Categories
YOBU

YOBU 17

1 Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika,

kumanda kwandikonzekeratu.

2 Zoonadi, ali nane ondiseka;

ndi diso langa lili chipenyere m’kundiwindula kwao.

3 Mupatse chigwiriro tsono,

mundikhalire chikole Inu nokha kwanu;

ndani adzapangana nane kundilipirira?

4 Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;

chifukwa chake simudzawakuza.

5 Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo,

m’maso mwa ana ake mudzada.

6 Anandiyesanso chitonzo cha anthu;

ndipo ndakhala ngati munthu womthira malovu pankhope pake.

7 M’diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni,

ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi.

8 Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho,

ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.

9 Koma wolungama asungitsa njira yake,

ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.

10 Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;

pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.

11 Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,

zakezake zomwe za mtima wanga.

12 Zisanduliza usiku ukhale usana;

kuunika kuyandikana ndi mdima.

13 Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;

ndikayala pogona panga mumdima.

14 Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;

kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;

15 chilikuti chiyembekezo changa?

Inde, chiyembekezo changa adzachiona ndani?

16 Chidzatsikira kumipingiridzo ya kumanda,

pamene tipumulira pamodzi kufumbi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/17-b338533e7f587ecaf82cea33fff5c062.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 18

Bilidadi atsutsa Yobu pa kudzikuza kwake, nanena za tsoka la oipa

1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,

2 Musaka mau kufikira liti?

Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.

3 Tiyesedwa bwanji ngati nyama zakuthengo,

ndi kukhala odetsedwa pamaso panu?

4 Iwe wodzing’amba mumkwiyo mwako,

kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe?

Kapena thanthwe lisunthike m’malo mwake?

5 Inde, kuunika kwa woipa kudzazima,

ndi lawi la moto wake silidzawala.

6 Kuunikaku kudzada m’hema mwake,

ndi nyali yake ya pamwamba pake idzazima.

7 Mapondedwe ake amphamvu adzasautsidwa,

ndi uphungu wakewake udzamgwetsa.

8 Pakuti aponyedwa mu ukonde ndi mapazi ake,

namaponda pamatanda.

9 Msampha udzamgwira kuchitendeni,

ndi khwekhwe lidzamkola.

10 Msampha woponda umbisikira pansi,

ndi msampha wa chipeto panjira.

11 Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo,

nadzampirikitsa kumbuyo kwake.

12 Njala idzatha mphamvu yake,

ndi tsoka lidzamkonzekeratu pambali pake.

13 Zidzatha ziwalo za thupi lake,

mwana woyamba wa imfa adzatha ziwalo zake.

14 Adzazulidwa kuhema kwake kumene anakhulupirira;

nadzatengedwa kunka naye kwa mfumu ya zoopsa.

15 Adzakhala m’hema mwake iwo amene sali ake;

miyala yasulufureidzawazika pokhala pake.

16 Mizu yake idzauma pansi,

ndi nthambi yake idzafota m’mwamba.

17 Chikumbukiro chake chidzatayika m’dziko,

ndipo adzasowa dzina kukhwalala.

18 Adzamkankha achoke kukuunika alowe kumdima;

adzampirikitsa achoke m’dziko lokhalamo anthu.

19 Sadzakhala naye mwana kapena chidzukulu

mwa anthu a mtundu wake,

kapena wina wotsalira kumene anakhalako.

20 Akudza m’mbuyo adzadabwa nalo tsiku lake,

monga aja omtsogolera anagwidwa mantha.

21 Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero,

ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/18-2872a6bcfc7f6d87ff987c4c91ec1b4e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 19

Yobu atchulira mabwenzi ake matsoka ake, napempha amchitire chifundo. Adzitonthoza ndi Mpulumutsi wake

1 Koma Yobu anayankha, nati,

2 Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti,

ndi kundithyolathyola nao mau?

3 Kakhumi aka mwandichititsa manyazi;

mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.

4 Ndipo ngati ndalakwa ndithu,

kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.

5 Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,

ndi kunditchulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao.

6 Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,

nandizinga ndi ukonde wake.

7 Taonani, ndifuula kuti, Chiwawa! Koma sandimvera;

ndikuwa, koma palibe chiweruzo.

8 Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,

naika mdima poyendapo ine.

9 Anandivula ulemerero wanga,

nandichotsera korona pamutu panga.

10 Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;

nachizula chiyembekezo changa ngati mtengo.

11 Wandiyatsiranso mkwiyo wake,

nandiyesera ngati wina wa adani ake.

12 Ankhondo ake andidzera pamodzi, nandiundira njira yao,

nandimangira misasa pozinga hema wanga.

13 Iye anandichotsera abale anga kutali,

ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.

14 Anansi anga andisowa,

ndi odziwana nane bwino andiiwala.

15 Iwo a m’nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo;

ndine wachilendo pamaso pao.

16 Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau,

chinkana ndimpembedza pakamwa panga.

17 Mpweya wanga unyansira mkazi wanga,

chinkana ndinampembedza ndi kutchula ana a thupi langa.

18 Angakhale ana aang’ono andipeputsa,

ndikanyamuka, andinena;

19 mabwenzi anga enieni onse anyansidwa nane;

ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.

20 Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga,

ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.

21 Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu;

pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.

22 Mundilondola bwanji ngati Mulungu,

losakukwanirani thupi langa?

23 Ha! Akadalembedwa mau anga!

Ha! Akadalembedwa m’buku!

24 Akadawazokota pathanthwe chikhalire,

ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu!

25 Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo,

nadzauka potsiriza pafumbi.

26 Ndipo khungu langa litaonongeka,

pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu,

27 amene ndidzampenya ndekha,

ndi maso anga adzamuona, si wina ai.

Imso zanga zatha m’kati mwanga.

28 Mukati, Tiyeni timlondole!

Popeza chifukwa cha mlandu chapezeka mwa ine;

29 muchite nalo mantha lupanga;

pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga,

kuti mudziwe pali chiweruzo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/19-a97e6e764d67158b755f3690a23fa43c.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 20

Zofari afotokozera masautso amene Mulungu atumizira oipa

1 Pamenepo anayankha Zofari Mnaama, nati,

2 M’mwemo zolingirira zanga zindiyankha,

chifukwa chake ndifulumidwa m’kati mwanga.

3 Ndamva kudzudzula kwakundichititsa manyazi,

ndi mzimu wa nzeru yanga undiyankha.

4 Kodi suchidziwa ichi chiyambire kale lomwe,

kuyambira anaika munthu padziko lapansi,

5 kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha,

ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?

6 Chinkana ukulu wake ukwera kunka kuthambo,

nugunda pamitambo mutu wake;

7 koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zake;

iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?

8 Adzauluka ngati loto, osapezekanso;

nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.

9 Diso lidamuonalo silidzamuonanso;

ndi malo ake sadzampenyanso.

10 Ana ake adzapempha aumphawi awakomere mtima;

ndi manja ake adzabweza chuma chake.

11 Mafupa ake adzala nao unyamata wake,

koma udzagona naye pansi m’fumbi.

12 Chinkana choipa chizuna m’kamwa mwake,

chinkana achibisa pansi pa lilime lake;

13 chinkana achisunga, osachileka,

nachikhalitsa m’kamwa mwake;

14 koma chakudya chake chidzasandulika m’matumbo mwake,

chidzakhala ndulu ya mphiri m’kati mwake.

15 Anachimeza chuma koma adzachisanzanso;

Mulungu adzachitulutsa m’mimba mwake.

16 Adzayamwa ndulu ya mphiri;

pakamwa pa njoka padzamupha.

17 Sadzapenyerera timitsinje,

toyenda nao uchi ndi mafuta.

18 Chimene adagwiriracho ntchito, adzachibweza, osachimeza;

sadzakondwera monga mwa zolemera zake adaziona.

19 Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi;

analanda nyumba mwachiwawa, imene sanaimange.

20 Popeza sanadziwe kupumula m’kati mwake,

sadzalanditsa kanthu ka zofunika zake.

21 Sikunatsalira kanthu kosadya iye,

chifukwa chake zokoma zake sizidzakhalitsa.

22 Pomkwanira kudzala kwake adzakhala m’kusauka;

dzanja la yense wovutika lidzamgwera.

23 Poti adzaze mimba yake,

Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali,

nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.

24 Adzathawa chida chachitsulo,

ndi muvi wa uta wamkuwa udzampyoza.

25 Auzula, nutuluka m’thupi mwake;

inde nsonga yonyezimira ituluka m’ndulu mwake;

zamgwera zoopsa.

26 Zamdima zonse zimsungikira zikhale chuma chake,

moto wosaukoleza munthu udzampsereza;

udzatha wotsalira m’hema mwake.

27 M’mwamba mudzavumbulutsa mphulupulu yake,

ndi dziko lapansi lidzamuukira.

28 Phindu la m’nyumba mwake lidzachoka,

akatundu ake adzamthawa tsiku la mkwiyo wake.

29 Ili ndi gawo la munthu woipa, lochokera kwa Mulungu,

ndi cholowa amuikiratu Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/20-749c414de1a2b9df99f584fdf38a538e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 21

Yobu ayankha kuti oipa ambiri amalemerera. Zooneka m’maso sizitiuza za mtima wa Mulungu

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Mvetsetsani mau anga;

ndi ichi chikhale chitonthozo chanu.

3 Mundilole, ndinene nanenso;

ndipo nditanena ine, sekani.

4 Kodi ine, kudandaula kwanga, ndidandaulira munthu?

Ndipo ndilekerenji kupsa mtima?

5 Ndiyang’anireni, nimusumwe,

gwirani pakamwa panu.

6 Ndikangokumbukira ndivutika mtima,

ndi thupi langa lichita nyaunyau.

7 Oipa akhaliranji ndi moyo,

nakalamba, nalemera kwakukulu?

8 Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao,

ndi ana ao pamaso pao.

9 Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha,

ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.

10 Ng’ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika;

ng’ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza.

11 Atulutsa makanda ao ngati gulu,

ndi ana ao amavinavina.

12 Aimbira lingaka ndi zeze,

nakondwera pomveka chitoliro.

13 Atsekereza masiku ao ndi zokoma,

natsikira m’kamphindi kumanda.

14 Koma adati kwa Mulungu, Tichokereni;

pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.

15 Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?

Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16 Taonani, zokoma zao sizili m’dzanja lao;

(koma uphungu wa oipa unditalikira.)

17 Ngati nyali za oipa zizimidwa kawirikawiri?

Ngati tsoka lao liwagwera?

Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wake?

18 Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo,

ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?

19 Mukuti, Mulungu asungira ana ake a munthu choipa chake,

ambwezere munthuyo kuti achidziwe.

20 Aone yekha chionongeko chake m’maso mwake,

namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.

21 Pakuti chomsamalitsa nyumba yake nchiyani, atapita iye,

chiwerengo cha miyezi yake chitadulidwa pakati?

22 Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru?

Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.

23 Wina akufa, wabiriwiri,

ali chikhalire ndi chipumulire.

24 Mbale zake zidzala ndi mkaka;

ndi wongo wa m’mafupa ake uli momwe.

25 Koma mnzake akufa ali nao mtima wakuwawa,

osalawa chokoma konse.

26 Iwo agona chimodzimodzi kufumbi,

ndi mphutsi ziwakuta.

27 Taonani, ndidziwa maganizo anu,

ndi chiwembu mundilingirira moipa.

28 Pakuti munena, Ili kuti nyumba ya kalonga?

Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti?

29 Simunawafunsa kodi opita m’njira?

Ndipo simusamalira zotsimikiza zao?

30 Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka?

Natulutsidwa tsiku la mkwiyo?

31 Adzamfotokozera ndani njira yake pamaso pake?

Nadzamlipitsa ndani pa ichi anachichita?

32 Potsiriza pake adzapita naye kumanda,

nadzadikira pamanda pake.

33 Zibuma za kuchigwa zidzamkomera.

Adzakoka anthu onse amtsate,

monga anamtsogolera osawerengeka.

34 Potero munditonthozeranji nazo zopanda pake,

popeza m’mayankho mwanu mutsala mabodza okha?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/21-111450dd7ce8b948d17130bcf97f6156.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 22

Elifazi amtchulira Yobu zoipa zambiri, namuuza alape, Mulungu nadzamchitira chifundo

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Kodi munthu apindulira Mulungu?

Koma wanzeru angodzipindulira yekha.

3 Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako

kuti iwe ndiwe wolungama?

Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

4 Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu,

chifukwa cha kumuopa kwako?

5 Zoipa zako sizichuluka kodi?

Ndi mphulupulu zako sizikhala zosawerengeka kodi?

6 Pakuti wamtenga chikole kwa mbale wako wopanda chifukwa,

ndi kuvula ausiwa zovala zao.

7 Sunampatsa wolema madzi amwe,

ndi wanjala unammana chakudya.

8 Koma munthu mwini mphamvu, dziko ndi lake;

ndi munthu wovomerezeka, anakhala momwemo.

9 Unabweza akazi amasiye osawaninkha kanthu,

ndi manja a ana amasiye anathyoledwa.

10 Chifukwa chake misampha ikuzinga.

Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa,

11 kapena mdima kuti ungaone,

ndi madzi aunyinji akumiza.

12 Kodi Mulungu sakhala m’mwamba m’tali?

Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m’talitali.

13 Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu?

Aweruza kodi mwa mdima wa bii?

14 Mitambo ndiyo chomphimba, kuti angaone;

ndipo amayenda pa thambo lakumwamba.

15 Udzasunga kodi njira yakale,

anaiponda anthu amphulupulu?

16 Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,

chigumula chinakokolola kuzika kwao;

17 amene anati kwa Mulungu, Tichokereni;

ndipo, Angatichitire chiyani Wamphamvuyonse?

18 Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;

koma uphungu wa oipa unditalikira.

19 Olungama achiona nakondwera;

ndi osalakwa awaseka pwepwete,

20 ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,

ndi zowatsalira, moto unazipsereza.

21 Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;

ukatero zokoma zidzakudzera.

22 Landira tsono chilamulo pakamwa pake,

nuwasunge maneno ake mumtima mwako.

23 Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino;

ukachotsera chosalungama kutali kwa mahema ako.

24 Ndipo utaye chuma chako kufumbi,

ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje.

25 Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala chuma chako,

ndi ndalama zako zofunika.

26 Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse,

ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

27 Udzampemphera ndipo adzakumvera;

nudzatsiriza zowinda zako.

28 Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe;

ndi kuunika kudzawala panjira zako.

29 Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza;

ndipo adzapulumutsa wodzichepetsayo.

30 Adzamasula ngakhale wopalamula,

inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/22-0c8eaf0ad4df2bd7f5ecabd45970a9c9.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 23

Yobu abwereza kukana kuti sanachimwe. Mulungu wosadziwika achita chifuniro chake. Kwambiri ochimwa oyenera kulangidwa akhala bwino m’moyo uno

1 Koma Yobu anayankha, nati,

2 Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;

kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m’kulemera kwake.

3 Ha! Ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,

kuti ndifike kumpando wake!

4 Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pake,

ndikadadzaza m’kamwa mwanga ndi matsutsano.

5 Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,

ndikadazindikira chimene akadanena nane.

6 Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yake yaikulu?

Iai, koma akadanditcherera khutu.

7 Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;

ndipo ndikadapulumuka chipulumukire kwa Woweruza wanga.

8 Taonani, ndikanka m’tsogolo, kulibe Iye;

kapena m’mbuyo sindimzindikira;

9 akachita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;

akabisala kulamanja, sindimuona.

10 Koma adziwa njira ndilowayi;

atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.

11 Phazi langa lagwiratu moponda Iye,

ndasunga njira yake, wosapatukamo.

12 Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake;

ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.

13 Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?

Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.

14 Pakuti adzachita chondiikidwiratu;

ndipo zambiri zotere zili ndi Iye.

15 Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake;

ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye.

16 Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,

ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.

17 Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo,

ndipo sanandiphimbire nkhope yanga ndi mdima wa bii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/23-19fdf6c1cbf04aed83d4155c5d4aa7c3.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 24

1 Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?

Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?

2 Alipo akusendeza malire;

alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.

3 Akankhizira kwao bulu wa amasiye,

atenga ng’ombe ya mfedwa ikhale chikole.

4 Apatukitsa aumphawi m’njira;

osauka a padziko abisala pamodzi.

5 Taonani, ngati mbidzi za m’chipululu

atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya;

chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.

6 Atema dzinthu zao m’munda;

natola khunkha m’munda wampesa wa woipa.

7 Agona amaliseche usiku wonse opanda chovala,

alibe chofunda pachisanu.

8 Avumbwa ndi mvula kumapiri,

nafukata thanthwe posowa pousapo.

9 Akwatula wamasiye kubere,

natenga chikole chovala cha osauka;

10 momwemo ayenda amaliseche opanda chovala,

nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.

11 M’kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;

aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.

12 M’mzinda waukulu anthu abuula alinkufa;

ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula;

koma Mulungu sasamalira choipacho.

13 Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,

sadziwa njira zake, Sasunga mayendedwe ake.

14 Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;

ndi usiku asanduka mbala.

15 Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira,

ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;

navala chophimba pankhope pake.

16 Kuli mdima aboola nyumba,

usana adzitsekera,

osadziwa kuunika.

17 Pakuti iwo onse auyesa m’mawa mthunzi wa imfa;

pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.

18 Atengedwa ngati choyandama pamadzi;

gawo lao litembereredwa padziko;

sadzalunjikanso njira ya minda yampesa.

19 Chilala ndi dzuwa zitha madzi a chipale chofewa,

momwemo manda achita nao ochimwa.

20 M’mimba mudzamuiwala;

mphutsi zidzamudya mokondwera.

Sadzamkumbukiranso;

ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo.

21 Alusira chumba wosabala,

osamchitira wamasiye chokoma.

22 Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake;

iwo aukanso m’mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.

23 Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo;

koma maso ake ali panjira zao.

24 Akwezeka; m’kamphindi kuli zii;

inde atsitsidwa, achotsedwa monga ena onse,

adulidwa ngati tirigu ngala zake.

25 Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza,

ndi kuyesa mau anga opanda pake?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/24-0ebef2528ceab784f33c50d5003ebd31.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 25

Bilidadi akuti munthu sayenera kudziyesa wolungama pamaso pa Mulungu

1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,

2 Kulamulira ndi kuopsa kuli ndi Iye;

achita mtendere pa zam’mwamba zake.

3 Ngati awerengedwa makamu ake?

Ndipo ndaniyo, kuunika kwake sikumtulukira?

4 Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?

Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?

5 Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala;

ndi nyenyezi siziyera pamaso pake;

6 kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi!

Ndi wobadwa ndi munthu, ndiye nyongolotsi!

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/25-f6bb25ba6efb11ddaf8650d6fe9dea13.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 26

Yobu atsutsa Bilidadi kuti sanamthandize; yekha nalemekeza ukulu wa Mulungu

1 Koma Yobu anayankha, nati,

2 Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu.

Kulipulumutsa dzanja losalimba!

3 Wampangira bwanji wopanda nzeruyu!

Ndi kudziwitsa nzeru zenizeni mochuluka!

4 Wafotokozera yani mau?

Ndi mzimu wa yani unatuluka mwa iwe?

5 Adafawo anjenjemera

pansi pamadzi ndi zokhalamo.

6 Kumanda kuli padagu pamaso pake,

ndi kuchionongeko kusowa chophimbako.

7 Ayala kumpoto popanda kanthu,

nalenjeka dziko pachabe.

8 Amanga madzi m’mitambo yake yochindikira;

ndi mtambo sung’ambika pansi pake.

9 Atchingira pa mpando wake wachifumu,

nayalapo mtambo wake.

10 Analembera madziwo malire,

mpaka polekeza kuunika ndi mdima.

11 Mizati ya thambo injenjemera,

ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.

12 Mwa mphamvu yake agwetsa nyanja bata;

ndipo mwa luntha lake akantha kudzikuza kwake.

13 Mwa mzimu wake anyezimiritsa thambo;

dzanja lake linapyoza njoka yothawayo.

14 Taonani, awa ndi malekezero a njira zake;

ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong’onezo chaching’ono;

koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/26-db742895a2bb224dcb871d6449c6d54e.mp3?version_id=1068—