Rebeka apalidwa ubwenzi ndi Isaki
1 Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse.
2 Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:
3 ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
4 Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isaki mkazi.
5 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu?
6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Chenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.
7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.
9 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu Mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho.
10 Ndipo mnyamatayo anatengangamirakhumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m’dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
11 Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mzinda, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.
12 Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu.
13 Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m’mzinda atuluka kudzatunga madzi;
14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.
15 Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m’maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera.
17 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang’ono a m’mtsuko mwako.
18 Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m’manja mwake namwetsa iye.
19 Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamira zako, mpaka zitamwa zonse.
20 Ndipo anafulumira nathira madzi a m’mtsuko wake m’chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamira zake zonse.
21 Munthuyo ndipo anamyang’anira iye, nakhala chete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai.
22 Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m’manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
23 Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi kunyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife?
24 Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.
25 Natinso kwa iye, Tili nao udzu ndi zakudya zambiri ndi malo ogona.
26 Munthuyo ndipo anawerama mutu namyamika Yehova.
27 Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m’njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.
28 Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo kunyumba ya amake.
29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.
30 Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.
31 Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.
32 Munthuyo ndipo analowa m’nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.
33 Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
34 Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu.
35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng’ombe, ndisilivandi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.
36 Ndipo Sara mkazi wake wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo.
37 Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamtengere mwana wanga mkazi wa ana aakazi a Kanani, m’dziko mwao m’mene ndikhala ine;
38 koma udzanke kunyumba ya atate wanga, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga mkazi.
39 Ndipo ndinati kwa mbuyanga, Kapena mkazi sadzanditsata ine.
40 Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m’njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;
41 ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako.
42 Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m’mene ndinkamo ine;
43 taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene atuluka kudzatunga madzi ndimwe pang’ono m’mtsuko mwako;
44 ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.
45 Ndisanathe kunena m’mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
46 Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lake, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamira.
47 Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake.
48 Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m’njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.
49 Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere.
50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.
51 Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.
52 Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi.
53 Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.
54 Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m’mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
55 Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka.
56 Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m’njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
57 Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pake.
58 Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka.
59 Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake.
60 Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
61 Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamira natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka.
62 Ndipo Isaki anadzera njira ya Beere-Lahai-Roi; chifukwa kuti anakhala iye m’dziko la kumwera.
63 Ndipo Isaki anatuluka kulingalira m’munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, taona, ngamira zinalinkudza.
64 Ndipo Rebeka anatukula maso ake, ndipo pamene anaona Isaki anatsika pa ngamira.
65 Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m’munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.
66 Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita.
67 Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m’hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/24-006b0bf6dce6bba173f56f7d6772eead.mp3?version_id=1068—