Autsa chihema ku Silo
1 Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komwekochihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.
2 Ndipo anatsala mwa ana a Israele mafuko asanu ndi awiri osawagawira cholowa chao.
3 Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Muchedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani?
4 Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati padziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine.
5 Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m’malire ake kumwera, ndi a m’nyumba ya Yosefe adzakhala m’malire mwao kumpoto.
6 Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu.
7 Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum’mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.
8 Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati padziko, ndi kulilemba, nimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova pa Silo.
9 Namuka amunawo, napitapita pakati padziko, nalilemba m’buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo.
10 Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.
Malire a Benjamini
11 Ndipo maere a fuko la ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anatuluka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.
12 Ndipo malire ao a kumpoto anachokera ku Yordani; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi matulukiro ake anali ku chipululu cha Betaveni.
13 Ndipo malire anapitirirapo kunka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Betele, kumwera; ndi malire anatsikira kunka ku Ataroti-Adara, kuphiri lokhala kumwera kwa Betehoroni wa kunsi.
14 Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mzinda wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.
15 Ndipo mbali ya kumwera inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; natuluka malire kunka kumadzulo, natuluka kunka ku chitsime cha madzi a Nefitowa;
16 natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m’chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele;
17 nalembedwa kunka kumpoto, natuluka ku Enisemesi, natuluka ku Geliloti, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumimu; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
18 napitirira ku mbali ya pandunji pa Betaraba kumpoto, natsirika kunka ku Araba;
19 napitirira malire kunka ku mbali ya Betehogila kumpoto; ndi matulukiro ake a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mchere; pa kulekezera kwa kumwera kwa Yordani; ndiwo malire a kumwera.
20 Ndipo malire ake mbali ya kum’mawa ndiwo Yordani, ndicho cholowa cha ana a Benjamini, kunena za malire ake pozungulira pake, monga mwa mabanja ao.
21 Koma mizinda ya fuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Betehogila, ndi Emekezizi;
22 ndi Betaraba, ndi Zemaraimu, ndi Betele;
23 ndi Avimu ndi Para, ndi Ofura;
24 ndi Kefaramoni, ndi Ofini, ndi Geba; mizinda khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yao;
25 Gibiyoni ndi Rama, ndi Beeroti;
26 ndi Mizipa, ndi Kefira, ndi Moza;
27 ndi Rekemu, ndi Iripele ndi Tarala;
28 ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndiYerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/18-c6ad6a4457f16f0b75bc1868bb2d6739.mp3?version_id=1068—