Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 8

Madalitso olonjezedwa ndi Mulungu

1 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

2 Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanjeZiyonindi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu.

3 Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati paYerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.

4 Atero Yehova wa makamu: M’miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m’dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake.

5 Ndi m’miseu ya mzinda mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akusewera m’miseu yake.

6 Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu.

7 Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m’dziko la kum’mawa, ndi m’dziko la kumadzulo;

8 ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m’kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m’choonadi ndi m’chilungamo.

9 Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe.

10 Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.

11 Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu.

12 Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.

13 Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwaamitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israele, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musaope, alimbike manja anu.

14 Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;

15 momwemonso ndinalingirira masiku ano kuchitira chokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa.

16 Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m’zipata zanu;

17 ndipo musalingirira choipa m’mtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.

18 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

19 Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.

20 Atero Yehova wa makamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m’mizinda yambiri adzafika,

21 ndi okhala m’mzinda umodzi adzamuka kumzinda wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.

22 Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.

23 Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/8-7943b914bf6b33accc8f7a991ede24b2.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *