Categories
YOHANE

YOHANE 13

Yesu asambitsa mapazi a anyamata ake

1 Koma pasanafike chikondwerero laPaska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m’mene anakonda ake a Iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.

2 Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,

3 Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m’manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,

4 ananyamuka pamgonero, navula malaya ake; ndipo m’mene adatenga chopukutira, anadzimanga m’chuuno.

5 Pomwepo anathira madzi m’beseni, nayamba kusambitsa mapazi aophunziraake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.

6 Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?

7 Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwake.

8 Petro ananena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga kunthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine.

9 Simoni Petro ananena ndi Iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu.

10 Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.

11 Pakuti anadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi anati, Simuli oyera nonse.

12 Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi?

13 Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

14 Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.

15 Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.

16 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye.

17 Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.

18 Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.

19 Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.

20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira aliyense amene ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.

Yesu aneneratu kuti Yudasi adzampereka

21 Yesu m’mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22 Ophunzira analikupenyana wina kwa mnzake, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani.

23 Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.

24 Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.

25 Iyeyu potsamira pomwepo, pa chifukwa cha Yesu, anena ndi Iye, Ambuye, ndiye yani?

26 Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m’mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.

27 Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo,Satanaanalowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.

28 Koma palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa chimene anafuna, poti atere naye.

29 Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.

30 Pamenepo iyeyo m’mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku.

31 Tsono m’mene adatuluka, Yesu ananena, Tsopano walemekezekaMwana wa Munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa Iye;

32 ndipo Mulungu adzamlemekeza Iye mwa Iye yekha, adzamlemekeza Iye tsopano apa.

33 Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.

34 Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.

35 Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.

Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana

36 Simoni Petro anena ndi Iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, udzanditsata bwino lomwe.

37 Petro ananena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu.

38 Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/13-1a9da6e94b820b49a9bac217ef84589d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *