Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 30

Hezekiya achita Paska ku Yerusalemu

1 Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso makalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova kuYerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa IsraelePaska.

2 Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.

3 Pakuti sanakhoze kumchita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikire, ndi anthu sadasonkhane ku Yerusalemu.

4 Ndipo chinthuchi chinayenera m’maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse.

5 Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israele lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikulu sanachite monga mudalembedwa.

6 Tsono amtokoma anamuka ndi makalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m’dzanja la mafumu a Asiriya.

7 Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene analakwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya.

8 Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m’malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu.

9 Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m’dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa chisomo ndi chifundo; sadzakuyang’anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye.

10 Ndipo amtokoma anapitira m’mizinda yonse ya dziko la Efuremu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.

11 Komatu ena a Asere ndi Manase ndi a Zebuloni anadzichepetsa, nadza ku Yerusalemu.

12 Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.

13 Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchitachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsamwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu.

14 Ndipo anauka nachotsa maguwa a nsembe okhala mu Yerusalemu, nachotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m’mtsinje wa Kidroni.

15 Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova.

16 Naima m’malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa chilamulo cha Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira kudzanja la Alevi.

17 Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatule; potero Alevi anayang’anira kupha za Paska kwa aliyense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova.

18 Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efuremu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretse, koma anadya Paska mosati monga munalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense

19 wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.

20 Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawachiritsa anthu.

21 Ndipo ana a Israele opezeka mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa kwa Yehova.

22 Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.

23 Ndipo msonkhano wonse unapangana kuchita masiku asanu ndi awiri ena, nachita masiku asanu ndi ena ndi chimwemwe.

24 Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng’ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akulu anapatsa msonkhano ng’ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembe ambiri adadzipatula.

25 Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala mu Yuda, anakondwera.

26 Momwemo munali chimwemwe chachikulu mu Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele simunachitike chotero mu Yerusalemu.

27 Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/30-7956a3ac55adff94fc09babbf82998de.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 31

Afafaniza chipembedzo chonse cha mafano

1 Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumizinda ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe mu Yuda monse, ndi mu Benjamini, mu Efuremunso, ndi mu Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumizinda yao.

2 Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Yehova.

3 Naikanso gawo la mfumu lotapa pa chuma chake la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m’mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m’chilamulo cha Yehova.

4 Anauzanso anthu okhala muYerusalemuapereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m’chilamulo cha Yehova.

5 Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m’minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka.

6 Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m’mizinda ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng’ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu.

7 Mwezi wachitatu anayamba kuika miyalo ya miyuluyi, naitsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri.

8 Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.

9 Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuluyi.

10 Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala.

11 Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m’nyumba ya Yehova; nazikonza.

12 Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang’anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng’ono wake ndiye wotsatana naye.

13 Ndi Yehiyele, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asahele, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyele, ndi Isimakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng’ono wake, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkulu wa kunyumba ya Mulungu.

14 Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum’mawa, anayang’anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.

15 Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Miniyamini, ndi Yesuwa, ndi Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m’mizinda ya ansembe, kugawira abale ao m’zigawo zao mokhulupirika, akulu monga ang’ono;

16 pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa aliyense amene adalowa m’nyumba ya Yehova, monga mwa ntchito yake pa tsiku lake, kukachita za utumiki wao mu udikiro wao monga mwa zigawo zao;

17 ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mu udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;

18 ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ana ao aang’ono onse, akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi, mwa msonkhano wonse; pakuti m’kukhulupirika kwao anadzipatula akhale opatulika;

19 panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m’minda ya kubusa kwa mizinda yao, m’mzinda uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao.

20 Momwemo anachita Hezekiya mwa Yuda lonse nachita chokoma, ndi choyenera, ndi chokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wake.

21 Ndipo m’ntchito iliyonse anaiyamba mu utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m’chilamulo, ndi m’mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/31-a22a0d4dd9b18d7bbb42979c635d764d.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 32

Senakeribu agwera Yuda

1 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira mizinda yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.

2 Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Senakeribu, ndi kuti nkhope yake inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndiYerusalemu,

3 anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a mu akasupe okhala kunja kwa mzinda; namthandiza iwo.

4 Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati padziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri.

5 Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m’mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.

6 Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye kubwalo la kuchipata cha mzinda, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti,

7 Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye;

8 pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.

9 Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,

10 Atero Senakeribu mfumu ya Asiriya, Mutama chiyani kuti mukhala m’linga mu Yerusalemu?

11 Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m’dzanja la mfumu ya Asiriya?

12 Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?

13 Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m’maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m’dzanja langa?

14 Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ake m’dzanja mwanga?

15 Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe Mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu, kapena ufumu uliwonse, unakhoza kulanditsa anthu ake m’dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m’dzanja langa?

16 Ndipo anyamata ake anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wake Hezekiya.

17 Analemberanso makalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m’maiko, imene siinalanditse anthu ao m’dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m’dzanja mwanga.

18 Ndipo anafuula ndi mau aakulu m’chinenedwe cha Ayuda kwa anthu a mu Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwavuta, kuti alande mzindawu.

19 Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a padziko lapansi, ndiyo ntchito ya manja a anthu.

20 Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesayamnenerimwana wa Amozi, anapemphera pa ichi, nafuulira Kumwamba.

21 Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m’nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m’matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.

22 Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala mu Yerusalemu m’dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m’dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.

23 Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso paamitunduonse kuyambira pomwepo.

Nthenda ndi imfa ya Hezekiya

24 Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa chizindikiro chodabwitsa.

25 Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.

26 Koma Hezekiya anadzichepetsa m’kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala mu Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzere masiku a Hezekiya.

27 Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramosiliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse;

28 ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iliyonse, ndi makola a zoweta.

29 Nadzimangiranso mizinda, nadzionera nkhosa ndi ng’ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri.

30 Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse.

31 Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m’dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.

32 Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m’masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

33 Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala mu Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/32-992fffafd25659057ef3d5ff6461ed3d.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 33

Manase aikanso chipembedzo cha mafano

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi asanu mphambu zisanu.

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa zaamitundu, amene Yehova anawachotsa m’dziko mwao pamaso pa ana a Israele.

3 Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wake, nautsira Abaalamaguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.

4 Namanga maguwa a nsembe m’nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, Mu Yerusalemu mudzakhala dzina langa kunthawi zonse.

5 Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.

6 Anapititsanso ana ake pamoto m’chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.

7 Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m’nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M’nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha m’mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse;

8 ndipo sindidzasunthanso phazi la Israele kudziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kuchita zonse ndawalamulira, chilamulo chonse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.

9 Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele.

Manase atengedwa kunka ku Babiloni, alapa nabwezedwa ku Yerusalemu

10 Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake, koma sanasamalire.

11 Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.

12 Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.

13 Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu mu ufumu wake. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.

14 Chitatha ichi tsono iye anaumangira mzinda wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m’chigwa, mpaka polowera pa Chipata cha Nsomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m’mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda.

15 Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m’nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m’phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu, nawataya kunja kwa mzinda.

16 Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israele.

17 Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.

18 Machitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndi mau a alauli akunena naye m’dzina la Yehova Mulungu wa Israele, taonani, zalembedwa m’machitidwe a mafumu a Israele.

19 Pemphero lake lomwe, ndi m’mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m’buku la mau a Hozai.

20 Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m’nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Amoni mfumu yoipayo

21 Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka ziwiri.

22 Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira Manase atate wake; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wake, nawatumikira.

23 Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.

24 Ndipo anyamata ake anampangira chiwembu, namupha m’nyumba yakeyake.

25 Koma anthu a m’dziko anapha onse adampangira chiwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m’dziko analonga Yosiya mwana wake akhale mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/33-b73155349cc6e99d52123fdc1438b719.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 34

Yosiya achotsa chipembedzo cha mafano, nakonzanso Kachisi

1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi atatu mphambu chimodzi.

2 Nachita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m’njira za Davide kholo lake, osapatuka kudzanja lamanja kapena kulamanzere.

3 Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.

4 Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.

5 Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.

6 Nateronso m’mizinda ya Manase, ndi Efuremu, ndi Simeoni, mpaka Nafutali, m’mabwinja mwao mozungulira.

7 Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m’dziko lonse la Israele, nabwerera kunka ku Yerusalemu.

8 Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma Safani mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya kazembe wa mzinda, ndi Yowa mwana wa Yehowahazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wake.

9 Ndipo anadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama adabwera nazo kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira kudzanja la Manase ndi Efuremu, ndi kwa otsala onse a Israele, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala mu Yerusalemu.

10 Ndipo anazipereka m’dzanja la antchito oikidwa ayang’anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m’nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;

11 anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam’mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.

12 Ndipo amunawo anachita ntchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang’anire ndiwo Yahati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena aliyense waluso la zoimbira.

13 Anayang’aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira ntchito ya utumiki uliwonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira.

Hilikiya apeza buku la chilamulo

14 Ndipo pakutulutsa ndalama zimene adalowa nazo kunyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.

15 Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m’nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani.

16 Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzichita.

17 Nakhuthula ndalama zinapezeka m’nyumba ya Yehova, nazipereka m’manja a akapitao ndi m’manja a antchito.

18 Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

19 Ndipo kunali, atamva mfumu mau a chilamulo, anang’amba zovala zake.

20 Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

21 Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala mu Israele ndi Yuda, za mau a m’buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukulu; popeza makolo athu sanasunge mau a Yehova kuchita monga mwa zonse zolembedwa m’bukumu.

Hulida aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu

22 Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulidamneneriwamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala mu Yerusalemu m’dera lachiwiri, nanena naye mwakuti.

23 Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

24 Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m’mwemo choipa, ndicho matemberero onse olembedwa m’buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda;

25 chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.

26 Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva,

27 popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m’mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung’amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.

28 Taona, ndidzakusonkhanitsa kumakolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m’mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.

Yosiya ndi anthu achitanso pangano ndi Mulungu

29 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.

30 Nikwera mfumu kunyumba ya Yehova ndi amuna onse a mu Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse aakulu ndi aang’ono; nawerenga iye m’makutu mwao mau onse a buku lachipanganoadalipeza m’nyumba ya Yehova.

31 Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mau a chipangano olembedwa m’bukumu.

32 Naimiritsapo onse okhala mu Yerusalemu ndi mu Benjamini. Ndipo okhala mu Yerusalemu anachita monga mwa chipangano cha Mulungu, Mulungu wa makolo ao.

33 Yosiya nachotsa zonyansa zonse m’maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka mu Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/34-4e15f281ba987cc2f14e8d363bd66ea1.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 35

Yosiya achita Paska ku Yerusalemu

1 Pamenepo Yosiya anachitira YehovaPaskamuYerusalemu, naphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba.

2 Ndipo anaika ansembe pa udikiro wao, nawalimbikitsa achite utumiki wa nyumba ya Yehova.

3 Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m’nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.

4 Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m’zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israele, ndi umo adalembera Solomoni mwana wake.

5 Ndipo muimirire m’malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.

6 Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.

7 Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, anaankhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paska kwa aliyense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng’ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa chuma cha mfumu.

8 Ndi akulu ake anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a m’nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing’ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng’ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paska.

9 Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netanele, abale ake, ndi Hasabiya, ndi Yeiyele, ndi Yozabadi, akulu a Alevi, anapatsa Alevi zoweta zazing’ono zikwi zisanu, ndi ng’ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paska.

10 Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m’zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu.

11 Pamenepo anaphera Paska; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m’manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.

12 Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m’buku la Mose. Natero momwemo ndi ng’ombezo.

13 Ndipo anaotcha Paska pamoto, monga mwa chiweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m’miphika, ndi m’mitsuko, ndi m’ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.

14 Ndi pambuyo pake anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; chifukwa chake Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.

15 Ndi oimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera.

16 Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kuchita Paska, ndi kupereka nsembe zopsereza paguwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.

17 Ndipo ana a Israele okhalako anachita Paska nthawi yomweyo, ndichikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsamasiku asanu ndi awiri.

18 Panalibe Paska wochitika mu Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuelemneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala mu Yerusalemu.

19 Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anachita Paska amene.

Yosiya ayambana ndi Neko mfumu ya Aejipito, naphedwa

20 Chitatha ichi chonse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aejipito anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Yufurate; ndipo Yosiya anamtulukira kuyambana naye.

21 Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndili ndi chiyani ndi inu, mfumu ya Yuda? Sindinafike kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndili nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kuvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.

22 Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m’kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m’chigwa cha Megido.

23 Ndipo oponya anayang’anitsa mivi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ake, Ndichotseni ndalasidwa ndithu.

24 Pamenepo anyamata ake anamtulutsa m’galeta, namuika m’galeta wachiwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m’manda a makolo ake. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.

25 Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.

26 Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi ntchito zake zokoma, monga mulembedwa m’chilamulo cha Yehova,

27 ndi zochita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m’buku la mafumu a Israele ndi Yuda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/35-e5dca4080ef031116dc82fe65179a398.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 36

Yehowahazi, Yehoyakimu, Yehoyakini, mafumu a Yuda

1 Pamenepo anthu a m’dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu muYerusalemu, m’malo mwa atate wake.

2 Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu.

3 Ndipo mfumu ya Aejipito anamchotsera ufumu wake mu Yerusalemu, nasonkhetsa dziko matalente zana limodzi asiliva, ndi talente limodzi la golide.

4 Ndi mfumu ya Aejipito anamlonga Eliyakimu mng’ono wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lake likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehowahazi mkulu wake, namuka naye ku Ejipito.

Yehoyakimu mfumu ya Yuda

5 Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.

6 Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babiloni.

7 Nebukadinezara anatenganso ndi zipangizo za nyumba ya Yehova kunka nazo ku Babiloni, naziika mu Kachisi wake ku Babiloni.

8 Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zake anazichita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m’buku la mafumu a Israele ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

9 Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nachita choipa pamaso pa Yehova.

10 Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babiloni, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.

Zedekiya woipa, mfumu yotsiriza ya Yuda

11 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi,

12 nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetse kwa Yeremiyamneneriwakunena zochokera pakamwa pa Yehova.

13 Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.

14 Ndiponso ansembe aakulu onse ndi anthu anachulukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse zaamitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene anapatula mu Yerusalemu.

15 Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake;

16 koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.

Yerusalemu apasulidwa anthu natengedwa ukapolo ku Babiloni

17 Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m’nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m’dzanja lake.

18 Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing’ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.

19 Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.

20 Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babiloni, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake, mpaka mfumu ya Persiya idachita ufumu;

21 kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasungaSabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.

Kirusi alola yense wofuna abwere kwao kukamanga Kachisi

22 Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,

23 Atero Kirusi mfumu ya Persiya, Yehova Mulungu Wam’mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/36-6d0593dc2381b9c2f8ce922dc33e3230.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Nkhani imene ili mu buku la

Ezara

ikutsatana ndi nkhani za m’mabuku awiri a

Mbiri

, ndipo ikulongosola za kubwerera kwa ena mwa Ayuda kuchokera ku Babiloni kumene anatengedwa ngati akapolo. Bukuli likufotokozanso za kubwezeretsedwa kwa moyo ndi chipembedzo mu Yerusalemu. Nkhanizi zaperekedwa m’magawo atatu: Gawo loyamba ndi la gulu la Ayuda amene anabwerera kuchokera ku Babiloni potsatira lamulo limene adapereka Kirusi amene anali mfumu ya Persiya. Gawo lachiwiri likunena za kumangidwanso ndi kupatulidwa kwa Kachisi komanso za kukonzedwanso kwa chipembedzo cha Mulungu ku Yerusalemu. Gawo lachitatu likunena za gulu lina la Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu motsogozedwa ndi Ezara, amene anali katswiri pa Malamulo a Mulungu, ndipo iye anawathandiza anthu kuti akonzenso chikhalidwe ndi moyo wa chipembedzo pofuna kusunga miyambo ya chipembedzo mu Israele.

Za mkatimu

Gulu loyamba la anthu libwerera

1.1—2.70

Kachisi amangidwanso napatulidwa

3.1—6.22

Ezara abwerera ndi anthu ena

7.1—10.44

Categories
EZARA

EZARA 1

Mulungu apangira Kirusi alole Ayuda abwere kwao kukamanga Kachisi

1 Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m’kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,

2 Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam’mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba muYerusalemu, ndiwo mu Yuda.

3 Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.

4 Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndisiliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.

5 Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.

6 Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.

Kirusi abweza zipangizo za Kachisi

7 Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa mu Yerusalemu, ndi kuziika m’nyumba ya milungu yake;

8 zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.

9 Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;

10 zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.

11 Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/1-d4bfde8d5f981aaca5e1f02e9ea7e505.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 2

Maina a Ayuda obwera ku Yerusalemu ndi Zerubabele

1 Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m’ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka kuYerusalemundi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:

2 ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:

3 ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

4 Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

5 Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu.

6 Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri.

7 Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

8 Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu.

9 Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

10 Ana a Bani, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.

11 Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

12 Ana a Azigadi, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi awiri ndi awiri.

13 Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi.

14 Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

15 Ana a Adini, mazana anai mphambu makumi asanu kudza anai.

16 Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu.

17 Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu.

18 Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

19 Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

20 Ana a Gibara, makumi asanu ndi anai mphambu asanu.

21 Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.

22 Anthu a ku Netofa, makumi asanu mphambu asanu ndi mmodzi.

23 Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

24 Ana a Azimaveti, makumi anai mphambu awiri.

25 Ana a Kiriyati-Arimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.

26 Ana a Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

27 Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

28 Anthu a ku Betele ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

29 Ana a Nebo, makumi asanu mphambu awiri.

30 Ana a Magabisi, zana limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

31 Ana a Elamu wina, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

32 Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.

33 Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza asanu.

34 Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

35 Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.

36 Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.

37 Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

38 Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.

39 Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.

40 Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.

41 Oimba: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

42 Ana a odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, onse pamodzi ndiwo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anai.

43 Antchito a m’kachisi: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,

44 ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni,

45 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu,

46 ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani,

47 ana a Gidele, ana a Gahara, ana a Reaya,

48 ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu,

49 ana a Uza, ana a Paseya, ana a Besai,

50 ana a Asina, ana a Meunimu, ana a Nefisimu,

51 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,

52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,

53 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,

54 ana a Neziya, ana a Hatifa.

55 Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,

56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele,

57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Ami.

58 Antchito onse a m’kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.

59 Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele:

60 ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

61 Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.

62 Awa anafunafuna maina ao m’buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe chao, koma osawapeza; potero anachotsedwa ku ntchito ya nsembe monga odetsedwa.

63 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndiUrimu ndi Tumimu.

64 Msonkhano wonse pamodzi ndiwo wa zikwi makumi anai ndi awiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,

65 osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri.

66 Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu;

67 ngamirazao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.

68 Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake.

69 Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina yasilivazikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi.

70 Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m’kachisi, anakhala m’midzi mwao, ndi Aisraele onse m’midzi mwao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/2-07bda91fdb85273b79feb6b054be8301.mp3?version_id=1068—