Categories
YOHANE

YOHANE 19

1 Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.

2 Ndipo asilikali, m’mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa;

3 nadza kwa Iye, nanena, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Nampanda khofu.

4 Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.

5 Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!

6 Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.

7 Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.

8 Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa.

9 Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.

10 Chifukwa chake Pilato ananena kwa Iye, Simulankhula ndi ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndili nao wakukumasulani, ndipo ndili nao ulamuliro wakukupachikani?

11 Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.

12 Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi laKaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.

13 Pamenepo Pilato, m’mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma mu Chihebri, Gabata.

14 Koma linali tsiku lokonzaPaska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu!

15 Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.

16 Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike.

Ampachika Yesu pamtanda

Pamenepo anatenga Yesu;

17 ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa mu Chihebri, Gologota:

18 kumene anampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, chakuno ndi chauko, koma Yesu pakati.

19 Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.

20 Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mzindawo; ndipo linalembedwa mu Chihebri, ndi mu Chilatini, ndi mu Chigriki.

21 Pamenepo ansembe aakulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndili mfumu ya Ayuda.

22 Pilato anayankha, Chimene ndalemba, ndalemba.

23 Pamenepo asilikali, m’mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko.

24 Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang’ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi.

25 Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.

26 Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunziraamene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu!

27 Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.

Yesu afa pamtanda

28 Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.

29 Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi lahisope, nachifikitsa kukamwa kwake.

30 Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.

Sathyola miyendo ya Yesu

31 Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe.

32 Chifukwa chake anadza asilikali nathyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopachikidwa pamodzi ndi Iye;

33 koma pofika kwa Yesu, m’mene anamuona Iye, kuti wafa kale, sanathyole miyendo yake;

34 koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m’nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.

35 Ndipo iye amene anaona, wachita umboni, ndi umboni wake uli woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupirire.

36 Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa.

37 Ndipo linenanso lembo lina, Adzayang’ana pa Iye amene anampyoza.

Kuikidwa kwa Yesu

38 Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake.

39 Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisakanizo chamurendi aloe, monga miyeso zana.

40 Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.

41 Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m’mundamo munali manda atsopano m’mene sanaikidwemo munthu aliyense nthawi zonse.

42 Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/19-67d413f75a0a4afcb034097e8ceb475c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *