Categories
YOSWA

YOSWA 9

Yoswa anyengedwa ndi Agibiyoni napangana nao

1 Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

2 anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israele, ndi mtima umodzi.

3 Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,

4 zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong’ambika ndi omangamanga;

5 ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, ndipo zinavala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

6 Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, ndipo zinati kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe.

7 Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?

8 Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? Ndipo mufuma kuti?

9 Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,

10 ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.

11 Ndipo akulu athu ndi nzika zonse za m’dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m’dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe.

12 Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m’nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu;

13 ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang’ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.

14 Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.

15 Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira.

16 Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao.

17 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.

18 Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga.

19 Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israele, m’mwemo sitikhoza kuwachitira kanthu.

20 Tidzawachitira ichi, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo chifukwa cha lumbirolo tidawalumbirira.

21 Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao.

22 Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga chifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutalitali ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife?

23 Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.

24 Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m’dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.

25 Ndipo tsopano, taonani, tili m’dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani.

26 Pamenepo anawachitira chotero, nawalanditsa m’dzanja la ana a Israele, angawaphe.

27 Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/9-6ddc3c83cb92b6e3fc44a6c80cb24380.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *