Categories
AHEBRI

AHEBRI 10

1 Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.

2 Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?

3 Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka.

4 Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.

5 Mwa ichi polowa m’dziko lapansi, anena,

Nsembe ndi chopereka simunazifune,

koma thupi munandikonzera Ine.

6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo

simunakondwere nazo;

7 pamenepo ndinati, Taonani, ndafika,

(Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine)

kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.

8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifune, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),

9 pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho.

10 Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la YesuKhristu, kamodzi, kwatha.

11 Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;

12 koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire;

13 kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake.

14 Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa.

15 Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena,

16 Ichi ndichipanganondidzapangana nao,

atapita masiku ajawo, anena Ambuye:

Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;

ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;

17 ndipo machimo ao ndi kusaweruzika kwao

sindidzakumbukiranso.

18 Koma pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.

Awachenjeza alimbike m’chikhulupiriro

19 Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m’malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,

20 pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;

21 ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;

22 tiyandikire ndi mtima woona, m’chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

23 tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;

24 ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,

25 osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

26 Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,

27 koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.

28 Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa opanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:

29 ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;

30 pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.

31 Kugwa m’manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.

32 Koma tadzikumbutsani masiku akale, m’menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa;

33 pena pochitidwa chinthu chooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ochitidwa zotere.

34 Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m’ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.

35 Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.

36 Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.

37 Pakuti katsala kanthawi kakang’onong’ono,

ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.

38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro:

Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.

39 Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/10-88c37333e42ca597e035e8c20ea5f34e.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 11

Za Okhulupirira a mu Chipangano Chakale

1 Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.

2 Pakuti momwemo akulu anachitidwa umboni.

3 Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m’mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwe kuchokera mu zoonekazo.

4 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.

5 Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeke, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;

6 koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.

7 Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.

8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.

9 Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m’mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;

10 pakuti analindirira mzinda wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.

11 Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;

12 mwa ichinso kudachokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m’mwamba, ndi ngati mchenga, uli m’mphepete mwa nyanja, osawerengeka.

13 Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.

14 Pakuti iwo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.

15 Ndipotu akadakumbukira lijalo adatulukamo akadaona njira yakubwerera nayo.

16 Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la mu Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mzinda.

17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha;

18 amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isaki mbeu yako idzaitanidwa:

19 poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.

20 Ndi chikhulupiriro Isaki anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zilinkudza.

21 Ndi chikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pamutu wa ndodo yake.

22 Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anatchula za matulukidwe a ana a Israele; nalamulira za mafupa ake.

23 Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum’bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaope chilamuliro cha mfumu.

24 Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi waFarao;

25 nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;

26 nawerenga tonzo laKhristuchuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.

27 Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.

28 Ndi chikhulupiriro anachitaPaska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.

29 Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.

30 Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.

31 Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeke pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.

32 Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;

33 amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,

34 nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.

35 Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,

36 kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m’ndende;

37 anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,

38 (amenewo dziko lapansi silinayenere iwo), osokerera m’mapululu, ndi m’mapiri, ndi m’mapanga, ndi m’mauna a dziko.

39 Ndipo iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandire lonjezanolo,

40 popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/11-632f7413373adfe690762303cf34f281.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 12

Tipirire angakhale masautso achuluka, monga anatero Khristu

1 Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,

2 Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

3 Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.

4 Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo tchimo;

5 ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana,

Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye,

kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye;

6 pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga,

nakwapula mwana aliyense amlandira.

7 Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?

8 Koma ngati mukhala opanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli am’thengo, si ana ai.

9 Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

10 Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake.

11 Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

12 Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;

13 ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m’njira, koma chichiritsidwe.

14 Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

15 ndi kuyang’anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;

16 kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya.

17 Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.

18 Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,

19 ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;

20 pakuti sanakhoze kulola cholamulidwacho. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala;

21 ndipo maonekedwewo anali oopsa otere, kuti Mose anati, Ndiopatu ndi kunthunthumira.

22 Komatu mwayandikira kuphiri laZiyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo,Yerusalemuwa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka waangelo,

23 ndi kwa msonkhano wa onse ndiMpingowa obadwa oyamba olembedwa mu Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,

24 ndi kwa Yesu Nkhoswe yachipanganochatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.

25 Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;

26 amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m’mwamba.

27 Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.

28 Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.

29 Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/12-43ffdf14c88d5786348ee17bbbf56cd0.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 13

1 Chikondi cha pa abale chikhalebe.

2 Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anacherezaangeloosachidziwa.

3 Kumbukirani am’nsinga, monga am’nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m’thupi.

4 Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.

5 Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

6 Kotero kuti tinena molimbika mtima,

Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa;

adzandichitira chiyani munthu?

7 Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.

8 YesuKhristuali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.

9 Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.

10 Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako.

11 Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m’malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.

12 Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.

13 Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake.

14 Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.

15 Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

16 Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.

17 Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.

18 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.

19 Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.

20 Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wachipanganochosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,

21 akuyeseni inu opanda chilema m’chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi.Amen.

22 Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule.

23 Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.

24 Perekani moni kwa atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akupatsani moni iwo a ku Italiya.

25 Chisomo chikhale ndi inu nonse, Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/13-6c22d691f3869cf94b3e09168362e92f.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Wolemba kalatayi alembera Akhristu achiyuda obalalika kumaiko osiyanasiyana. Apereka malangizo amitundumitundu owathandiza kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira ya Chikhristu. Aziwonetsa makhalidwe abwino pa zochita zao zonse, pakuti “chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.” (2.17)

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1

Za chikhulupiriro ndi nzeru 1.2-8

Za umphawi ndi chuma 1.9-11

Za kuyesedwa ndi zovuta kapena zinyengo 1.12-18

Za kumva ndi kuchita zimene Mulungu anena 1.19-27

Awachenjeza kuti asamachite tsankho 2.1-13

Za chikhulupiriro ndi ntchito zake 2.14-26

Za kuwongolera lilime potsata nzeru zochokera kumwamba 3.1-18

Za kuchita chibwenzi ndi pansi pano 4.1—5.6

Za kuyembekeza mopirira ndi kupempherera odwala 5.7-20

Categories
YAKOBO

YAKOBO 1

1 Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye YesuKhristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m’chibalaliko: ndikupatsani moni.

Za mayesero

2 Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu;

3 pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.

4 Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

5 Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

6 Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

7 Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;

8 munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha panjira zake zonse.

9 Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wake;

10 ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu.

11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m’mayendedwe ake.

12 Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.

13 Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:

14 koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.

15 Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.

16 Musanyengedwe, abale anga okondedwa.

17 Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

18 Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.

Tikhale akuchita a mau

19 Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.

20 Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.

21 Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.

22 Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

23 Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole;

24 pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani.

25 Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.

26 Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.

27 Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/1-2befdb6b7b5e71c1747b0e4d1087eeb5.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 2

Asachite tsankho pakati pa anthu

1 Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu YesuKhristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.

2 Pakuti akalowa m’sunagogemwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa;

3 ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;

4 kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

5 Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?

6 Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu?

7 Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?

8 Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:

9 koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa.

10 Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.

11 Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

12 Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.

13 Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Chikhulupiriro chopanda ntchito zake chikhala chopanda pake

14 Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa?

15 Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake,

16 ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?

17 Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.

18 Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m’ntchito zanga.

19 Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.

20 Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?

21 Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe?

22 Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro;

23 ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

24 Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.

25 Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina?

26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/2-292c9914e17fa02a3992da014148541a.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 3

Azichenjera ndi pakamwa pao

1 Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.

2 Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

3 Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m’kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.

4 Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nkutengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling’ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.

5 Kotero lilimenso lili chiwalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!

6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndiGehena.

7 Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam’nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;

8 koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

9 Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;

10 Mochokera m’kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.

11 Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa?

12 Kodi mkuyu ukhoza kubalaazitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.

Nzeru yochokera Kumwamba

13 Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.

14 Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.

15 Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.

16 Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.

17 Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.

18 Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/3-91e9b88f1bda5bdcf04695d91b72bb18.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 4

Adziletse polakalaka zoipa

1 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m’ziwalo zanu?

2 Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simungathe kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.

3 Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.

4 Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.

5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?

6 Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.

7 Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

8 Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.

9 Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

10 Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

11 Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.

12 Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

Sikudziwika ngati zidzachitika zofuna ifezi

13 Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;

14 inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.

15 Mukadanena inu, Akalola Ambuye, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.

16 Koma tsopano mudzitamandira m’kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.

17 Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/4-0097d69dd02d4537bb4a32eb9d733dec.mp3?version_id=1068—

Categories
YAKOBO

YAKOBO 5

Achuma ouma mtima atsutsidwa

1 Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.

2 Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete.

3 Golide wanu ndisilivawanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

4 Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m’minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m’makutu a Ambuye wa makamu.

5 Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha.

6 Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakaniza inu.

Apirire. Za kulumbira, kupemphera, kubweza wosochera

7 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.

8 Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.

9 Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

10 Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.

11 Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.

12 Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m’chiweruziro.

13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire.

14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu aMpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye:

15 ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.

16 Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m’machitidwe ake.

17 Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.

18 Ndipo anapempheranso; ndipo m’mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake.

19 Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake;

20 azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/5-ff1832cb27ea435e04dd90535a98e3ac.mp3?version_id=1068—