Yesu achulukitsa mikate
1 Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.
2 Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.
3 Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndiophunziraake.
4 NdipoPaska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira.
5 Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?
6 Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita.
7 Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang’ono.
8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,
9 Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?
10 Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.
11 Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.
12 Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.
13 Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo.
14 Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiyemnenerindithu wakudzayo m’dziko lapansi.
15 Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.
Yesu ayenda panyanja
16 Koma pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira kunyanja;
17 ndipo pamene adalowa m’ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.
18 Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako.
19 Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.
20 Koma Iye ananena nao, Ndine; musaope.
21 Pamenepo analola kumlandira m’ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.
Yesu mkate wamoyo wa okhulupirira
22 M’mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m’ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha;
23 koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m’mene Ambuye Yesu adayamika;
24 chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m’ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.
25 Ndipo pamene anampeza Iye tsidya lina la nyanja, anati kwa Iye,Rabi, munadza kuno liti?
26 Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.
27 Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimeneMwana wa Munthuadzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
28 Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?
29 Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.
30 Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?
31 Atate athu anadyamanam’chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m’mwamba anawapatsa iwo kudya.
32 Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.
33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.
34 Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.
35 Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
36 Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.
37 Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.
38 Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.
39 Koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti za ichi chonse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza.
40 Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
41 Chifukwa chake Ayuda anang’ung’udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.
42 Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?
43 Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang’ung’udze wina ndi mnzake.
44 Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
45 Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.
46 Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.
47 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha.
48 Ine ndine mkate wamoyo.
49 Makolo anu adadya m’chipululu, ndipo adamwalira.
50 Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira.
51 Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.
52 Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?
53 Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.
54 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
55 Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.
56 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.
57 Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.
58 Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.
59 Izi ananena m’sunagoge, pakuphunzitsa mu Kapernao.
Ophunzira ambiri aleka kutsata Yesu
60 Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?
61 Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung’ung’udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?
62 Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?
63 Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.
64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.
65 Ndipo ananena, Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.
Chivomerezo cha Petro
66 Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye.
67 Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka?
68 Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.
69 Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.
70 Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?
71 Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/6-3a0ee6223a373a174fa399efa56fb215.mp3?version_id=1068—