Achiritsidwa munthu wosaona chibadwire
1 Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire.
2 Ndipoophunziraake anamfunsa Iye, nanena,Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona?
3 Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.
4 Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.
5 Pakukhala Ine m’dziko lapansi, ndili kuunika kwa dziko lapansi.
6 Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m’maso,
7 nati kwa iye, Muka, kasambe m’thamanda la Siloamu (ndilo losandulika, Wotumidwa). Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona.
8 Chifukwa chake anzake ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?
9 Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene.
10 Pamenepo anenana ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji?
11 Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m’maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m’mene ndinasamba ndinapenya.
12 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.
13 Anapita naye amene anali wosaona kale kwaAfarisi.
14 Koma tsikulo ndi laSabatalimene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ake.
15 Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera. Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m’maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.
16 Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.
17 Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, AliMneneri.
18 Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya;
19 nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona?
20 Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wake ndi amake anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona;
21 koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.
22 Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiyeKhristu, akhale woletsedwa m’sunagoge.
23 Chifukwa cha ichi atate wake ndi amake anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye.
24 Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.
25 Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya.
26 Chifukwa chake anati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji?
27 Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamve; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala ophunzira ake?
28 Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife ophunzira a Iyeyu, ife ndife ophunzira a Mose.
29 Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo.
30 Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m’menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.
31 Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.
32 Kuyambira pachiyambi sikunamveke kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire.
33 Ngati uyu sanachokere kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.
34 Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m’zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.
35 Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupiriraMwana wa Munthu?
36 Iyeyu anayankha nati, Ndipo ndani Iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire Iye?
37 Yesu anati kwa iye, Wamuona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo.
38 Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira Iye.
39 Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.
40 Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye anamva izi, nati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osaona?
41 Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/9-c2efc42050d0cd8b4e5e9ce8b76efca3.mp3?version_id=1068—