Categories
YOBU

YOBU 27

Yobu adzikaniza nanenetsa kuti ochimwa ambiri akhala osalangidwa. Ena ali ndi nzeru ndi chuma, koma opanda nzeru yeniyeni

1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,

2 Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine,

ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,

3 pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,

ndi mpweya wa Mulungu m’mphuno mwanga;

4 milomo yanga siilankhula chosalungama,

ndi lilime langa silitchula zachinyengo.

5 Sindivomereza konse kuti muli olungama;

mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.

6 Ndiumirira chilungamo changa, osachileka;

chikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.

7 Mdani wanga akhale ngati woipa,

ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.

8 Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu,

pomchotsera moyo wake?

9 Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso?

10 Kodi adzadzikondweretsa naye Wamphamvuyonse,

ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?

11 Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;

chokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzachibisa.

12 Taonani, inu nonse munachiona;

ndipo mugwidwa nazo zopanda pake chifukwa ninji?

13 Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu,

ndi cholowa cha akupsinja anzao achilandira kwa Wamphamvuyonse.

14 Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga,

ndi ana ake sadzakhuta chakudya.

15 Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,

ndi akazi ake amasiye sadzalira maliro.

16 Chinkana akundika ndalama ngati fumbi,

ndi kukonzeratu zovala ngati dothi;

17 azikonzeretu, koma wolungama adzazivala,

ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.

18 Amanga nyumba yake ngati kangaude,

ndi ngati wolindira amanga dindiro.

19 Agona pansi ali wachuma, koma saikidwa;

potsegula maso ake, wafa chikomo.

20 Zoopsa zimgwera ngati madzi;

nkuntho umtenga usiku.

21 Mphepo ya kum’mawa imtenga, nachoka iye;

nimkankha achoke m’malo mwake.

22 Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osamleka;

kuthawa akadathawa m’dzanja lake.

23 Anthu adzamuombera manja,

nadzamuimbira mluzu achoke m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/27-bd63e4d17d63827b5beea54c88b61219.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 28

1 Koma kuli mtapo wasiliva,

ndi malo a golide amene amuyenga.

2 Chitsulo achitenga m’nthaka,

ndi mkuwa ausungunula kumwala.

3 Munthu athawitsa mdima,

nafunafuna mpaka malekezero onse,

miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.

4 Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;

aiwalika ndi phazi lopitapo;

apachikika kutali ndi anthu, nalendewalendewa.

5 Kunena za nthaka, kuchokera momwemo mumatuluka chakudya,

ndi m’munsi mwake musandulizika ngati ndi moto.

6 Miyala yake ndiyo malo a safiro,

ndipo ili nalo fumbi lagolide.

7 Njira imeneyi palibe chiombankhanga chiidziwa;

lingakhale diso la kabawi losapenyapo.

8 Nyama zodzikuza sizinapondapo,

ngakhale mkango waukali sunapitapo.

9 Munthu atambasulira dzanja lake kumwala;

agubuduza mapiri kuyambira kumizu.

10 Asema njira pakati pa matanthwe,

ndi diso lake liona chilichonse cha mtengo wake.

11 Atseka mitsinje ingadonthe;

natulutsira poyera chobisikachi.

12 Koma nzeru, idzapezeka kuti?

Ndi luntha, malo ake ali kuti?

13 Munthu sadziwa mtengo wake;

ndipo silipezeka m’dziko la amoyo.

14 Pozama pakuti, Mwa ine mulibe;

ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.

15 Silipezeka ndi golide,

sayesapo siliva mtengo wake.

16 Sailinganiza ndi golide wa Ofiri,

ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro.

17 Golide ndi krustalo sizilingana nayo;

ndi kusinthana kwake,

siisinthanika ndi zisambiro za golide woyengetsa.

18 Korali kapena ngale sizikumbukikapo.

Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira.

19 Topazi wa Kusi sufanana nayo,

sailinganiza ndi golide wolongosoka.

20 Koma nzeru ifuma kuti?

Ndi luntha, pokhala pake pali kuti?

21 Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,

pabisikiranso mbalame za m’mlengalenga.

22 Chionongeko ndi Imfa zikuti,

Tamva mbiri yake m’makutu mwathu.

23 Mulungu ndiye azindikira njira yake,

ndiye adziwa pokhala pake.

24 Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,

naona pansi pa thambo ponse;

25 pamene anaikira mphepo muyeso wake,

nayesera madzi miyeso;

26 pakuchitira mvula lamulo,

ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;

27 pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;

anaikonza, naisanthula.

28 Koma kwa munthu anati,

Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;

ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/28-e038ea55e9281f6c3929e8f7b1f4b24b.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 29

Yobu alinganiza chikhalidwe chake chakale ndi tsoka latsopano, nalimbika kuti sanachite zotchulidwazi

1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,

2 Ha! Ndikadakhala monga m’miyezi yapitayi,

monga m’masiku akundisunga Mulungu;

3 muja nyali yake inawala pamutu panga,

ndipo ndi kuunika kwake ndinayenda mumdima;

4 monga umo ndinakhala m’masiku anga olimba,

muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga.

5 Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi,

ndi ana anga anandizinga;

6 muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka,

ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona!

7 Muja ndinatuluka kunka kuchipata kumzinda,

muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,

8 anyamata anandiona nabisala,

okalamba anandinyamukira, nakhala chilili.

9 Akalonga anadziletsa kulankhula,

ndi kugwira pakamwa pao;

10 mau a omveka anali zii,

ndi lilime lao linamamatira kumalakalaka ao.

11 Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa;

ndipo pondiona diso, linandichitira umboni.

12 Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakufuula;

mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.

13 Dalitso la iye akati atayike linandidzera,

ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera.

14 Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine;

chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.

15 Ndinali maso a akhungu,

ndi mapazi a otsimphina.

16 Ndinali atate wa waumphawi;

ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.

17 Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama,

ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.

18 Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m’chisa changa;

ndipo ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.

19 Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;

ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.

20 Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine,

ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m’dzanja mwanga.

21 Anthu anandimvera, nalindira,

nakhala chete, kuti ndiwapangire.

22 Nditanena mau anga sanalankhulenso,

ndi kunena kwanga kunawakhera.

23 Anandilindira ngati kulindira mvula,

nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.

24 Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima;

ndipo sanagwetse kusangalala kwa nkhope yanga.

25 Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkulu wao.

Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ake,

ngati wotonthoza ofedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/29-61687a8946ef1c110c43364a7f10869e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 30

1 Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka,

iwo amene atate ao ndikadawapeputsa,

osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.

2 Mphamvunso ya m’manja mwao ndikadapindulanji nayo?

Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha,

3 atsala mafupa okhaokha ndi kusowa ndi njala;

akungudza nthaka youma kuli mdima wa m’chipululu chopasuka.

4 Atchera therere lokolera kuzitsamba,

ndi chakudya chao ndicho mizu ya dinde.

5 Anawapirikitsa pakati pa anthu,

awafuulira ngati kutsata mbala.

6 Azikhala m’zigwa za chizirezire,

m’maenje a m’nthaka ndi m’mapanga.

7 Pakati pa zitsamba alira ngati bulu,

pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.

8 Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;

anawaingitsa kuwachotsa m’dziko.

9 Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo,

nandiyesa chitonzo.

10 Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine,

saleka kuthira malovu pankhope panga.

11 Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza;

anataya chomangira m’kamwa mwao pamaso panga.

12 Kudzanja langa lamanja anauka oluluka,

akankha mapazi anga,

andiundira njira zao zakundiononga.

13 Aipsa njira yanga,

athandizana ndi tsoka langa;

ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.

14 Akudza ngati opitira pogamuka linga papakulu,

pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine.

15 Anditembenuzira zondiopsa,

auluza ulemu wanga ngati mphepo;

ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.

16 Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m’kati mwanga;

masiku akuzunza andigwira.

17 Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine,

ndi zowawa zondikungudza sizipuma.

18 Mwa mphamvu yaikulu ya nthenda yanga

chovala changa chinasandulika,

chindithina ngati pakhosi pa malaya anga.

19 Iye anandiponya m’matope,

ndipo ndafanana ndi fumbi ndi phulusa.

20 Ndifuula kwa Inu, koma simundiyankha;

ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.

21 Mwasandulika kundichitira nkharwe;

ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.

22 Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo;

ndipo mundisungunula mumkuntho.

23 Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,

ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.

24 Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lake kodi?

Akati aonongeke, safuulako kodi?

25 Kodi sindinamlirire misozi wakulawa zowawa?

Kodi moyo wanga sunachitire chisoni osowa?

26 Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa,

ndipo polindira kuunika unadza mdima.

27 M’kati mwanga mupweteka mosapuma,

masiku a mazunzo andidzera.

28 Ndiyenda ndili wothimbirira osati ndi dzuwa ai;

ndinyamuka mumsonkhano ndi kufuula.

29 Ndili mbale wao wa ankhandwe,

ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.

30 Khungu langa lada, nilindifundukira;

ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.

31 Chifukwa chake zeze wanga wasandulika wa maliro,

ndi chitoliro changa cha mau a olira misozi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/30-67d2b39b09e0b82ceb31f255ca7e2ec1.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 31

1 Ndinapangana ndi maso anga,

potero ndipenyerenji namwali?

2 Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba,

ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m’mwambamo nchiyani?

3 Si ndizo chionongeko cha wosalungama,

ndi tsoka la ochita mphulupulu?

4 Nanga sapenya njira zanga,

ndi kuwerenga moponda mwanga monse?

5 Ngati ndinayanjana nalo bodza,

ndi phazi langa linathamangira chinyengo;

6 andiyese ndi muyeso wolingana,

kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.

7 Ngati phazi langa linapatuka m’njira,

ndi mtima wanga unatsata maso anga?

Ngati chilema chamamatira manja anga?

8 Ndibzale ine nadye wina,

ndi zondimerera ine zizulidwe.

9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,

ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,

10 mkazi wanga aperere wina;

wina namuike kumbuyo.

11 Pakuti icho ndi choipitsitsa,

ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.

12 Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko,

ndi chakuzula zipatso zanga zonse.

13 Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga,

kapena wa mdzakazi wanga,

potsutsana nane iwo,

14 ndidzatani ponyamuka Mulungu?

Ndipo pondizonda Iye ndidzamnyankha chiyani?

15 Kodi Iye amene anandilenga ine m’mimba

sanamlenge iyenso?

Sindiye mmodzi anatiumba m’mimba?

16 Ngati ndakaniza aumphawi chifuniro chao,

kapena kutopetsa maso a amasiye,

17 kapena kudya nthongo yanga ndekha,

osadyako mwana wamasiye;

18 (pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa

ndi ine monga ndi atate;

ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.)

19 Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda chovala,

kapena kuti wosowa alibe chofunda;

20 ngati ziuno zake sizinandiyamike,

ngati sanafunde ubweya wa nkhosa zanga;

21 ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,

popeza ndinaona thandizo langa kuchipata;

22 libanthuke phewa langa paphalo,

ndi dzanja langa liduke pagwangwa.

23 Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa,

ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.

24 Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa,

ndi kunena ndi golide woyengetsa,

ndiwe chikhazikitso changa;

25 ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu,

ndi dzanja langa lapeza zochuluka;

26 ngati ndalambira dzuwa lilikuwala,

kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;

27 ndi mtima wanga wakopeka m’tseri,

ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;

28 ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza

kunena mlandu wake;

pakuti ndikadakana Mulungu ali m’mwamba.

29 Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,

kapena kudzitukula pompeza choipa;

30 ndithu sindinalole m’kamwa mwanga muchimwe,

kupempha motemberera moyo wake.

31 Ngati amuna a m’hema mwanga sanati,

ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?

32 Mlendo sakagona pakhwalala,

koma ndinatsegulira wam’njira pakhomo panga.

33 Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu,

ndi kubisa mphulupulu yanga m’chifuwa mwanga;

34 popeza ndinaopa unyinji waukulu,

ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa;

potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga.

35 Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera,

chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe;

mwenzi ntakhala nao mau akundineneza

analemberawo mdani wanga!

36 Ndithu ndikadawasenza paphewa panga,

ndi kudzimangirira awa ngati korona.

37 Ndikadamfotokozera chiwerengo cha mopondamo mwanga,

ndikadamsenderera Iye ngati kalonga.

38 Ngati minda yanga ifuula monditsutsa,

ndi nthumbira zake zilira pamodzi;

39 ngati ndadya zipatso zake wopanda ndalama.

Kapena kutayitsa eni ake moyo wao;

40 imere minga m’malo mwa tirigu,

ndi dawi m’malo mwa barele.

Mau a Yobu atha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/31-b4d82b61b735a2c350eea6591b10e9dd.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 32

Elihu adzudzula Yobu ndi mabwenzi atatu omwe

1 Pamenepo amuna atatuwa analeka kumyankha Yobu; pakuti anali wolungama pamaso pake pa iye mwini.

2 Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.

3 Adapsa mtima pa mabwenzi ake atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.

4 Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.

5 Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.

6 Ndipo Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi anayankha, nati,

Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba;

chifukwa chake ndinadziletsa,

ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.

7 Ndinati, Amisinkhu anene,

ndi a zaka zochuluka alangize nzeru.

8 Koma m’munthu muli mzimu,

ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.

9 Akulu sindiwo eni nzeru,

ndi okalamba sindiwo ozindikira chiweruzo.

10 Chifukwa chake ndinati, Ndimvereni ine,

inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine.

11 Taonani, ndinalindira mau anu,

ndinatcherera khutu zifukwa zanu,

pofunafuna inu ponena.

12 Inde ndinasamalira inu;

koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu,

kapena wakumbwezera mau pakati pa inu.

13 Msamati, Tapeza nzeru ndife,

Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai;

14 popeza sanandiponyere ine mau,

sindidzamyankha ndi maneno anu.

15 Asumwa, sayankhanso, Anawathera mau.

16 Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo,

popeza akhala duu osayankhanso?

17 Ndidzayankha inenso mau anga,

ndidzaonetsa inenso za m’mtima mwanga.

18 Pakuti ndadzazidwa ndi mau,

ndi mzimu wa m’kati mwanga undifulumiza.

19 Taonani, m’chifuwa mwanga muli ngati vinyo

wosowa popungulira,

ngati matumba atsopano akuti aphulike.

20 Ndidzanena kuti chifundo chitsike;

ndidzatsegula milomo yanga ndi kuyankha.

21 Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu,

kapena kumtchula munthu maina omdyola nao;

22 pakuti sindidziwa kutchula maina osyasyalika;

ndikatero Mlengi wanga adzandichotsa msanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/32-00656da0cdf0bdca941ec0d2efa0b7e0.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 33

Elihu atsutsa Yobu pa kudzikuza kwake, nanenetsa kuti pomlanga munthu Mulungu ali nacho chifukwa

1 Komatu, Yobu, mumvere maneno anga,

mutcherere khutu mau anga.

2 Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga,

lilime langa lanena m’kamwa mwanga.

3 Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga,

ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.

4 Mzimu wa Mulungu unandilenga,

ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.

5 Ngati mukhoza, mundiyankhe;

mulongosolere mau anu pamaso panga, mukonzeke.

6 Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu;

inenso ndinaumbidwa ndi dothi.

7 Taonani, kuopsa kwanga simudzachita nako mantha;

ndi ichi ndikusenzetsani sichidzakulemererani.

8 Zedi mwanena m’makutu mwanga,

ndinamvanso mau a kunena kwanu, akuti,

9 Ndine woyera ine, wopanda kulakwa,

ndine wosapalamula, ndilibe mphulupulu.

10 Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo,

andiyesa mdani wake;

11 amanga mapazi anga m’zigologolo,

ayang’anira poyenda ine ponse.

12 Taonani, ndidzakuyankhani m’mene muli mosalungama;

pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.

13 Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji?

Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.

14 Pakuti Mulungu alankhula kamodzi,

kapena kawiri, koma anthu sasamalira.

15 M’kulota, m’masomphenya a usiku,

pakuwagwera anthu tulo tatikulu,

pogona mwatcheru pakama,

16 pamenepo atsegula makutu a anthu,

nakomera chizindikiro chilangizo chao;

17 kuti achotse munthu ku chimene akadachita,

ndi kubisira munthu kudzikuza kwake;

18 kuti amletse angaonongeke,

ndi moyo wake ungatayike ndi lupanga.

19 Alangidwanso ndi zowawa pakama pake,

ndi kulimbana kowawa kosapuma m’mafupa ake.

20 M’mwemo mtima wake uchita mseru ndi mkate,

ndi moyo wake pa chakudya cholongosoka.

21 Mnofu wake udatha, kuti sungapenyeke;

ndi mafupa ake akusaoneka atuluka.

22 Inde wasendera kufupi kumanda,

ndi moyo wake kwa akuononga.

23 Akakhala kwa iye mthenga,

womasulira mau mmodzi mwa chikwi,

kuonetsera munthu chomuyenera;

24 pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati,

Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo.

25 Mnofu wake udzakhala see, woposa wa mwana;

adzabwerera kumasiku a ubwana wake.

26 Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima;

m’mwemo aona nkhope yake mokondwera;

ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.

27 Apenyerera anthu, ndi kuti,

ndinachimwa, ndaipsa choongokacho,

ndipo sindinapindule nako.

28 Koma anandiombola ndingatsikire kumanda,

ndi moyo wanga udzaona kuunika.

29 Taona, izi zonse azichita Mulungu

kawiri katatu ndi munthu,

30 kumbweza angalowe kumanda,

kuti kuunika kwa moyo kumuwalire.

31 Tcherani khutu, Yobu, mundimvere ine;

mukhale chete, ndipo ndidzanena ine.

32 Ngati muli nao mau mundiyankhe.

Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani.

33 Ngati mulibe mau, tamverani ine;

mukhale chete, ndipo ndidzakuphunzitsani nzeru.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/33-6d6dabdb298b36f1bc7033bc043ed9ef.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 34

Elihu anenetsa Mulungu sangathe kukhala wosalungama, koma asiyanitsa pakati pa okoma ndi oipa

1 Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,

2 Tamverani mau anga, inu anzeru;

munditcherere khutu inu akudziwa.

3 Pakuti khutu liyesa mau,

monga m’kamwa mulawa chakudya.

4 Tidzisankhire choyeneracho,

tidziwe mwa tokha chokomacho.

5 Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,

ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine

6 Kodi ndidzinamizire?

Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwe.

7 Wakunga Yobu ndani,

wakumwa mwano ngati madzi?

8 Wakutsagana nao ochita mphulupulu,

nayendayenda nao anthu oipa.

9 Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako

kuvomerezana naye Mulungu.

10 Chifukwa chake mundimvere ine, eni nzeru inu,

nkutali ndi Mulungu kuchita choipa,

ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.

11 Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake,

napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake.

12 Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa,

ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.

13 Anamuikiza dziko lapansi ndani?

Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?

14 Akadzikumbukira yekha mumtima mwake,

akadzisonkhanitsira yekha mzimu wake ndi mpweya wake,

15 zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,

ndi munthu adzabwerera kufumbi.

16 Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ichi,

Tcherera khutu kunena kwanga.

17 Kodi munthu woipidwa nacho chiweruzo adzalamulira?

Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?

18 Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pake iwe,

kapena kwa akalonga, Oipa inu?

19 Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga,

wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka?

Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.

20 M’kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku,

anthu agwedezeka, napita,

amphamvu achotsedwa opanda dzanja lakuwachotsa.

21 Pakuti maso ake ali panjira ya munthu aliyense,

napenya moponda mwake monse.

22 Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa,

kuti ochita zopanda pake abisaleko.

23 Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu,

kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa.

24 Aphwanya eni mphamvu osatulutsa kubwalo mlandu wao,

naika ena m’malo mwao.

25 Pakuti asamalira ntchito zao,

nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.

26 Awakantha ngati oipa,

poyera pamaso pa anthu,

27 popeza anapatuka, naleka kumtsata,

osasamalira njira zake zilizonse.

28 M’mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka;

ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika.

29 Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani?

Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani?

Chikachitika pa mtundu wa anthu,

kapena pa munthu, nchimodzimodzi;

30 kuti munthu wonyoza Mulungu asachite ufumu,

ndi anthu asakodwe mumsampha.

31 Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu,

ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwe?

32 Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu,

ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.

33 Kodi chilango cha Mulungu chikhale

monga muchifuna inu, pakuti muchikana?

Musankhe ndi inu, ine ai;

m’mwemo monga mudziwa, nenani.

34 Anthu ozindikira adzanena nane,

inde anthu anzeru onse akundimva adzati,

35 Yobu alankhula wopanda kudziwa,

ndi mau ake alibe nzeru.

36 Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha,

chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu.

37 Pakuti pa kuchimwa kwake aonjeza kupikisana ndi Mulungu,

asansa manja pakati pa ife,

nachulukitsa maneno ake pa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/34-6b3962972c96bad768116d55d4bd9aa8.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 35

Elihu akuti kwa Mulungu kulibe chifukwa cha kuchita tsankho

1 Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,

2 Kodi muchiyesa choyenera,

umo mukuti, Chilungamo changa chiposa cha Mulungu,

3 pakuti munena, Upindulanji nacho?

Posachimwa ndinapindula chiyani

chimene sindikadapindula pochimwa?

4 Ndidzakuyankhani,

ndi anzanu pamodzi ndi inu.

5 Yang’anani kumwamba, nimuone,

tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.

6 Ngati mwachimwa, mumchitira Iye chiyani?

Zikachuluka zolakwa zanu, mumchitira Iye chiyani?

7 Mukakhala wolungama, mumninkhapo chiyani?

Kapena alandira chiyani padzanja lanu?

8 Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu,

ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.

9 Chifukwa cha kuchuluka masautso anthu anafuula,

afuula chifukwa cha dzanja la amphamvu.

10 Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga,

wakupatsa nyimbo usiku;

11 wakutilangiza ife koposa nyama za padziko,

wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m’mlengalenga?

12 Apo afuula, koma Iye sawayankha;

chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oipa.

13 Zedi Mulungu samvera zachabe,

ndi Wamphamvuyonse sazisamalira.

14 Inde mungakhale munena, Sindimpenya,

mlanduwo uli pamaso pake, ndipo mumlindira.

15 Ndipo tsopano popeza analibe kumzonda m’kukwiya kwake,

ndi kusamalitsa cholakwa,

16 chifukwa chake Yobu anatsegula pakamwa pake mwachabe,

nachulukitsa mau opanda nzeru.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/35-8525ccbd64b59ac863d97c2d28d2f81b.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 36

Elihu alemekeza chilungamo ndi mphamvu ya Mulungu. Mulungu ndi wangwiro, ife tilephera kumdziwa

1 Elihu anabwereza, nati,

2 Mundilole pang’ono, ndidzakuuzani,

pakuti ndili naonso mau akunenera Mulungu.

3 Ndidzatenga nzeru zanga kutali,

ndidzavomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama.

4 Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza,

wakudziwitsa mwangwiro ali nanu.

5 Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu,

ndipo sapeputsa munthu;

mphamvu ya nzeru zake ndi yaikulu.

6 Sasunga woipa akhale ndi moyo,

koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo.

7 Sawachotsera wolungama maso ake,

koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao

awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.

8 Ndipo akamangidwa m’nsinga,

nakakodwa ndi zingwe za mazunzo,

9 pamenepo awafotokozera ntchito zao,

ndi zolakwa zao, kuti anachita modzikuza.

10 Awatseguliranso m’khutu mwao kuti awalangize,

nawauza abwerere kuleka mphulupulu.

11 Akamvera ndi kumtumikira,

adzatsiriza masiku ao modala,

ndi zaka zao mokondwera.

12 Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga,

nadzatsirizika osadziwa kanthu.

13 Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo,

akawamanga Iye, safuulira.

14 Iwowa akufa akali biriwiri,

ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.

15 Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwake,

nawatsegulira m’khutu mwao mwa kupsinjika kwao.

16 Inde akadakukopani muchoke posaukira,

mulowe kuchitando kopanda chopsinja;

ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.

17 Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa,

zolingirirazo ndi chiweruzo zidzakugwiranibe.

18 Pakuti muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo;

ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.

19 Chuma chanu chidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,

kapena mphamvu yanu yonse yolimba?

20 Musakhumbe usiku,

umene anthu alikhidwe m’malo mwao.

21 Chenjerani, musalunjike kumphulupulu;

pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22 Taonani, Mulungu achita mokwezeka mu mphamvu yake,

mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23 Anamuikira njira yake ndani?

Adzati ndani, Mwachita chosalungama?

24 Kumbukirani kuti mukuze ntchito zake

zimene anaziimbira anthu.

25 Anthu onse azipenyerera,

anthu aziyang’anira kutali.

26 Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa;

chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.

27 Pakuti akweza madontho a mvula,

akhetsa mvula ya m’nkhungu yake

28 imene mitambo itsanulira,

nivumbitsira anthu mochuluka.

29 Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo,

ndi kugunda kwa msasa wake?

30 Taonani, Iye ayala kuunika kwake pamenepo.

Navundikira kunsi kwake kwa nyanja.

31 Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu

apatsa chakudya chochuluka.

32 Akutidwa manja ake ndi mphezi,

nailamulira igwere pofunapo Iye.

33 Kugunda kwake kulalikira za Iye,

zoweta zomwe zilota mtambo woyandikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/36-1c16f54b203c3f942c688ddc1bba0cc8.mp3?version_id=1068—