Chiukitso cha Lazaro
1 Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m’mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita.
2 Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.
3 Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.
4 Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.
5 Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro.
6 Chifukwa chake pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pamalo pomwepo masiku awiri.
7 Ndipo pambuyo pake ananena kwaophunziraake, Tiyeni tipitenso ku Yudeya.
8 Ophunzira ananena ndi Iye,Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?
9 Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi.
10 Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye.
11 Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.
12 Chifukwa chake ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira.
13 Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.
14 Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.
15 Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.
16 Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.
17 Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m’manda masiku anai.
18 Koma Betaniya anali pafupi paYerusalemu, nthawi yake yonga ya mastadiya khumi ndi asanu;
19 koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.
20 Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi Iye; koma Maria anakhalabe m’nyumba.
21 Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.
22 Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu.
23 Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka.
24 Marita ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.
25 Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;
26 ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?
27 Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinuKhristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m’dziko lapansi.
28 Ndipo m’mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m’tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.
29 Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa Iye.
30 (Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye.)
31 Pamenepo Ayuda okhala naye m’nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.
32 Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m’mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.
33 Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,
34 nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni mukaone.
35 Yesu analira.
36 Chifukwa chake Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!
37 Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sakanatha kodi kuchita kuti asafe ameneyunso?
38 Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.
39 Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.
40 Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?
41 Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.
42 Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
43 Ndipo m’mene adanena izi, anafuula ndi mau aakulu, Lazaro, tuluka.
44 Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
45 Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m’mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.
46 Koma ena a mwa iwo anamuka kwaAfarisi, nawauza zimene Yesu adazichita.
Afarisi apangana za kupha Yesu
47 Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.
48 Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.
49 Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu,
50 kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke.
51 Koma ichi sananene kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho ananenera kuti Yesu adzafera mtunduwo;
52 ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo.
53 Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye.
54 Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.
55 KomaPaskawa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.
56 Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzake poimirira iwo mu Kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuchikondwerero kodi?
57 Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/11-e85eeb5710066782c0432fec7c6911ee.mp3?version_id=1068—