Masomphenya achisanu ndi chitatu: magaleta anai
1 Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.
2 Ku galeta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi kugaleta wachiwiri akavalo akuda;
3 ndi kugaleta wachitatu a kavalo oyera; ndi kugaleta wachinai akavalo olimba amawanga.
4 Ndipo ndinayankha ndinati kwa mthenga wolankhula ndi ine, Izi nziyani, mbuyanga?
5 Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Galeta wa akavalo akuda atulukira kudziko la kumpoto; ndi oyerawo atulukira kuwatsata; ndi amawanga atulukira kudziko la kumwera.
7 Ndi amphamvuwo anatuluka nayesa kunka kuyendayenda m’dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m’dziko. Momwemo anayendayenda m’dziko.
8 Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m’dziko la kumpoto.
Akorona a Yoswa
9 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,
10 Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni,
11 ndipo utengesilivandi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe;
12 nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m’malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova:
13 inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri.
14 Ndipo akorona adzakhala wa Helidai, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Heni mwana wa Zefaniya, akhale chikumbutso mu Kachisi wa Yehova.
15 Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/6-6943f1ec7080e79cd0132cf692a2d81c.mp3?version_id=1068—