Masomphenya achisanu: choikaponyali chagolide ndi nyali zake
1 Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m’tulo take.
2 Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;
3 ndi mitengo iwiri yaazitonapomwepo, wina kudzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina kudzanja lake lamanzere.
4 Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziyani mbuyanga?
5 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.
6 Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.
7 Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.
8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,
9 Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu.
10 Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating’ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m’dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.
11 Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa choikaponyali nchiyani?
12 Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?
13 Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.
14 Pamenepo anati, Awa ndi ana aamuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/4-8c44396282dee4e72e15e44a9e3759e4.mp3?version_id=1068—