Categories
YOSWA

YOSWA 17

Malire a Manase

1 Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.

2 Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.

3 Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

4 Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.

5 Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani:

6 popeza ana aakazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake aamuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala.

7 Ndipo malire a Manase anayambira ku Asere, kunka ku Mikametati, wokhala chakuno cha Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapuwa.

8 Dziko la Tapuwa linali la Manase; koma Tapuwa mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efuremu.

9 Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; mizinda iyi inakhala ya Efuremu pakati pa mizinda ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndi matulukiro ake anali kunyanja;

10 kumwera nkwa Efuremu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ake ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Asere, ndi kum’mawa anakomana ndi Isakara.

11 Ndipo mu Isakara ndi mu Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.

12 Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m’mizinda aja, popeza Akanani anafuna kukhala m’dziko lija.

13 Ndipo kunali pamene ana a Israele atakula mphamvu anasonkhetsa Akanani osawaingitsa onse.

14 Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?

15 Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m’dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu.

16 Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m’dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala mu Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m’chigwa cha Yezireele.

17 Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m’nyumba ya Yosefe, kwa Efuremu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikulu; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha;

18 koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi matulukiro ake adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magaleta achitsulo, angakhale ali amphamvu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/17-30824d478415cf4fe846c84c28ca4e27.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *