Kulangidwa kwa amitundu ena
1 Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;
2 ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Tiro ndi Sidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri.
3 Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundikasilivangati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo.
4 Taonani, Ambuye adzamlanda zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m’manja; ndipo adzatha ndi moto.
5 Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.
6 Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala mu Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.
7 Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m’kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko mu Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.
8 Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.
9 Kondwera kwambiri, mwana wamkazi waZiyoni; fuula mwana wamkazi waYerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
10 Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwaamitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.
11 Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m’dzenje m’mene mulibe madzi.
12 Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.
13 Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
14 Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.
15 Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe.
16 Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m’korona yakunyezimira padziko lake.
17 Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/9-d3b0e5262d121c9a64a8d58cfbe0db23.mp3?version_id=1068—