Ukulu wa Israele m’tsogolo
1 Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele.
Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m’kati mwake;
2 Taonani, ndidzaikaYerusalemuakhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.
3 Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndiamitunduonse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.
4 Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo aliyense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.
5 Ndipo akalonga a Yuda adzanena m’mtima mwao, Okhala mu Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga mu Yehova wa makamu Mulungu wao.
6 Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m’malo mwake, mu Yerusalemu.
7 Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala mu Yerusalemu usakulire Yuda.
8 Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.
9 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu.
10 Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.
11 Tsiku lomwelo kudzakhala maliro aakulu mu Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m’chigwa cha Megido.
12 Ndipo dziko lidzalira, banja lililonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;
13 banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha;
14 mabanja onse otsala, banja lililonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/12-2118067be46e224f9ad6caa6e917a36b.mp3?version_id=1068—