Categories
1 YOHANE

1 YOHANE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yoyamba yolembedwa ndi mtumwi Yohane

ili ndi mfundo ziwiri zazikulu: mfundo yoyamba ndiyo kulimbikitsa awerengi kuti akhale m’moyo woyanjana ndi Mulungu komanso ndi mwana wake Yesu Khristu, ndipo yachiwiri ndi kuwachenjeza kuti asatsate ziphunzitso zonyenga zimene zikhoza kuononga chiyanjano chao ndi Mulungu. Ziphuzitsozi zimagona pa chikhulupiriro chakuti dziko lapansi ndi loipa ndi munthu amakhala woipa pamene wakhudzana ndi dziko lino. Ankanenanso kuti Yesu amene ali Mwana wa Mulungu, sakadakhala munthu weniweni. Aphunzitsi amenewo amanena kuti munthu akhoza kupulumutsidwa pokhapokha atasiyana kulumikizana ndi dzikoli, komanso amanena kuti chipulumutso sichikhudzana konse ndi khalidwe labwino kapena kukonda anthu ena.

Pofuna kutsutsa chiphunzitso chimenechi, wolemba bukuli akunenetsa kuti Yesu Khristu analidi munthu weniweni, ndipo iye akutsindika kuti onse okhulupirira mwa Yesu amakonda Mulungu ndipo ayeneranso kukondana wina ndi mnzake.

Za mkatimu

Mau Oyamba 1.1-4

Kuwala ndi mdima 1.5—2.29

Ana a Mulungu ndi ana a Satana 3.1-24

Choonadi ndi bodza 4.1-6

Udindo wa chikondi 4.7-21

Chikhulupiriro chopambana 5.1-21

Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 1

Mau a moyo aoneka m’thupi

1 Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m’maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo,

2 (ndipo moyowo unaonekera, ndipo tidaona, ndipo tichita umboni, ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuonekera kwa ife);

3 chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake YesuKhristu;

4 ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe.

Mulungu ali kuunika; wosayenda m’kuunika alibe chiyanjano ndi Iye

5 Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.

6 Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;

7 koma ngati tiyenda m’kuunika, monga Iye ali m’kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Za kuwulula machimo ndi kukhululukidwa

8 Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi.

9 Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

10 Tikanena kuti sitidachimwe, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/1-fa5d2d29720872ba878eb0893245f4ae.mp3?version_id=1068—

Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 2

1 Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye YesuKhristuwolungama;

2 ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.

Za kusunga malamulo, kukondana, ndi kudzimana zapadziko

3 Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.

4 Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;

5 koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M’menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;

6 iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.

7 Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva.

8 Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala.

9 Iye amene anena kuti ali m’kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.

10 Iye amene akonda mbale wake akhala m’kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.

11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.

12 Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake.

13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.

15 Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.

16 Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.

17 Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.

Za okana Khristu

18 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.

19 Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.

20 Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.

21 Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.

22 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.

23 Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso.

24 Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.

25 Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.

26 Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.

27 Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.

28 Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akaonekere Iye tikakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake.

29 Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/2-705d454469123994948e9f5864b31ebc.mp3?version_id=1068—

Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 3

Ife ndife ana a Mulungu

1 Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

2 Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.

3 Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.

4 Yense wakuchita tchimo achitanso kusaweruzika; ndipo tchimo ndilo kusaweruzika.

5 Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.

6 Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.

7 Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:

8 iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.

9 Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sangathe kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.

10 M’menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.

11 Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake:

12 osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.

13 Musazizwe, abale, likadana nanu dziko lapansi.

14 Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m’moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.

15 Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.

16 Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.

17 Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?

18 Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.

19 Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake,

20 m’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.

21 Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu;

22 ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.

23 Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake YesuKhristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira.

24 Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m’menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/3-fcb9d35c2182c7c442dcd528bb0d9b42.mp3?version_id=1068—

Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 4

Za aphunzitsi onyenga

1 Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m’dziko lapansi.

2 M’menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti YesuKhristuanadza m’thupi, uchokera mwa Mulungu;

3 ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m’dziko lapansi tsopano lomwe,

4 Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m’dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m’dziko lapansi;

5 mwa ichi alankhula monga ochokera m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera.

6 Ife ndife ochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa choonadi, ndi mzimu wa chisokeretso.

Mulungu ndiye chikondi. Za kukonda Mulungu ndi kukondana ndi abale

7 Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.

8 Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.

9 Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.

10 Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.

11 Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.

12 Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;

13 m’menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.

14 Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.

15 Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.

16 Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.

17 M’menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m’tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m’dziko lino lapansi.

18 Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m’chikondi.

19 Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.

20 Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.

21 Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/4-6f5ecc11d939af64088c71f141d45125.mp3?version_id=1068—

Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 5

Za kukhulupirira Yesu ndi zotsatira zake

1 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiyeKhristuwabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.

2 Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake.

3 Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.

4 Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.

5 Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?

6 Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.

7 Pakuti pali atatu akuchita umboni,

8 Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.

9 Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake.

10 Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.

11 Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.

12 Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

13 Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.

Mphamvu ya kupemphera

14 Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;

15 ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.

16 Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.

17 Chosalungama chilichonse chili uchimo; ndipo pali tchimo losati la kuimfa.

18 Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

19 Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.

20 Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.

21 Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/5-3d6b4460b20fdcfea6f90fc7303f3f5f.mp3?version_id=1068—

Categories
2 YOHANE

2 YOHANE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yachiwiri yolembedwa ndi mtumwi Yohane

inalembedwa ndi “Mkuluyo” kupita kwa “mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake”, amene mwina akutanthauza mpingo ndi anthu ake. Uthenga wake ndi waufupi ndipo ndi wolimbitsana za kukondana komanso kuchenjeza za aphunzitsi onyenga ndi ziphunzitso zawo zachinyengo.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-3

Kufunikira kwa chikondi 1.4-6

Awachenjeze asatsate ziphunzitso zonyenga 1.7-11

Mau omaliza 1.12-13

Categories
2 YOHANE

2 YOHANE 1

1 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m’choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi;

2 chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha:

3 Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa YesuKhristuMwana wa Atate, m’choonadi ndi m’chikondi.

Za chikondano. Za aphunzitsi onyenga

4 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m’choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.

5 Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake.

6 Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.

7 Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m’dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m’thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.

8 Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.

9 Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m’chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana.

10 Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni.

11 Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa.

12 Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.

13 Akupereka moni ana a mbale wanu wosankhika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2JN/1-36bd159537e75f3891bea6c2f03289ff.mp3?version_id=1068—

Categories
3 YOHANE

3 YOHANE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yachitatu yolembedwa ndi mtumwi Yohane

inalembedwa ndi “Mkuluyo” kulembera mtsogoleri wa mpingo dzina lake Gayo. Mlembiyo akumuyamikira Gayo chifukwa cha kuthandiza Akhristu ena, komanso akuwachenjeza za munthu wina dzina lake Diotrefe.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-4

Gayo akumulemekeza 1.5-8

Diotrefe akumudzudzula 9-10

Demetrio akumuyamikira 1.11-12

Mau omaliza 1.13-15

Categories
3 YOHANE

3 YOHANE 1

1 Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m’choonadi.

2 Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.

3 Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m’choonadi.

Za kuchereza abale ndi alendo

4 Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.

5 Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chilichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe;

6 amene anachita umboni za chikondi chako pamaso paMpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:

7 pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwaamitundu.

8 Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.

Za Diotrefe ndi Demetrio

9 Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.

10 Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo.

11 Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuone Mulungu.

12 Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.

13 Ndinali nazo zambiri za kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni;

14 koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana.

15 Mtendere ukhale nawe. Akupereka moni abwenzi. Upereke moni kwa abwenzi ndi kutchula maina ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/3JN/1-3ef7c2f35a82dd29d5c8d5893e907c93.mp3?version_id=1068—