Categories
YOBU

YOBU 5

1 Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi?

Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?

2 Pakuti mkwiyo umapha wopusa,

ndi nsanje imakantha wopanda pake.

3 Ndinapenya wopusa woyala mizu;

koma pomwepo ndinatemberera pokhala pake.

4 Ana ake akhala otekeseka,

napsinjika kuchipata,

wopanda wina wakuwapulumutsa.

5 Zokolola zao anjala azidya,

azitenga ngakhale kuminga,

ndi aludzu ameza chuma chao.

6 Pakuti nsautso sutuluka m’fumbi,

ndi mavuto saphuka m’nthaka.

7 Koma munthu abadwira mavuto,

monga mbaliwali zikwera ziuluzika.

8 Koma ine ndikadafuna Mulungu,

ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;

9 amene achita zazikulu ndi zosalondoleka,

zinthu zodabwitsa zosawerengeka.

10 Amene avumbitsa mvula panthaka,

natumiza madzi paminda;

11 kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka,

kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka.

12 Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera,

kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.

13 Akola eni nzeru m’kuchenjera kwao,

ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe.

14 Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa,

nayambasa dzuwa lili pakati pamutu monga usiku.

15 Apulumutsa aumphawi kulupanga

la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu.

16 Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo,

ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.

17 Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula;

chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.

18 Pakuti apweteka, namanganso mabala;

alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.

19 Adzakupulumutsa m’masautso asanu ndi limodzi;

chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.

20 Adzakuombola kuimfa m’njala,

ndi kumphamvu ya lupanga m’nkhondo.

21 Udzabisikira mkwapulo wa lilime,

sudzachiopanso chikadza chipasuko.

22 Chipasuko ndi njala udzaziseka;

ngakhale zilombo za padziko osaziopa.

23 Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala yakuthengo;

ndi nyama zakuthengo zidzakhala nawe mumtendere.

24 Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere;

nudzazonda za m’banja mwako osasowapo kanthu.

25 Udzapezanso kuti mbeu zako zidzachuluka,

ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.

26 Udzafika kumanda utakalamba,

monga abwera nao mtolo wa tirigu m’nyengo yake.

27 Taona, ichi tachifunafuna, chili chotero;

uchimvere, nuchidziwire wekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/5-35f8439fd0bb1a9554af3b9fdb4ba2a9.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *