Categories
YOHANE

YOHANE 17

Yesu apempherera ophunzira ake

1 Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m’mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;

2 monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.

3 Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi YesuKhristuamene munamtuma.

4 Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m’mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.

5 Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.

6 Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m’dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.

7 Azindikira tsopano kuti zinthu zilizonse zimene mwandipatsa Ine zichokera kwa Inu;

8 chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine.

9 Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine,

10 chifukwa ali anu: ndipo zanga zonse zili zanu, ndi zanu zili zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo.

11 Sindikhalanso m’dziko lapansi, koma iwo ali m’dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m’dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.

12 Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m’dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.

13 Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m’dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha.

14 Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.

15 Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.

16 Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.

17 Patulani iwo m’choonadi; mau anu ndi choonadi.

18 Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo kudziko lapansi.

19 Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m’choonadi.

20 Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mau ao;

21 kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.

22 Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tili mmodzi;

23 Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.

24 Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.

25 Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine;

26 ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/17-d24043e80e76ebc6264a063e5a768ae6.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *