Categories
YOBU

YOBU 37

1 Pa ichinso mtima wanga unjenjemera,

nusunthika m’malo mwake.

2 Mvetsetsani chibumo cha mau ake,

ndi kugunda kotuluka m’kamwa mwake.

3 Akumveketsa pansi pa thambo ponse,

nang’anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi.

4 Mau abuma kuitsata,

agunda ndi mau a ukulu wake,

ndipo sailetsa atamveka mau ake.

5 Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ake,

achita zazikulu osazidziwa ife.

6 Pakuti anena kwa chipale chofewa, Ugwe padziko,

momwemonso kwa mvula,

ndi kwa mvumbi waukulu.

7 Atsekereza mokhomera chizindikiro dzanja la munthu aliyense,

kuti anthu onse anawalenga adziwe.

8 Pamenepo zilombo zilowa mobisalamo,

ndipo zikhala m’ngaka mwao.

9 M’chipinda mwake mutuluka kamvulumvulu,

ndi chisanu chifuma kumpoto.

10 Mwa kupuma kwake Mulungu apereka chipale,

ndi madzi achitando aundana.

11 Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi,

afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yake;

12 ndipo utembenukatembenuka pakulangiza kwake,

kuti uchite zilizonse aulamulira,

pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu;

13 ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula,

kapena kulichitira chifundo.

14 Tamverani ichi, Yobu.

Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu.

15 Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi,

nawalitsa mphezi ya m’mtambo mwake?

16 Kodi mudziwa madendekeredwe ake a mitambo,

zodabwitsa za Iye wakudziwa mwangwiro?

17 Kodi mudziwa umo zovala zanu zifundira,

pamene dziko lili thuu chifukwa cha mwera?

18 Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye,

ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka?

19 Mutilangize chimene tidzanena ndi Iye;

sitidziwa kulongosola mau athu chifukwa cha mdima.

20 Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena,

kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa?

21 Ndipo tsopano anthu sangathe kupenyerera kuunika

pakunyezimira kuthambo,

ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa.

22 Kuchokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira,

Mulungu ali nao ukulu woopsa.

23 Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule;

ndiye wa mphamvu yoposa;

koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.

24 M’mwemo anthu amuopa,

Iye sasamalira aliyense wanzeru mumtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/37-f2fd93babd3776ddcbe1246e5ad4081f.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 38

Mulungu aonekera kwa Yobu osamtsutsa. Koma amkumbutsa za ukulu wopambana wa Mulungu. Yobu adzichepetsapo

1 Pamenepo Yehova anayankha Yobu m’kamvulumvulu, nati,

2 Ndani uyu adetsa uphungu,

ndi mau opanda nzeru?

3 Udzimangire m’chuuno tsono ngati mwamuna;

ndikufunsa, undidziwitse.

4 Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?

Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.

5 Analemba malire ake ndani, popeza udziwa?

Anayesapo chingwe chake ndani?

6 Maziko ake anakumbidwa pa chiyani?

Kapena anaika ndani mwala wake wa pangodya,

7 muja nyenyezi za m’mawa zinaimba limodzi mokondwera,

ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?

8 Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko,

muja idakamula ngati kutuluka m’mimba,

9 muja ndinayesa mtambo chovala chake,

ndi mdima wa bii nsalu yake yokulunga,

10 ndi kuilembera malire anga,

ndi kuika mipikizo ndi zitseko,

11 ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;

apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?

12 Kodi walamulira m’mawa chiyambire masiku ako,

ndi kudziwitsa mbandakucha malo ake;

13 kuti agwire malekezero a dziko lapansi,

nakutumule oipa achokeko?

14 Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa chosindikiza,

ndi zonse zibuka ngati chovala;

15 ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,

ndi dzanja losamulidwa lithyoledwa.

16 Kodi unalowa magwero a nyanja?

Kodi unayendayenda pozama penipeni?

17 Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe?

Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?

18 Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi?

Fotokozera, ngati uchidziwa chonse.

19 Ili kuti njira yomukira pokhala kuunika?

Ndi mdima, pokhala pake pali kuti,

20 kuti upite nao kumalire ake,

kuti uzindikire miseu ya kunyumba yake?

21 Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo,

ndi masiku ako achuluka kuwerenga kwao.

22 Kodi unalowa m’zosungiramo chipale chofewa?

Kapena unapenya zosungiramo matalala,

23 amene ndiwasungira tsiku la nsautso,

tsiku lakulimbana nkhondo?

24 Njira ili kuti yomukira pogawikana kuunika,

kapena pomwazikira mphepo ya kum’mawa padziko lapansi?

25 Ndani anachikumbira mchera chimvula,

kapena njira ya bingu la mphezi,

26 kuvumbitsa mvula padziko lopanda anthu,

kuchipululu kosakhala munthu,

27 kukhutitsa thengo la kunkhwangwala,

ndi kuphukitsa msipu?

28 Kodi mvula ili naye atate?

Kapena wabala ndani madontho a mame?

29 Chipale chinatuluka m’mimba ya yani?

Ndi chisanu chochokera m’mwamba anachibala ndani?

30 Madzi aundana ngati mwala,

ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.

31 Kodi ungamange gulu la Nsangwe?

Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?

32 Ungatulutse kodi nyenyezi m’nyengo zao

monga mwa malongosoledwe ao?

Kapena kutsogolera Mlalang’amba ndi ana ake?

33 Kodi udziwa malemba a kuthambo?

Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao padziko lapansi?

34 Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo,

kuti madzi ochuluka akukute?

35 Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke,

ndi kunena nawe, Tili pano?

36 Ndani analonga nzeru m’mitambomo?

Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha?

37 Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru,

ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani,

38 pokandika fumbi,

ndi kuundana zibuma pamodzi?

39 Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama?

Ndi kukwaniritsa chakudya cha misona,

40 pamene ibwatama m’ngaka mwao,

nikhala mobisala kulaliramo?

41 Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani,

pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu,

naulukauluka osowa chakudya?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/38-85fe4bf7618f7688a05d4ef8f051fdbf.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 39

1 Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma?

Kodi wapenyerera pakuswa mbawala?

2 Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira,

kapena udziwa nyengo yoti ziswane?

3 Zithuntha, ziswa,

zitaya zowawa zao.

4 Ana ao akhala ojincha, akulira kuthengo,

achoka osabwerera kwa amao.

5 Ndani walola mbidzi ituluke yaufulu?

Anaimasulira mbidzi nsinga zake ndani,

6 imene ndachiyesa chipululu nyumba yake,

ndi dziko lakhulo pokhala pake?

7 Aseka phokoso la kumzinda,

osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m’goli.

8 Poyenda ponse pamapiri mpa busa pake;

ilondola chachiwisi chilichonse.

9 Kodi njati idzavomera kukutumikira,

idzakhala ku chodyetseramo chako kodi?

10 Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lake ilime m’mchera?

Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m’zigwa?

11 Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yake njaikulu?

Udzaisiyira ntchito yako kodi?

12 Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako,

ndi kuzisonkhanitsira kudwale?

13 Phiko la nthiwatiwa likondwera,

koma mapiko ndi nthenga zake nzofatsa kodi?

14 Pakuti isiya mazira ake panthaka,

nimafunditsa m’fumbi,

15 nkuiwala kuti phazi lingawaphwanye,

kapena chilombo chingawapondereze.

16 Iumira mtima ana ake monga ngati sali ake;

idzilemetsa ndi ntchito chabe, popeza ilibe mantha;

17 pakuti Mulungu anaimana nzeru,

ndipo sanaigawire luntha.

18 Ikafika nthawi yake, iweramuka,

iseka kavalo ndi wa pamsana pake.

19 Wampatsa kavalo mphamvu yake kodi?

Wamveka pakhosi pake chenjerere chogwedezeka?

20 Wamlumphitsa kodi ngati dzombe?

Ulemerero wa kumina kwake ngwoopsa.

21 Apalasa kuchigwa, nakondwera nayo mphamvu yake;

atuluka kukomana nao eni zida.

22 Aseka mantha osaopsedwa,

osabwerera kuthawa lupanga.

23 Phodo likuti kochokocho panthiti pake,

mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe.

24 Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka,

osaimitsika pomveka lipenga.

25 Pomveka lipenga akuti, Hee!

Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali,

kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza.

26 Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako,

natambasula mapiko ake kunka kumwera?

27 Kodi chiombankhanga chikwera m’mwamba pochilamulira iwe,

nkumanga chisanja chake m’mwamba?

28 Kwao nkuthanthwe, chigona komweko,

pansonga pa thanthwe pokhazikikapo.

29 Pokhala kumeneko chiyang’ana chakudya;

maso ake achipenyetsetsa chili kutali.

30 Ana ake akumwa mwazi,

ndipo pomwe pali ophedwa, apo pali icho.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/39-4ad684f063e68e8b88bfb17fc474f8a9.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 40

1 Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati,

2 Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?

Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.

3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova nati,

4 Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?

Ndigwira pakamwa.

5 Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;

inde kawiri, koma sindionjezanso.

6 Ndipo Yehova anamyankha Yobu m’kamvulumvulu, nati,

7 Dzimangire m’chuuno tsono ngati mwamuna;

ndidzakufunsa, undidziwitse.

8 Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi?

Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi,

kuti ukhale wolungama ndiwe?

9 Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?

Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?

10 Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika,

nuvale ulemu ndi ulemerero.

11 Tsanulira mkwiyo wako wosefuka,

nupenyerere aliyense wodzikuza ndi kumchepetsa.

12 Upenyerere aliyense wodzikuza, numtsitse,

nupondereze oipa pomwe akhala.

13 Uwakwirire pamodzi m’fumbi,

uzimange nkhope zao pobisika.

14 Pamenepo inenso ndidzakuvomereza,

kuti dzanja lakolako lamanja likupulumutsa.

15 Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe,

ikudya udzu ngati ng’ombe.

16 Tapenya tsono, mphamvu yake ili m’chuuno mwake,

ndi kulimbalimba kwake kuli m’mitsempha ya m’mimba yake.

17 Igwedeza mchira wake ngati mkungudza;

mitsempha ya ntchafu zake ipotana.

18 Mafupa ake akunga misiwe yamkuwa;

ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu.

19 Iyo ndiyo chiyambi cha machitidwe a Mulungu;

wakuilenga anaininkha lupanga lake.

20 Pakuti mapiri aiphukitsira chakudya,

kumene zisewera nyama zonse zakuthengo.

21 Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,

pobisala pabango ndi pathawale.

22 Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao,

misondodzi ya kumtsinje iizinga.

23 Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera;

ilimbika mtima, ngakhale Yordani atupa mpaka pakamwa pake.

24 Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi?

Kapena kuboola m’mphuno mwake ili m’khwekhwe?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/40-1e6529ccf0fa7095a692e8a602fb6a4d.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 41

1 Kodi ukhoza kukokaLeviyatanindi mbedza?

Kapena kukanikiza kalandira wake ndi chingwe?

2 Kodi ukhoza kumanga m’mphuno ndi mlulu?

Kapena kuboola nsagwada wake ndi mbedza?

3 Kodi idzachulukitsa mau akukupembedza?

Kapena idzanena nawe mau ofatsa?

4 Kodi idzapangana ndi iwe,

kuti uitenge ikhale kapolo wako wachikhalire?

5 Kodi udzasewera nayo ngati mbalame?

Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?

6 Kodi opangana malonda adzaitsatsa?

Adzaigawana eni malonda?

7 Kodi udzadzaza khungu lake ndi ntchetho,

kapena mutu wake ndi miomba?

8 Isanjike dzanja lako;

ukakumbukira nkhondoyi, sudzateronso.

9 Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe.

Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?

10 Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.

Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?

11 Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze?

Zilizonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.

12 Sindikhala chete osatchula ziwalo za ng’onayo,

ndi mbiri ya mphamvu yake, ndi makonzedwe ake okoma.

13 Ndani adzasenda chovala chake chakunja?

Adzalowa ndani kumizere iwiri ya mano ake?

14 Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake?

Mano ake aopsa pozungulira pao.

15 Mamba ake olimba ndiwo kudzitama kwake;

amangika pamodzi ngati okomeredwatu.

16 Alumikizana lina ndi linzake,

mphepo yosalowa pakati pao.

17 Amamatirana lina ndi linzake,

agwirana osagawanikana.

18 Pakuyetsemula ing’anipitsa kuunika,

ndi maso ake akunga zikope za m’mawa.

19 M’kamwa mwake mutuluka miuni,

mbaliwali za moto zibukamo.

20 M’mphuno mwake mutuluka utsi,

ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi

21 mpweya wake uyatsa makala,

ndi m’kamwa mwake mutuluka lawi la moto.

22 Kukhosi kwake kukhala mphamvu,

ndi mantha avumbuluka patsogolo pake.

23 Nyama yake yopsapsala igwirana

ikwima pathupi pake yosagwedezeka.

24 Mtima wake ulimba ngati mwala,

inde ulimba ngati mwala wa mphero.

25 Ikanyamuka, amphamvu achita mantha;

chifukwa cha kuopsedwa azimidwa nzeru.

26 Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma;

ngakhale nthungo, kapena muvi, kapena mkondo.

27 Chitsulo ichiyesa phesi,

ndi mkuwa ngati mtengo woola.

28 Muvi suithawitsa,

miyala ya pachoponyera iisandutsa chiputu.

29 Zibonga ziyesedwa chiputu,

iseka kuthikuza kwake kwa nthungo.

30 Kumimba kwake ikunga mapale akuthwa,

itasalala kuthope ngati chopunthira.

31 Ichititsa nthubwinthubwi pozama ngati nkhali,

isanduliza nyanja ikunge mafuta.

32 Ichititsa mifunde yonyezimira pambuyo pake;

munthu akadati pozama pali ndi imvi.

33 Padziko lapansi palibe china cholingana nayo,

cholengedwa chopanda mantha.

34 Ipenya chilichonse chodzikuza,

ndiyo mfumu ya zodzitama zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/41-f9fb380fe6f436d6af11a46c49efd6ed.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 42

Yobu adzichepetsa pamaso pa Mulungu, mabwenziwo adzudzulidwa ndi Mulungu, Yobu apulumutsidwa nadalitsidwanso

1 Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati,

2 Ndidziwa kuti mukhoza kuchita zonse,

ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse.

3 Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu?

Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikire,

zondidabwitsa, zosazidziwa ine.

4 Tamveranitu, ndidzanena ine,

ndidzakufunsani, mundidziwitse.

5 Kumva ndidamva mbiri yanu,

koma tsopano ndikupenyani maso;

6 chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa

m’fumbi ndi mapulusa.

7 Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.

8 Ndipo tsono, mudzitengere ng’ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.

9 Namuka Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, nachita monga Yehova adawauza; ndipo Yehova anavomereza Yobu.

10 Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.

11 Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m’nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide.

12 Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndingamirazikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng’ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu aakazi chikwi chimodzi.

13 Anali naonso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu.

14 Ndipo anamutcha dzina la woyamba Yemima, ndi dzina la wachiwiri Keziya, ndi dzina la wachitatu Kerenihapuki.

15 Ndipo m’dziko monse simunapezeke akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao.

16 Ndipo zitatha izi, Yobu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi mphambu makumi anai, naona ana ake ndi zidzukulu zake mibadwo inai.

17 Namwalira Yobu, wokalamba ndi wa masiku ochuluka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/42-b498856fe6ef03dc6b1b05409a179fba.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Ili ndi buku la nyimbo ndi mapemphero. Mau ake adalembedwa ndi anthu osiyanasiyana pa nthawi yaitali, ndipo Aisraele ankagwiritsa ntchito mauwo popembedza Yehova. Masalimowo alipo amitundumitundu: ena ndi nyimbo zotamanda Mulungu, zopembedza, kapena zothokoza; ena ndi mau opempha chithandizo ndi chitetezo pa nthawi ya mavuto, ena ndi mau olapa ndi opepesera machimo, mau opempha chikhululukiro, mwinanso mau opempha Mulungu kuti alange adani. Masalimowo ngothandiza anthu pakupemphera, aliyense molingana ndi zimene zadzaza mumtima wake, komanso moganizira zosowa za anthu onse a Mulungu ndi ubwino wao. Yesu nayenso ankagwiritsa ntchito Masalimowo popemphera; ndipo kuyambira pa chiyambi cha Mpingo, Akhristu akhala akugwiritsa ntchito buku lomwelo pamwambo wachipembedzo.

Za mkatimu

Bukuli lili ndi zigawo zisanu:

Masalimo 1 mpaka 41

Masalimo 42 mpaka 72

Masalimo 73 mpaka 89

Masalimo 90 mpaka 106

Masalimo 107 mpaka 150

Categories
MASALIMO

MASALIMO 1

Kusiyana pakati pa olungama ndi oipa

1 Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,

kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa,

kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.

2 Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake;

ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.

3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;

wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake,

tsamba lake lomwe losafota;

ndipo zonse azichita apindula nazo.

4 Oipa satero ai;

koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.

5 Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo,

kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.

6 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;

koma mayendedwe a oipa adzatayika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/1-7cc95113bd363644c1c5933efc45eb76.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 2

Ufumu wa wodzozedwa wa Yehova

1 Aphokoseranjiamitundu,

nalingiriranji anthu zopanda pake?

2 Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi,

nachita upo akulu pamodzi,

Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,

3 Tidule zomangira zao,

titaye nsinga zao.

4 Wokhala m’mwambayo adzaseka;

Ambuye adzawanyoza.

5 Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake,

nadzawaopsa mu ukali wake.

6 Koma Ine ndadzoza mfumu yanga

PaZiyoni, phiri langa loyera.

7 Ndidzauza za chitsimikizo:

Yehova ananena ndi Ine,

Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.

8 Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu

akhale cholowa chako,

ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.

9 Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo;

udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.

10 Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru;

langikani, oweruza inu a dziko lapansi.

11 Tumikirani Yehova ndi mantha,

ndipo kondwerani ndi chinthenthe.

12 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye,

ndipo mungatayike m’njira

ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wake.

Odala onse akumkhulupirira Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/2-0cb4e5951d6c2f03d6a79956f669cf45.mp3?version_id=1068—

Categories
MASALIMO

MASALIMO 3

Kukhulupirika kwa Mulungu

Salimo la Davide, muja anathawa Abisalomu mwana wake.

1 Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine!

Akundiukira ine ndi ambiri.

2 Ambiri amati kwa moyo wanga,

alibe chipulumutso mwa Mulungu.

3 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa;

ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.

4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga,

ndipo andiyankha m’phiri lake loyera.

5 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;

ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.

6 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.

7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!

Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;

mwawathyola mano oipawo.

8 Chipulumutso ncha Yehova;

dalitso lanu likhale pa anthu anu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/3-60f1eca1f3eec23e92384018de71d6bc.mp3?version_id=1068—