Categories
YONA

YONA 4

Kudandaula kwa Yona, kumdzudzula kwa Mulungu

1 Koma sikudakomere Yona konse, ndipo anapsa mtima.

2 Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m’dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.

3 Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.

4 Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?

5 Pamenepo Yona anatuluka m’mzinda, nakhala pansi kum’mawa kwa mzinda, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mzinda.

6 Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m’nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.

7 Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m’mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota.

8 Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum’mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.

9 Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

10 Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirepo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

11 ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m’mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JON/4-564daa16dc68aaf72129c732994fd76f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *