Categories
YOBU

YOBU 8

Poona tsoka lao Bilidadi akuti Yobu ndi ana ake anachimwa, anena mofanizira

1 Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,

2 Udzanena izi kufikira liti?

Ndipo mau a pakamwa pako

adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

3 Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo?

Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?

4 Chinkana ana ako anamchimwira Iye,

ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;

5 koma ukafunitsitsa Mulungu,

ndi kupembedza Wamphamvuyonse;

6 ukakhala woyera ndi woongoka mtima,

zoonadi adzakugalamukira tsopano,

ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.

7 Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching’ono,

chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.

8 Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo,

nusamalire zimene makolo ao adazisanthula.

9 Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,

popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10 amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,

ndi kutulutsa mau a mumtima mwao?

11 Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho?

Ngati manchedza amera popanda madzi?

12 Akali auwisi, sanawacheke,

auma, asanaume mathengo onse ena.

13 Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;

ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.

14 Kulimbika mtima kwake kudzathyoka,

chikhulupiriro chake chikunga nyumba ya kangaude.

15 Adzatsamira nyumba yake, koma yosamlimbira;

adzaiumirira koma yosakhalitsa.

16 Akhala wamuwisi pali dzuwa,

ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake.

17 Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi,

apenyerera pokhalapo miyala.

18 Akamuononga kumchotsa pamalo pake,

padzamkana, ndi kuti, Sindinakuone.

19 Taona, ichi ndicho chomkondweretsa panjira pake,

ndi panthaka padzamera ena.

20 Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro;

kapena kugwiriziza ochita zoipa.

21 Koma adzadzaza m’kamwa mwako ndi kuseka,

ndi milomo yako kufuula.

22 Iwo akudana nawe adzavala manyazi;

ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/8-cc0837d44517aafd54c6f9308f29da7c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *