Categories
YOHANE

YOHANE 12

Maria adzoza mapazi a Yesu

1 Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafikePaska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.

2 Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye.

3 Pamenepo Maria m’mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino anaridoweniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.

4 Koma Yudasi Iskariote, mmodzi waophunziraake, amene adzampereka Iye, ananena,

5 Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwe chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?

6 Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.

7 Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga.

8 Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

9 Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.

10 Koma ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso;

11 pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.

Yesu alowa mu Yerusalemu

12 M’mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza kuYerusalemu,

13 anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m’dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele.

14 Koma Yesu, m’mene adapeza kabulu anakhala pamenepo; monga mulembedwa:

15 Usaope, mwana wamkazi waZiyoni; taona mfumu yako idza wokhala pa mwana wa bulu.

16 Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.

17 Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m’mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni.

18 Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.

19 Chifukwa chakeAfarisiananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.

Agriki afuna kuona Yesu; Iye ayankhapo

20 Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero.

21 Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.

22 Filipo anadza nanena kwa Andrea; nadza Andrea ndi Filipo, nanena ndi Yesu.

23 Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kutiMwana wa Munthualemekezedwe.

24 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m’nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.

25 Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha.

26 Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.

27 Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.

28 Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.

29 Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena,Mngelowalankhula ndi Iye.

30 Yesu anayankha nati, Mau awa sanafike chifukwa cha Ine, koma cha inu.

31 Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.

32 Ndipo Ine, m’mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.

33 Koma ananena ichi ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.

34 Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m’chilamulo kutiKhristuakhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani?

35 Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang’ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.

36 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira.

37 Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;

38 kuti mau a Yesayamneneriakakwaniridwe, amene anati,

Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?

Ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?

39 Chifukwa cha ichi sanathe kukhulupirira, pakuti Yesaya anatinso,

40 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;

kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,

nangatembenuke,

ndipo ndingawachiritse.

41 Izi anati Yesaya, chifukwa anaona ulemerero wake; nalankhula za Iye.

42 Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m’sunagoge,

43 pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.

44 Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine.

45 Ndipo wondiona Ine aona amene anandituma Ine.

46 Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.

47 Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadze kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.

48 Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.

49 Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.

50 Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake lili moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/12-1f37420411c52cd5e734bf7b45793ec3.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *