Za mkazi wachigololo
1 Koma Yesu anamuka kuphiri la Azitona.
2 Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m’mene anakhala pansi anawaphunzitsa.
3 Koma alembi ndiAfarisianabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m’chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,
4 ananena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkuchita chigololo.
5 Koma m’chilamulo Mose anatilamula, tiwaponye miyala otere. Chifukwa chake Inu munena chiyani za iye?
6 Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m’mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.
7 Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.
8 Ndipo m’mene adaweramanso analemba ndi chala chake pansi.
9 Koma iwo, m’mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.
10 Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?
11 Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.
Yesu wotumidwa ndi Atate
12 Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.
13 Chifukwa chake Afarisi anati kwa Iye, Muchita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona.
14 Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.
15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.
16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruziro changa chili choona; pakuti sindili pa ndekha, koma Ine ndi Atate amene anandituma Ine.
17 Inde kudalembedwa m’chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli woona.
18 Ine ndine wakuchita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine achita umboni wa Ine.
19 Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.
20 Mau awa analankhula m’nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.
21 Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m’tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.
22 Chifukwa chake Ayuda anenana, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?
23 Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.
24 Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m’machimo kwa inu, kuti mudzafa m’machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m’machimo anu.
25 Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.
26 Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.
27 Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.
28 Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkwezaMwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.
29 Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.
30 Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye.
31 Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m’mau anga, muliophunziraanga ndithu;
32 ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.
33 Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhale akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu?
34 Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.
35 Koma kapolo sakhala m’nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.
36 Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.
37 Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu.
38 Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu.
39 Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.
40 Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite.
41 Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwe ife m’chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.
42 Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadze kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.
43 Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga.
44 Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.
45 Koma Ine, chifukwa ndinena choonadi, simukhulupirira Ine.
46 Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?
47 Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.
48 Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinuMsamariya, ndipo muli ndi chiwanda?
49 Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.
50 Koma Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.
51 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.
52 Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.
53 Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?
54 Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;
55 ndipo inu simunamdziwe Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake.
56 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona nasangalala.
57 Ayuda pamenepo anati kwa Iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?
58 Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.
59 Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/8-98cef08d3bf9da2b376256f706101014.mp3?version_id=1068—