Categories
ZEKARIYA

ZEKARIYA 1

Mneneri adandaulira anthu Ayuda aleke zoipa zao

1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Idomneneri, ndi kuti,

2 Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.

3 Chifukwa chake uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu.

4 Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova.

5 Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi?

6 Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.

Masomphenya oyamba: akavalo

7 Tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wakhumi ndi chimodzi, ndiwo mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,

8 Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.

9 Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani.

10 Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m’dziko.

11 Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m’dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula.

12 Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundoYerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?

13 Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima.

14 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, fuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndiZiyonindi nsanje yaikulu.

15 Ndipo ndikwiya naoamitunduokhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang’ono, ndipo anathandizira choipa.

16 Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.

17 Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.

Masomphenya achiwiri: nyanga zinai ndi osula anai

18 Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.

19 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.

20 Ndipo Yehova anandionetsa osula anai.

21 Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEC/1-f5510f91626ffadd7875a2ee85142e76.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *