Categories
YOBU

YOBU 7

1 Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno?

Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?

2 Monga kapolo woliralira mthunzi,

monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,

3 momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake.

Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.

4 Ndigona pansi, ndikuti,

Ndidzauka liti? Koma usiku undikulira;

ndipo ndimapalapata mpaka mbandakucha.

5 Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi;

khungu langa lang’ambika, nilinyansa.

6 Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,

apitirira opanda chiyembekezo.

7 Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo,

diso langa silidzaonanso chokoma.

8 Diso la amene andiona silidzandionanso,

maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.

9 Mtambo wapita watha,

momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.

10 Sadzabweranso kunyumba yake,

osamdziwanso malo ake.

11 Potero sindidzaletsa pakamwa panga;

ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga;

ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.

12 Ndine nyanja kodi, kapena chinjoka cha m’nyanja,

kuti Inu mundiikira odikira?

13 Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,

pogona panga padzachepsa chondidandaulitsa;

14 pamenepo mundiopsa ndi maloto,

nimundichititsa mantha ndi masomphenya;

15 potero moyo wanga usankha kupotedwa,

ndi imfa, koposa mafupa anga awa.

16 Ndinyansidwa nao moyo wanga;

sindidzakhala ndi moyo chikhalire;

mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.

17 Munthu ndani kuti mumkuze,

ndi kuti muike mtima wanu pa iye,

18 ndi kuti mucheze naye m’mawa ndi m’mawa,

ndi kumuyesa nthawi zonse?

19 Mukana kundichokera kufikira liti,

kapena kundileka mpaka nditameza dovu?

20 Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani,

Inu wodikira anthu?

Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu?

Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?

21 Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga

ndi kundichotsera mphulupulu yanga?

Popeza tsopano ndidzagona kufumbi;

mudzandifunafuna, koma ine palibe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/7-733b988db546a25ec801104bdc4ae2fc.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 8

Poona tsoka lao Bilidadi akuti Yobu ndi ana ake anachimwa, anena mofanizira

1 Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,

2 Udzanena izi kufikira liti?

Ndipo mau a pakamwa pako

adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

3 Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo?

Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?

4 Chinkana ana ako anamchimwira Iye,

ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;

5 koma ukafunitsitsa Mulungu,

ndi kupembedza Wamphamvuyonse;

6 ukakhala woyera ndi woongoka mtima,

zoonadi adzakugalamukira tsopano,

ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.

7 Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching’ono,

chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.

8 Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo,

nusamalire zimene makolo ao adazisanthula.

9 Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,

popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10 amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,

ndi kutulutsa mau a mumtima mwao?

11 Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho?

Ngati manchedza amera popanda madzi?

12 Akali auwisi, sanawacheke,

auma, asanaume mathengo onse ena.

13 Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;

ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.

14 Kulimbika mtima kwake kudzathyoka,

chikhulupiriro chake chikunga nyumba ya kangaude.

15 Adzatsamira nyumba yake, koma yosamlimbira;

adzaiumirira koma yosakhalitsa.

16 Akhala wamuwisi pali dzuwa,

ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake.

17 Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi,

apenyerera pokhalapo miyala.

18 Akamuononga kumchotsa pamalo pake,

padzamkana, ndi kuti, Sindinakuone.

19 Taona, ichi ndicho chomkondweretsa panjira pake,

ndi panthaka padzamera ena.

20 Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro;

kapena kugwiriziza ochita zoipa.

21 Koma adzadzaza m’kamwa mwako ndi kuseka,

ndi milomo yako kufuula.

22 Iwo akudana nawe adzavala manyazi;

ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/8-cc0837d44517aafd54c6f9308f29da7c.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 9

Yobu avomereza ukulu wa Mulungu, koma okoma ndi oipa alangidwa mmodzimmodzi. Masautso ake amfunitsa kufa

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Zoona, ndidziwa kuti chili chotero.

Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu?

3 Akafuna Iye kutsutsana naye,

sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi.

4 Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu;

ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?

5 Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo,

amene amagubuduza mu mkwiyo wake.

6 Amene agwedeza dziko lapansi lichoke m’malo mwake,

ndi mizati yake injenjemere.

7 Amene alamulira dzuwa ndipo silituluka,

nakomera nyenyezi chizindikiro chakuzitsekera.

8 Woyala thambo yekha,

naponda pa mafunde a panyanja.

9 Wolenga Mlalang’amba, Akamwiniatsatana,

ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita.

10 Wochita zazikulu zosasanthulika,

ndi zodabwitsa zosawerengeka.

11 Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya;

napitirira, koma osamzindikira ine.

12 Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani?

Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?

13 Mulungu sadzabweza mkwiyo wake;

athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.

14 Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji,

ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?

15 Ameneyo, chinkana ndikadakhala wolungama,

sindikadamyankha;

ndikadangompembedza wondiweruza ine.

16 Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye,

koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.

17 Pakuti andithyola ndi mkuntho,

nachulukitsa mabala anga kopanda chifukwa.

18 Sandilola kuti ndipume,

koma andidzaza ndi zowawa.

19 Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu?

Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?

20 Chinkana ndikhala wolungama,

pakamwa panga padzanditsutsa;

chinkana ndikhala wangwiro,

padzanditsutsa wamphulupulu.

21 Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini,

ndipeputsa moyo wanga.

22 Kuli chimodzimodzi monsemo, m’mwemo ndikuti

Iye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.

23 Mkwapulo ukapha modzidzimutsa,

adzaseka tsoka la wosachimwa.

24 Dziko lapansi laperekedwa m’dzanja la woipa;

aphimba maso a oweruza ake.

Ngati sindiye, pali yaninso?

25 Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma;

athawa osaona chokoma.

26 Apitirira ngati zombo zaliwiro;

ngati mphungu igudukira chakudya chake.

27 Ndikati, Ndidzaiwala chondidandaulitsa,

ndidzasintha nkhope yanga yachisoni, ndidzasekerera.

28 Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse,

ndidziwa kuti simudzandiyesa wosachimwa.

29 Mlandu udzanditsutsa;

potero ndigwire ntchito chabe chifukwa ninji?

30 Ndikasamba madzi a chipale chofewa

ndi kuyeretsa manja anga ndi sopo.

31 Mudzandiviikanso muli zoola,

ndi zovala zanga zidzanyansidwa nane.

32 Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe.

Kuti tikomane mlandu.

33 Palibe wakutiweruza,

wakutisanjika ife tonse awiri manja ake.

34 Andichotsere ndodo yake,

choopsa chake chisandichititse mantha;

35 kuti ndinene, osamuopa,

pakuti sinditero monga umo ndili.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/9-c084b770067fd667d80b53bd6ef70365.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 10

1 Mtima wanga ulema nao moyo wanga,

ndidzadzilolera kudandaula kwanga,

ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.

2 Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse;

mundidziwitse chifukwa cha kutsutsana nane.

3 Chikukomerani kodi kungosautsa,

kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu,

ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?

4 Muli nao maso a thupi kodi?

Mupenya kodi monga umo apenyera munthu?

5 Masiku anu akunga masiku a munthu kodi,

zaka zanu zikunga masiku a munthu;

6 kuti mufunsa mphulupulu yanga,

ndi kulondola choipa changa;

7 chinkana mudziwa kuti sindili woipa,

ndipo palibe wakupulumutsa m’dzanja lanu?

8 Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu,

koma mufuna kundiononga.

9 Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi;

ndipo kodi mudzandibwezera kufumbi?

10 Simunanditsanule kodi ngati mkaka,

ndi kundilimbitsa ngati mase?

11 Munandiveka khungu ndi mnofu,

ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha.

12 Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima,

ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.

13 Koma izi munazibisa mumtima mwanu;

ndidziwa kuti ichi muli nacho.

14 Ndikachimwa mundipenya;

ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.

15 Ndikakhala woipa, tsoka ine;

ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutu wanga;

ndadzazidwa ndi manyazi,

koma penyani kuzunzika kwanga.

16 Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango;

mubweranso ndi kudzionetsera modabwitsa kwa ine.

17 Mundikonzeranso mboni zonditsutsa,

ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu;

nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.

18 Potero munandibadwitsa chifukwa ninji?

Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso.

19 Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala;

akadanditenga pobadwapo kunka nane kumanda.

20 Masiku anga satsala owerengeka nanga? Lindani.

Bandilekani kuti nditsitsimuke pang’ono,

21 ndisanachoke kunka kumene sindikabweranso,

ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa.

22 Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani,

dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka,

kumene kuunika kukunga mdima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/10-ce34da4f829e5495004bd59a6b8c1687.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 11

Zofari adzudzula Yobu pa kudzilungamitsa kwake, namchenjeza alape

1 Pamenepo anayankha Zofari wa ku Naama, nati,

2 Kodi mau ochulukawa sayenera kuwayankha?

Ndi munthu wa milomo ayenera kuyesedwa wolungama?

3 Kodi zotamanda zako ziwatseke anthu pakamwa?

Useka kodi, wopanda munthu wakukuchititsapo manyazi?

4 Pakuti unena, Chiphunzitso changa nchoona,

ndipo ndili woyera pamaso pako.

5 Koma, ha? Mwenzi atanena Mulungu,

ndi kukutsegulira milomo yake motsutsa;

6 nakufotokozere zinsinsi za nzeru,

popeza zipindikapindika machitidwe ao!

Chifukwa chake dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina.

7 Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna?

Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?

8 Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji?

Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?

9 Muyeso wake utalikira utali wake wa dziko lapansi,

chitando chake chiposa cha nyanja.

10 Akapita, nakatsekera,

nakatulutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?

11 Pakuti adziwa anthu opanda pake,

napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira.

12 Koma munthu wopanda pake asowa nzeru,

ngakhale munthu abadwa ngati mwanawabulu.

13 Ukakonzeratu mtima wako,

ndi kumtambasulira Iye manja ako;

14 Mukakhala mphulupulu m’dzanja lako, uichotseretu kutali,

ndi chisalungamo chisakhale m’mahema mwako.

15 Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga;

nudzalimbika osachita mantha;

16 pakuti udzaiwala chisoni chako,

udzachikumbukira ngati madzi opita.

17 Ndipo moyo wako udzayera koposa usana;

kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m’mawa.

18 Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo;

nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.

19 Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa,

ndipo ambiri adzakupembedza.

20 Koma maso a oipa adzagoma,

ndi pothawirapo padzawasowa,

ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/11-26d69c25d7343eef21a294904e13e96c.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 12

Yobu avomerezanso ukulu wa Mulungu, koma mau a abwenziwo ndi opanda pake; nanena za moyo wa munthu ukutha msanga

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Zoonadi inu ndinu anthu,

ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.

3 Koma inenso ndili nayo nzeru monga inu.

Sindingakuchepereni;

ndani sadziwa zonga izi?

4 Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake,

ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;

munthu wolungama wangwiro asekedwa.

5 Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwake,

limlindira woterereka mapazi ake.

6 Mahema a achifwamba akhala mumtendere,

ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima;

amene Mulungu amadzazira dzanja lao.

7 Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,

ndi mbalame za m’mlengalenga, zidzakuuza.

8 Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;

ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera.

9 Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;

kuti dzanja la Yehova lichita ichi?

10 M’dzanja mwake muli mpweya wa zamoyo zonse,

ndi mzimu wa munthu aliyense.

11 M’khutumu simuyesa mau,

monga m’kamwa mulawa chakudya chake?

12 Kwa okalamba kuli nzeru,

ndi kwa a masiku ochuluka luntha.

13 Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu;

uphungu ndi luntha ali nazo.

14 Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso;

amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira.

15 Taona atsekera madzi, naphwa;

awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.

16 Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru.

Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ake.

17 Apita nao maphungu atawafunkhira,

napulukiritsa oweruza milandu.

18 Amasula chomangira cha mafumu,

nawamangira nsinga m’chuuno mwao.

19 Apita nao, ansembe atawafunkhira,

nagubuduza amphamvu.

20 Amchotsera wokhulupirika kunena kwake.

Nalanda luntha la akulu.

21 Atsanulira mnyozo pa akalonga,

nawansezera olimba lamba lao.

22 Avumbulutsa zozama mumdima,

natulutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;

23 achulukitsaamitundu, nawaononganso;

abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.

24 Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao,

nawasokeretsa m’chipululu chopanda njira.

25 Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika,

ndipo awayendetsa dzandidzandi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/12-3adde100b71ca5970876427d6f6c0b18.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 13

1 Taonani, diso langa lachiona chonsechi;

m’khutu mwanga ndachimva ndi kuchizindikira.

2 Chimene muchidziwa inu, inenso ndichidziwa;

sindikucheperani.

3 Koma ine ndidzanena ndi Wamphamvuyonse,

ndipo ndifuna kudzikanira kwa Mulungu.

4 Koma inu ndinu opanga zabodza,

asing’anga opanda pake inu nonse.

5 Mwenzi mutakhala chete konse,

ndiko kukadakhala nzeru zanu.

6 Tamvani tsono kudzikanira kwanga,

tamverani kudzinenera kwa milomo yanga.

7 Kodi munenera Mulungu mosalungama,

ndi kumnenera Iye monyenga?

8 Kodi mukhalira kumodzi ndi Iye?

Kodi mungamuimilire Mulungu pa mlandu?

9 Nchokoma kodi kuti Iye akusanthuleni?

Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu?

10 Adzakudzudzulani ndithu,

mukachita tsankho m’tseri.

11 Ukulu wake sukuchititsani mantha,

ndi kuopsa kwake sikukugwerani kodi?

12 Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa;

zodzikanira zanu zikunga malinga adothi.

13 Khalani chete, ndilekeni, kuti ndinene,

chondifikira chifike.

14 Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga,

ndi kupereka moyo wanga m’dzanja langa?

15 Angakhale andipha koma ndidzamlindira;

komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.

16 Iye adzakhalanso chipulumutso changa,

pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pake.

17 Mvetsetsani mau anga,

ndi kunenetsa kwanga kumveke m’makutu mwanu.

18 Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;

ndidziwa kuti adzandimasula ndili wolungama.

19 Ndaniyo adzatsutsana nane?

Ndikakhala chete, ndidzapereka mzimu wanga.

20 Zinthu ziwiri zokha musandichitire,

pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu.

21 Mundichotsere dzanja lanu kutali,

ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha.

22 Pamenepo muitane, ndipo ndidzayankha;

kapena ndinene ndine, ndipo mundiyankhe ndinu.

23 Mphulupulu zanga ndi zochimwa zanga ndi zingati?

Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi tchimo langa.

24 Mubisiranji nkhope yanu,

ndi kundiyesa mdani wanu?

25 Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka,

ndi kulondola ziputu zouma?

26 Pakuti mundilembera zinthu zowawa,

ndi kundipatsa ngati cholowa mphulupulu za ubwana wanga.

27 Mulonganso mapazi anga m’zigologolo,

ndi kupenyerera mayendedwe anga onse;

mudzilembera malire mopanika mapazi anga.

28 Momwemo munthu akutha ngati chinthu choola,

ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/13-ff29d48737c0c4e2fe0efe0563e5ffcb.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 14

1 Munthu wobadwa ndi mkazi

ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.

2 Atuluka ngati duwa, nafota;

athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.

3 Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo,

ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu?

4 Adzatulutsa choyera m’chinthu chodetsa ndani?

Nnena mmodzi yense.

5 Popeza masiku ake alembedwa,

chiwerengo cha miyezi yake chikhala ndi Inu,

ndipo mwamlembera malire ake kuti asapitirirepo iye;

6 mumleke osamthira maso, kuti apumule,

kuti akondwere nalo tsiku lake monga wolembedwa ntchito.

7 Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso,

ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasowa.

8 Ngakhale muzu wake wakalamba m’nthaka,

ndi tsinde lake likufa pansi.

9 Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka,

nudzaswa nthambi ngati womera.

10 Koma munthu akufa atachita liondeonde

inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?

11 Madzi achoka m’nyanja,

ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;

12 momwemo munthu agona pansi, osaukanso;

kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,

kapena kuutsidwa pa tulo take.

13 Ha? Mukadandibisa kumanda,

mukadandisunga m’tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.

Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.

14 Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?

Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,

mpaka kwafika kusandulika kwanga.

15 Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;

mukadakhumba ntchito ya manja anu.

16 Koma tsopano muwerenga moponda mwanga;

kodi simuyang’anitsa tchimo langa?

17 Cholakwa changa chaikidwa m’thumba lokhomedwa chizindikiro;

ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.

18 Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;

ndi thanthwe lisunthika m’malo mwake.

19 Madzi anyenya miyala;

zosefukira zao zikokolola fumbi la nthaka;

ndipo muononga chiyembekezo cha munthu.

20 Mumpambana kotheratu, napita iye;

musintha nkhope yake, mumuuza achoke.

21 Ana ake aona ulemu osadziwa iye;

napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.

22 Koma thupi lake limuwawira yekha,

ndi mtima wake umliritsa yekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/14-05bb4dcdc6001c5feb27e4be78431419.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 15

Elifazi atsutsa Yobu pa kudzikuza kwake. Akuti, akulu omwe atsimikiza kuti ochimwa sakhala bwino

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika,

ndi kudzaza mimba yake ndi mphepo ya kum’mawa?

3 Kodi atsutsane ndi mnzake ndi mau akusathandiza?

Kapena ndi maneno akusapindulitsa?

4 Zedi uyesa chabe mantha,

nuchepsa chilingiriro pamaso pa Mulungu.

5 Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako,

nusankha lilime la ochenjerera.

6 Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai.

Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.

7 Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?

Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?

8 Kodi unamva uphungu wachinsinsi wa Mulungu?

Ndipo unadzikokera nzeru kodi?

9 Udziwa chiyani, osachidziwa ife?

Uzindikira chiyani, chosakhala mwa ife?

10 Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa,

akuposa atate wako masiku ao.

11 Masangalatso a Mulungu akuchepera kodi?

Kapena uli nacho chinsinsi kodi?

12 Mtima wako usonthokeranji nawe?

Maso ako aphethiraphethira chifukwa ninji?

13 Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu,

ndi kulola mau otere atuluke m’kamwa mwako.

14 Munthu nchiyani kuti akhale woyera,

wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?

15 Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake;

ngakhale m’mwamba simuyera pamaso pake.

16 Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa,

wakumwa chosalungama ngati madzi.

17 Ndidzakuonetsa, undimvere;

chimene ndinachiona, ndidzakufotokozera;

18 chimene adachinena anzeru,

adachilandira kwa makolo ao, osachibisa;

19 ndiwo amene analandira okha dzikoli,

wosapita mlendo pakati pao.

20 Munthu woipa adzipweteka masiku ake onse,

ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.

21 M’makutu mwake mumveka zoopsetsa;

pali mtendere amfikira wakumuononga.

22 Sakhulupirira kuti adzatulukamo mumdima,

koma kuti lupanga limlindira.

23 Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti?

Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima.

24 Nsautso ndi chipsinjo zimchititsa mantha,

zimgonjetsa ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo.

25 Pakuti amtambasula dzanja lake moyambana ndi Mulungu,

napikisana ndi Wamphamvuyonse.

26 Amthamangira Iye mwaliuma,

ndi zikopa zake zochindikira.

27 Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake,

nachita mafunyenye a mafuta m’zuuno zake;

28 adzakhala m’mizinda yopasuka,

m’nyumba zosakhalamo munthu,

zoti zisandulika muunda.

29 Sadzakhala wolemera, ndi chuma chake sichidzakhalitsa,

ndi zipatso zake sizidzachuluka padziko.

30 Sadzachoka mumdima;

lawi la moto lidzaumitsa nthambi zake;

ndipo adzachoka ndi mpumo wa m’kamwa mwake.

31 Asatame zopanda pake, kudzinyenga nazo;

pakuti zopanda pake zidzakhala chombwezera chake.

32 Chidzachitika isanadze nthawi yake;

pakuti nthambi yake siidzaphuka.

33 Adzayoyoka zipatso zake zosapsa ngati mpesa,

nadzathothoka maluwa ake ngati mtengo waazitona.

34 Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala chumba,

ndi moto udzapsereza mahema a olandira chokometsera mlandu.

35 Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu,

ndi m’mimba mwao mukonzeratu chinyengo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/15-055e69e0a0493deaf497831e7675052e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 16

Yobu atonza mabwenziwo kuti mau ao samthandiza, akana kuti sanachimwe, nadziponya kwa Mulungu. Chiyembekezo chake ndi imfa

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Ndamva zambiri zotere;

inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa.

3 Kodi adzatha mau ouluzika?

Kapena chikuwindula nchiyani kuti uyankha zotere?

4 Inenso ndikadanena monga inu,

moyo wanu ukadakhala m’malo mwa moyo wanga,

ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu,

ndi kukupukusirani mutu wanga.

5 Koma ndikadakulimbikitsani ndi m’kamwa mwanga,

ndi chitonthozo cha milomo yanga chikadatsitsa chisoni chanu.

6 Chinkana ndinena chisoni changa sichitsika;

ndipo ndikaleka, chindichokera nchiyani?

7 Koma tsopano wandilemetsa Iye;

mwapasula msonkhano wanga wonse.

8 Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa,

kuonda kwanga kundiukira, kuchita umboni pamaso panga.

9 Iye ananding’amba m’kundida kwake, nakwiya nane,

anandikukutira mano;

mdani wanga ananditong’olera maso ake.

10 Iwo anandiyasamira pakamwa pao;

anandiomba pama ndi kunditonza;

asonkhana pamodzi kunditsutsa.

11 Mulungu andipereka kwa osulangama,

nandiponya m’manja a oipa.

12 Ndinali mkupuma, koma anandithyola;

inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya;

nandiimika ndikhale chandamali.

13 Eni mauta ake andizinga,

ang’amba impso zanga, osazileka;

natsanulira pansi ndulu yanga.

14 Andipasulapasula;

andithamangira ngati wamphamvu.

15 Ndadzisokerera chiguduli kukhungu langa.

Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m’fumbi.

16 Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi,

ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa;

17 pangakhale palibe chiwawa m’manja mwanga,

ndi pemphero langa ndi loyera.

18 Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga,

ndi kulira kwanga kusowe popumira.

19 Tsopanonso, taona, mboni yanga ili kumwamba,

ndi nkhoswe yanga ikhala m’mwamba.

20 Mabwenzi anga andinyoza;

koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu.

21 Ha? Munthu akadapembedzera mnzake kwa Mulungu,

monga munthu apembedzera mnansi wake!

22 Pakuti zitafika zaka zowerengeka,

ndidzamuka kunjira imene sindibwererako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/16-f78bde1bc7b47e1c85e13075d13dd839.mp3?version_id=1068—