Masomphenya achitatu: Yerusalemu ayesedwa ndi chingwe
1 Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m’dzanja lake.
2 Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, KukayesaYerusalemu, kuona ngati chitando chake nchotani, ndi m’litali mwake motani.
3 Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anatuluka, ndi mthenga wina anatuluka kukomana naye,
4 nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m’midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.
5 Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m’kati mwake.
6 Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.
7 HayaZiyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babiloni.
8 Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwaamitunduamene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso lake.
9 Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.
10 Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.
11 Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.
12 Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m’dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.
13 Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/2-abdfe21c52da40c6a4c722e081e0afc0.mp3?version_id=1068—