Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 11

Kulangidwa kwa osalapa

1 Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.

2 Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi.

3 Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa.

4 Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa;

5 zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo.

6 Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m’dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m’dzanja la mnansi wake, ndi m’dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m’dzanja mwao sindidzawalanditsa.

7 M’mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.

8 Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.

9 Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; chilikufa chife; chosoweka chisoweke; ndi zotsala zidyane, chonse nyama ya chinzake.

10 Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu.

11 Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.

12 Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli asilivamakumi atatu.

13 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m’nyumba ya Yehova.

14 Pamenepo ndinadula ndodo yanga ina, ndiyo Chomanganitsa, kuti ndithetse chibale cha pakati pa Yuda ndi Israele.

15 Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa.

16 Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m’dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang’amba ziboda zao.

17 Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/11-c561b50ce92666c22592fbac7470bb2b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *