Categories
YOBU

YOBU 36

Elihu alemekeza chilungamo ndi mphamvu ya Mulungu. Mulungu ndi wangwiro, ife tilephera kumdziwa

1 Elihu anabwereza, nati,

2 Mundilole pang’ono, ndidzakuuzani,

pakuti ndili naonso mau akunenera Mulungu.

3 Ndidzatenga nzeru zanga kutali,

ndidzavomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama.

4 Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza,

wakudziwitsa mwangwiro ali nanu.

5 Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu,

ndipo sapeputsa munthu;

mphamvu ya nzeru zake ndi yaikulu.

6 Sasunga woipa akhale ndi moyo,

koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo.

7 Sawachotsera wolungama maso ake,

koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao

awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.

8 Ndipo akamangidwa m’nsinga,

nakakodwa ndi zingwe za mazunzo,

9 pamenepo awafotokozera ntchito zao,

ndi zolakwa zao, kuti anachita modzikuza.

10 Awatseguliranso m’khutu mwao kuti awalangize,

nawauza abwerere kuleka mphulupulu.

11 Akamvera ndi kumtumikira,

adzatsiriza masiku ao modala,

ndi zaka zao mokondwera.

12 Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga,

nadzatsirizika osadziwa kanthu.

13 Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo,

akawamanga Iye, safuulira.

14 Iwowa akufa akali biriwiri,

ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.

15 Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwake,

nawatsegulira m’khutu mwao mwa kupsinjika kwao.

16 Inde akadakukopani muchoke posaukira,

mulowe kuchitando kopanda chopsinja;

ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.

17 Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa,

zolingirirazo ndi chiweruzo zidzakugwiranibe.

18 Pakuti muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo;

ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.

19 Chuma chanu chidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,

kapena mphamvu yanu yonse yolimba?

20 Musakhumbe usiku,

umene anthu alikhidwe m’malo mwao.

21 Chenjerani, musalunjike kumphulupulu;

pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22 Taonani, Mulungu achita mokwezeka mu mphamvu yake,

mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23 Anamuikira njira yake ndani?

Adzati ndani, Mwachita chosalungama?

24 Kumbukirani kuti mukuze ntchito zake

zimene anaziimbira anthu.

25 Anthu onse azipenyerera,

anthu aziyang’anira kutali.

26 Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa;

chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.

27 Pakuti akweza madontho a mvula,

akhetsa mvula ya m’nkhungu yake

28 imene mitambo itsanulira,

nivumbitsira anthu mochuluka.

29 Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo,

ndi kugunda kwa msasa wake?

30 Taonani, Iye ayala kuunika kwake pamenepo.

Navundikira kunsi kwake kwa nyanja.

31 Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu

apatsa chakudya chochuluka.

32 Akutidwa manja ake ndi mphezi,

nailamulira igwere pofunapo Iye.

33 Kugunda kwake kulalikira za Iye,

zoweta zomwe zilota mtambo woyandikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/36-1c16f54b203c3f942c688ddc1bba0cc8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *