.

Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.

5 Iphani nsembe za chilungamo,

ndipo mumkhulupirire Yehova.

6 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani?

Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

7 Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga,

chakuposa chao m’nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.

8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;

chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/4-41ebdc08e25d9ab62ee6ed79d53b14ad.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 5

Matsoka a oipa, madalitso a olungama

Kwa Mkulu wa Nyimbo: aimbire zitoliro. Salimo la Davide.

1 Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.

2 Tamvetsani mau a kufuula kwanga,

Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga;

pakuti kwa Inu ndimapemphera.

3 M’mawa, Yehova, mudzamva mau anga;

m’mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.

4 Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa

mphulupulu siikhala ndi Inu.

5 Opusa sadzakhazikika pamaso panu,

mudana nao onse akuchita zopanda pake.

6 Mudzaononga iwo akunena bodza;

munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo,

Yehova anyansidwa naye.

7 Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu

ndidzalowa m’nyumba yanu;

ndidzagwada kuyang’ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.

8 Yehova, munditsogolere m’chilungamo chanu,

chifukwa cha akundizondawo;

mulungamitse njira yanu pamaso panga.

9 Pakuti m’kamwa mwao mulibe mau okhazikika;

m’kati mwao m’mosakaza;

m’mero mwao ndi manda apululu;

lilime lao asyasyalika nalo.

10 Muwayese otsutsika Mulungu;

agwe nao uphungu wao.

M’kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse;

pakuti anapikisana ndi Inu.

11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,

afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;

nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.

12 Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;

mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/5-7ac8e9291abfdad07ec8a74c1b4764ae.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 6

Davide apempha chifundo kwa Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto, pa Seminiti. Salimo la Davide.

1 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,

ndipo musandilange muukali wanu.

2 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine.

Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.

3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu;

ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?

4 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;

ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.

5 Pakuti muimfa m’mosakumbukira Inu;

m’mandamo adzakuyamikani ndani?

6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga;

ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;

mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

7 Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni;

lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.

8 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake;

pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.

9 Wamva Yehova kupemba kwanga;

Yehova adzalandira pemphero langa.

10 Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu

adani anga onse;

adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/6-12e6ac2c0a2d65440fbb65d805f91b7a.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 7

Adani amzinga, Davide adziponya kwa Mulungu

Syigayoni wa Davide woimbira Yehova, chifukwa cha mau a Kusi Mbenjamini.

1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu;

mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

2 kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,

ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.

3 Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi;

ngati m’manja anga muli chosalungama;

4 ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine;

(inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);

5 mdani alondole moyo wanga, naupeze;

naupondereze pansi moyo wanga,

naukhalitse ulemu wanga m’fumbi.

6 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,

nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa;

ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.

7 Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;

ndipo pamwamba pao mubwerere kunka kumwamba.

8 Yehova aweruza anthu mlandu;

mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa,

ndi ungwiro wanga uli mwa ine.

9 Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani,

koma wolungamayo mumkhazikitse.

Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.

10 Chikopa changa chili ndi Mulungu,

wopulumutsa oongoka mtima.

11 Mulungu ndiye Woweruza wolungama,

ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.

12 Akapanda kutembenuka munthu,

iye adzanola lupanga lake;

wakoka uta wake, naupiringidza.

13 Ndipo anamkonzera zida za imfa;

mivi yake aipanga ikhale yansakali.

14 Taonani, ali m’chikuta cha zopanda pake;

anaima ndi chovuta, nabala bodza.

15 Anachita dzenje, nalikumba,

nagwa m’mbuna yomwe anaikumba.

16 Chovuta chake chidzambwerera mwini,

ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.

17 Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake;

ndipo ndidzaimbira Yehova Wam’mwambamwamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/7-a085905e3182f7625fd62b99645e6371.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 8

Davide aimbira ulemerero wa Mulungu, ndi ulemu umene Mulungu achitira mtundu wa anthu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Gititi. Salimo la Davide.

1 Yehova, Ambuye wathu,

dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!

Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.

2 M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu,

chifukwa cha otsutsana ndi Inu,

kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.

3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu,

mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,

4 munthu ndani kuti mumkumbukira?

Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?

5 Pakuti munamchepsa pang’ono ndi Mulungu,

munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.

6 Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu;

mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;

7 nkhosa ndi ng’ombe, zonsezo,

ndi nyama zakuthengo zomwe;

8 mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja.

Zopita m’njira za m’nyanja.

9 Yehova, Ambuye wathu,

dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/8-827fd393f5e57445a7dc0fb268d8e7a4.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 9

Ayamikira chipulumutso chachikulu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Muti-Labeni. Salimo la Davide.

1 Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse;

ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse.

2 Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu;

ndidzaimbira dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu.

3 Pobwerera m’mbuyo adani anga,

akhumudwa naonongeka pankhope panu.

4 Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga;

mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.

5 Mwadzudzulaamitundu, mwaononga woipayo,

mwafafaniza dzina lao kunthawi yonka muyaya.

6 Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse;

ndipo mizindayo mwaipasula,

chikumbukiro chao pamodzi chatha.

7 Koma Yehova akhala chikhalire,

anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze.

8 Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m’chilungamo,

nadzaweruza anthu molunjika.

9 Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi.

Msanje m’nyengo za nsautso;

10 ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu;

pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.

11 Imbirani zoyamika Yehova, wokhala kuZiyoni;

lalikirani mwa anthu ntchito zake.

12 Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira;

saiwala kulira kwa ozunzika.

13 Ndichitireni chifundo, Yehova;

penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo,

inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.

14 Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse;

pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni,

ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.

15 Amitundu anagwa m’mbuna imene anaikumba,

lakodwa phazi lao muukonde anautchera.

16 Anadziwika Yehova, anachita kuweruza,

woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.

17 Oipawo adzabwerera kumanda,

inde amitundu onse akuiwala Mulungu.

18 Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi,

kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.

19 Ukani, Yehova, asalimbike munthu;

amitundu aweruzidwe pankhope panu.

20 Muwachititse mantha, Yehova;

adziwe amitundu kuti ali anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/9-fffea0a1edf8ea5da8db738c323b4b66.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 10

Athamangira Mulungu pothawa adani omtsata

1 Muimiranji patali, Yehova?

Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?

2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi;

agwe m’chiwembu anapanganacho.

3 Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake,

adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

4 Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira.

Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.

5 Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse;

maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;

adani ake onse awanyodola.

6 Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine;

ku mibadwomibadwo osagwa m’tsoka ine.

7 M’kamwa mwake mwadzala kutemberera

ndi manyengo ndi kuchenjerera;

pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.

8 Akhala m’molalira midzi;

mobisalamo akupha munthu wosachimwa.

Ambisira waumphawi nkhope yake.

9 Alalira monga mkango m’ngaka mwake;

alalira kugwira wozunzika,

agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.

10 Aunthama, nawerama,

ndipo aumphawi agwa m’zala zake.

11 Anena m’mtima mwake, Mulungu waiwala;

wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.

12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;

musaiwale ozunzika.

13 Woipa anyozeranji Mulungu,

anena m’mtima mwake, Simudzafunsira?

14 Mwapenya; pakuti mumayang’anira chivutitso

ndi chisoni kuti achipereke m’manja mwanu;

waumphawi adzipereka kwa Inu;

wamasiye mumakhala mthandizi wake.

15 Thyolani mkono wa woipa;

ndipo wochimwa, mutsate choipa chake

kufikira simuchipezanso china.

16 Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya;

aonongekaamitundum’dziko lake.

17 Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika,

mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;

18 kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,

kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/10-4363149da873ad6239f11877cd226247.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 11

Yehova asunga anthu ake nalanga oipa

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Ndakhulupirira Yehova,

mutani nkunena kwa moyo wanga,

Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?

2 Pakuti, onani, oipa akoka uta,

apiringidza muvi wao pansinga,

kuwaponyera mumdima oongoka mtima.

3 Akapasuka maziko,

wolungama angachitenji?

4 Yehova ali mu Kachisi wake woyera,

Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba;

apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.

5 Yehova ayesa wolungama mtima,

koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.

6 Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa;

moto ndi miyala yasulufure,

ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m’chikho chao.

7 Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama;

woongoka mtima adzapenya nkhope yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/11-6a0cc3d8a7d5d581b3105676a8e68595.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 12

Anthu ndi amabodza, Mulungu ndiye woona

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Seminiti. Salimo la Davide.

1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;

pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.

2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake,

amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.

3 Yehova adzadula milomo yonse yothyasika,

lilime lakudzitamandira;

4 amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;

milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?

5 Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika,

chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi,

ndiuka tsopano, ati Yehova;

ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.

6 Mau a Yehova ndi mau oona;

ngatisilivawoyenga m’ng’anjo yadothi,

yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.

7 Mudzawasunga, Yehova,

mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse.

8 Oipa amayenda mozungulirazungulira,

potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/12-7c5bb2f4a31918aa5895fc65a425fe52.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 13

Munkhawa athawira Mulungu namkhulupirira

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti?

Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?

2 Ndidzachita uphungu m’moyo mwanga kufikira liti,

pokhala ndi chisoni m’mtima mwanga tsiku lonse?

Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?

3 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga.

Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;

4 kuti anganene mdani wanga, Ndamgonjetsa;

ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.

5 Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu;

mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.

6 Ndidzaimbira Yehova,

pakuti anandichitira zokoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/13-9cde76954810ab1f67a49fbbdcdf3261.mp3?version_id=1068—