Categories
ESTERE

ESTERE 8

Ahasuwero avomereza pempho la Estere, Ayuda napulumuka

1 Tsiku lomwelo mfumu Ahasuwero anampatsa mkazi wamkulu Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda. Nafika Mordekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za chibale chake.

2 Ndipo mfumu inavula mphete yake adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Mordekai. Ndi Estere anaika Mordekai akhale woyang’anira nyumba ya Hamani.

3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda.

4 Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.

5 Nati, Chikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, ndi kumuyenera mfumu, ngatinso ndimchititsa kaso, alembe makalata kusintha mau a chiwembu cha Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m’maiko onse a mfumu;

6 pakuti ndidzapirira bwanji pakuchiona choipa chilikudzera a mtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuchiona chionongeko cha fuko langa?

7 Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.

8 Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m’dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata yolembedwa m’dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kuyisintha.

9 Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.

10 Ndipo analembera m’dzina la mfumu Ahasuwero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza makalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro achifumu, obadwa mosankhika;

11 m’menemo mfumu inalola Ayuda okhala mu mzinda uliwonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ao aang’ono, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,

12 tsiku lomwelo, m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.

13 Chitsanzo chake, cha lemboli, chakuti abukitse lamulo m’maiko onse, chinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera chilango adani ao.

14 Natuluka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro achifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m’chinyumba cha ku Susa.

15 Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mzinda wa Susa unafuula ndi kukondwera.

16 Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi chimwemwe, ndi ulemu.

17 Ndi m’maiko monse, ndi m’mizinda yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m’dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/8-9660cb13c0716d9bd2b13721bc40e932.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 9

Ayuda awapha adani ao

1 Mwezi wakhumi ndi chiwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, mau a mfumu ndi lamulo lake ali pafupi kuchitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwachitira ufumu, koma chinasinthika; popeza Ayuda anachitira ufumu iwo odana nao;

2 pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m’mizinda mwao, m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.

3 Ndipo akalonga onse a maikowo, ndi akazembe, ndi ziwanga, ndi iwo ochita ntchito ya mfumu, anathandiza Ayuda; popeza kuopsa kwa Mordekai kudawagwera.

4 Pakuti Mordekai anali wamkulu m’nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m’maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.

5 Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna.

6 Ndipo m’chinyumba cha ku Susa Ayuda anakantha, naononga amuna mazana asanu.

7 Napha Parasadata, ndi Dalifoni, ndi Asipata,

8 ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata,

9 ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaizata,

10 ana aamuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande zofunkha.

11 Tsiku lomwelo anabwera nacho kwa mfumu chiwerengo cha iwo ophedwa m’chinyumba cha ku Susa.

12 Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m’chinyumba cha ku Susa, ndi ana aamuna khumi a Hamani; nanga m’maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika.

13 Nati Estere, Chikakomera mfumu, alole Ayuda okhala mu Susa achite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana aamuna khumi a Hamani apachikidwe pamtengo.

14 Ndipo mfumu inati azichita motero, nalamulira mu Susa, napachikidwa ana aamuna khumi a Hamani.

15 Ndipo Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu mu Susa; koma sanalande zofunkha.

16 Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m’maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalande zofunkha.

17 Chinachitika ichi tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana tsiku lakhumi ndi chitatu ndi lakhumi ndi chinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi chisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19 Chifukwa chake Ayuda a kumidzi, okhala m’mizinda yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

Masungidwe a tsiku la Purimu

20 Ndipo Mordekai analembera izi, natumiza makalata kwa Ayuda onse okhala m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, a kufupi ndi a kutali,

21 kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi chinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chisanu lomwe, chaka ndi chaka,

22 ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23 Ndipo Ayuda anavomereza kuchita monga umo adayambira, ndi umo Mordekai adawalembera;

24 popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda chiwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

25 koma pofika mlanduwo kwa mfumu, iye adalamula polemba kalata kuti chiwembu choipa cha Hamani adachipangira Ayuda chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana ake aamuna apachikidwe pamtengo.

26 Chifukwa chake anatcha masikuwaPurimu, ndilo dzina la ulawo. Momwemo, chifukwa cha mau onse a kalatayo, ndi izi adaziona za mlanduwo, ndi ichi chidawadzera,

27 Ayuda anakhazikitsa ichi, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, chingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, chaka ndi chaka;

28 ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mzinda uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.

29 Pamenepo Estere mkazi wamkulu mwana wa Abihaili, ndi Mordekai Myuda, analembera molamulira, kukhazikitsa kalata iyi yachiwiri ya Purimu.

30 Natumiza iye makalata kwa Ayuda onse, kumaiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahasuwero, ndiwo mau a mtendere ndi choonadi;

31 kukhazikitsa masiku awa a Purimu m’nyengo zao, m’mene Mordekai Myuda ndi mkazi wamkulu Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kufuula kwao.

32 Ndipo kunena kwake kwa Estere kunakhazikitsa mau awa a Purimu; ndipo kunalembedwa m’buku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/9-0405c021758e9aec8ee5ce6d062431b6.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 10

Ukulu wa Mordekai

1 Ndipo mfumu Ahasuwero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja.

2 Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya?

3 Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/10-c234db11718620573d237f989aa9d663.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za Yobu, munthu wolungama amene anakumana ndi mavuto aakulu, nakhala akuzunzika ndi kudandaula, nafunitsitsa kudziwa chifukwa chimene Mulungu walolera zoterezi.

Yobu anagwa m’mavuto aakulu: ana ake onse anafa, chuma chake chonse nkuwonongeka, ndipo mwinawakeyo anagwidwa ndi nthenda yoopsa, thupi lake nkuwola.

Abwenzi ake atatu anabwera kudzampepesa pa mavuto akewo, nayamba kukambirana za gwero lake la mavutowo, aliyense natulutsa maganizo ake. Abwenzi atatu aja, pofuna kufotokoza za gwero la mavuto a Yobu, angotsata maganizo a makolo achiyuda, akuti Mulungu amadalitsa anthu abwino ndipo amalanga anthu ochimwa; ndiye kuti mavuto amene Yobuyu anakumana nawo akusonyeza kuti iye anachimwa. Pamenepo Yobu akuti, Iyayi, nchosatheka; pakuti iyeyo wakhala akuyesetsa kukhala wabwino ndi wolungama masiku onse. Chifukwa chosamvetsa gwero lake la mavuto akewo, ayamba kufunsa Mulungu mafunso, ndipo amupempha kuti achitepo kanthu kosonyeza kuti iye ngwolungamadi, ndipo motero mbiri yake isaipitsidwe pamaso pa anthu.

Yehova poyankha sasamala mafunso a Yobu aja, angomuwonetsa ukulu wake, mphamvu zake ndi nzeru zake zodabwitsa, kulimbitsa chikhulupiriro cha Yobu. Apo Yobuyo adzichepetsa pamaso pa Mulungu ndipo amupepesa chifukwa cha mau okalipa aja omwe iye adalankhula potsutsana ndi Yehova.

Pambuyo pake Mulungu amudalitsa Yobu pomubwezera zabwino zake mowirikiza, ndipo adzudzula abwenzi ake atatu aja, chifukwa iwo adalephera kumvetsa tanthauzo la mavuto a Yobu. Yobu yekhayu adazindikira kuti Mulungu ngwamkulu koposa m’mene makolo achiyuda ankaganizira.

Za mkatimu

Mau oyambirira

1.1—2.13

Yobu ndi abwenzi ake

3.1—31.40

a. Kudandaula kwa Yobu

3.1-26

b. Kukambirana koyamba

4.1—14.22

c. Kukambirana kwachiwiri

15.1—21.34

d. Kukambirana kwachitatu

22.1—27.23

e. Mau oyamikira nzeru

28.1-28

f. Mau otsiriza a Yobu

29.1—31.40

Mau a Elihu

32.1—37.24

Mau a Yehova oyankha Yobu

38.1—42.6

Mau omaliza

42.7-17

Categories
YOBU

YOBU 1

Yobu wosautsidwabe alimbika kutama Mulungu

1 Panali munthu m’dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

2 Ndipo anabala ana aamuna asanu ndi awiri, ndi ana aakazi atatu.

3 Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndingamirazikwi zitatu, ndi ng’ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum’mawa.

4 Ndipo ana ake aamuna anamuka kukachita madyerero m’nyumba ya yense pa tsiku lake; natumiza mthenga kuitana alongo ao atatu adzadye nadzamwe nao.

5 Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.

6 Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzansoSatanapakati pao.

7 Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m’dziko ndi kuyendayenda m’mwemo.

8 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

9 Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?

10 Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m’dziko.

11 Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.

12 Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m’dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.

13 Tsono panali tsiku loti ana ake aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wao;

14 nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng’ombe zinalikulima, ndi abulu aakazi analikudya pambali pao;

15 koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

16 Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

17 Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Ababiloni anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamira, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

18 Akali chilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wao;

19 ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.

20 Pamenepo Yobu ananyamuka, nang’amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,

21 nati, Ndinatuluka m’mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.

22 Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/1-39622e1b07c595d70d8d6edbd856ff10.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 2

1 Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadzaSatanayemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m’dziko, ndi kuyendayenda m’mwemo.

3 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa.

4 Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.

5 Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.

6 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m’dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.

7 Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.

8 Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m’maphulusa.

9 Pamenepo mkazi wake ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.

10 Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.

Mabwenzi ake atatu adzacheza naye

11 Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

12 Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang’amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.

13 Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukulu ndithu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/2-7862c23242b46a078b9b4cba4e23b540.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 3

Madandaulo a Yobu

1 Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pake, natemberera tsiku lake.

2 Nalankhula Yobu nati,

3 Litayike tsiku lobadwa ine,

ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna.

4 Tsiku lija likhale mdima;

Mulungu asalifunse kumwamba,

ndi kuunika kusaliwalire.

5 Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese laolao;

mtambo ulikhalire;

zonse zodetsa usana bii ziliopse.

6 Usiku uja, mdima weniweni uugwere;

usakondwerere mwa masiku a m’chaka;

usalowe m’chiwerengedwe cha miyezi.

7 Ha! Usiku uja ukhale chumba;

kuimbira kokondwera kusalowe m’mwemo.

8 Autemberere iwo akutemberera usana,

Odziwa kuutsaLeviyatani.

9 Nyenyezi za chizirezire zide;

uyembekezere kuunika, koma kuusowe;

usaone kephenyuka kwa mbandakucha;

10 popeza sunatseke pa makomo ake mimba ya mai wanga.

Kapena kundibisira mavuto pamaso panga.

11 Ndinalekeranji kufera m’mimba?

Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine.

12 Anandilandiriranji maondo?

Kapena mawere kuti ndiyamwe?

13 Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala chete;

ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula;

14 pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko,

akudzimangira m’mabwinja;

15 kapena pamodzi ndi akalonga eni ake a golide,

odzaza nyumba zao ndisiliva;

16 Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zii;

ngati makanda osaona kuunika.

17 Apo oipa aleka kumavuta;

ndi apo ofooka mphamvu akhala m’kupumula.

18 Apo a m’kaidi apumula pamodzi,

osamva mau a wofulumiza wao.

19 Ang’ono ndi akulu ali komwe;

ndi kapolo amasuka kwa mbuyake.

20 Amninkhiranji kuunika wovutika,

ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,

21 wakuyembekezera imfa, koma kuli zii,

ndi kuikumba koposa chuma chobisika,

22 wakusekerera ndi chimwemwe

ndi kukondwera pakupeza manda?

23 Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika,

amene wamtsekera Mulungu?

24 Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga;

ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.

25 Pakuti chimene ndinachiopa chandigwera,

ndi chimene ndachita nacho mantha chandidzera.

26 Wosakhazikika, ndi wosakhala chete, ndi wosapumula ine,

koma mavuto anandidzera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/3-6202c66f3a581cf16dd9267fbbf35907.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 4

Elifazi adzudzula Yobu

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Munthu akayesa kunena nawe mau,

kodi udzamva nao chisoni?

Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?

3 Taona iwe walangiza aunyinji,

walimbitsa manja a ofooka.

4 Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa,

walimbitsanso maondo otewa.

5 Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka;

chikukhudza, ndipo uvutika.

6 Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,

ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?

7 Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse?

Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?

8 Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu,

nabzala vuto, akololapo zomwezo.

9 Atayika ndi mpweya wa Mulungu,

nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.

10 Kubangula kwa mkango,

ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,

ndi mano a misona ya mkango athyoledwa.

11 Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,

ndi misona ya mkango waukazi imwazika.

12 Anditengera mau m’tseri,

m’khutu mwanga ndinalandira kunong’oneza kwake.

13 M’malingaliro a masomphenya a usiku,

powagwira anthu tulo tatikulu

14 Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,

nanthunthumira nako mafupa anga onse.

15 Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;

tsitsi la thupi langa lidati nyaunyau.

16 Unaima chilili, koma sindinathe kuzindikira maonekedwe ake;

panali mzukwa pamaso panga;

kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,

17 Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?

Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?

18 Taona, sakhulupirira atumiki ake;

nawanenera amithenga ake zopusa;

19 kopambana kotani nanga iwo akukhala m’nyumba zadothi,

amene kuzika kwao kuli m’fumbi,

angothudzulidwa ngati njenjete.

20 Kuyambira m’mawa kufikira madzulo athudzuka;

aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.

21 Kukometsetsa kwao sikumachotsedwa nao?

Amafa koma opanda nzeru.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/4-c4008d5cfe7524034f6cf5fb55f3f00e.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 5

1 Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi?

Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?

2 Pakuti mkwiyo umapha wopusa,

ndi nsanje imakantha wopanda pake.

3 Ndinapenya wopusa woyala mizu;

koma pomwepo ndinatemberera pokhala pake.

4 Ana ake akhala otekeseka,

napsinjika kuchipata,

wopanda wina wakuwapulumutsa.

5 Zokolola zao anjala azidya,

azitenga ngakhale kuminga,

ndi aludzu ameza chuma chao.

6 Pakuti nsautso sutuluka m’fumbi,

ndi mavuto saphuka m’nthaka.

7 Koma munthu abadwira mavuto,

monga mbaliwali zikwera ziuluzika.

8 Koma ine ndikadafuna Mulungu,

ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;

9 amene achita zazikulu ndi zosalondoleka,

zinthu zodabwitsa zosawerengeka.

10 Amene avumbitsa mvula panthaka,

natumiza madzi paminda;

11 kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka,

kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka.

12 Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera,

kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.

13 Akola eni nzeru m’kuchenjera kwao,

ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe.

14 Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa,

nayambasa dzuwa lili pakati pamutu monga usiku.

15 Apulumutsa aumphawi kulupanga

la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu.

16 Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo,

ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.

17 Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula;

chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.

18 Pakuti apweteka, namanganso mabala;

alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.

19 Adzakupulumutsa m’masautso asanu ndi limodzi;

chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.

20 Adzakuombola kuimfa m’njala,

ndi kumphamvu ya lupanga m’nkhondo.

21 Udzabisikira mkwapulo wa lilime,

sudzachiopanso chikadza chipasuko.

22 Chipasuko ndi njala udzaziseka;

ngakhale zilombo za padziko osaziopa.

23 Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala yakuthengo;

ndi nyama zakuthengo zidzakhala nawe mumtendere.

24 Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere;

nudzazonda za m’banja mwako osasowapo kanthu.

25 Udzapezanso kuti mbeu zako zidzachuluka,

ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.

26 Udzafika kumanda utakalamba,

monga abwera nao mtolo wa tirigu m’nyengo yake.

27 Taona, ichi tachifunafuna, chili chotero;

uchimvere, nuchidziwire wekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/5-35f8439fd0bb1a9554af3b9fdb4ba2a9.mp3?version_id=1068—

Categories
YOBU

YOBU 6

Yobu adzilungamitsa pa kudandaula kwake

1 Koma Yobu anayankha, nati,

2 Mwenzi atayesa bwino chisoni changa,

ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!

3 Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja;

chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena.

4 Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa,

mzimu wanga uwumwa ulembe wake;

zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.

5 Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu?

Ilira kodi ng’ombe pa chakudya chake?

6 Kodi chinthu chosakolera chidyeka chopanda mchere?

Choyera cha dzira chikolera kodi?

7 Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza

zikunga chakudya chosakolera kwa ine.

8 Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha,

Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!

9 Chimkomere Mulungu kundiphwanya,

alole dzanja lake lindilikhe!

10 Pamenepo ndidzasangalala,

ndidzakondwera nacho chowawa chosandileka;

pakuti sindinawabise mau a Woyerayo.

11 Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze?

Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?

12 Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala?

Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?

13 Mulibe thandizo mwa ine ndekha; chipulumutso chandithawa.

14 Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo;

angaleke kuopa Wamphamvuyonse.

15 Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje,

ngati madzi a timitsinje akupitirira.

16 Amada chifukwa cha madzi oundana.

M’menemo chipale chofewa chibisika;

17 atafikira mafundi, mitsinje iuma;

kukatentha, imwerera m’malo mwao.

18 Aulendo akutsata njira yao apatukapo,

akwerera poti see, natayika.

19 Aulendo a ku Tema anapenyerera,

makamu a ku Sheba anaiyembekezera.

20 Anazimidwa popeza adaikhulupirira;

anafikako, nathedwa nzeru.

21 Pakuti tsopano mukhala momwemo;

muona choopsa, muchitapo mantha.

22 Ngati ndinati, Mundipatse?

Kapena, Muperekeko kwa ine chuma chanu?

23 Kapena, Mundilanditse m’dzanja la mdani?

Kapena, Mundiombole m’dzanja la oopsa?

24 Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine;

mundizindikiritse umo ndinalakwira.

25 Mau oongoka si ndiwo amphamvu?

Koma kudzudzula kwanu mudzudzula chiyani?

26 Kodi muyesa kudzudzula mau?

Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.

27 Indetu, mugwetsera wamasiye msampha,

mumkumbira bwenzi lanu mbuna.

28 Koma tsopano balindani, mundipenyerere;

ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.

29 Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu;

inde, bwereraninso mlandu wanga ngwolungama.

30 Kodi pali chosalungama palilime panga?

Ngati sindizindikire zopanda pake m’kamwa mwanga?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/6-622f1e656ca2334371fef00e9a5cd165.mp3?version_id=1068—