Categories
YOBU

YOBU 34

Elihu anenetsa Mulungu sangathe kukhala wosalungama, koma asiyanitsa pakati pa okoma ndi oipa

1 Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,

2 Tamverani mau anga, inu anzeru;

munditcherere khutu inu akudziwa.

3 Pakuti khutu liyesa mau,

monga m’kamwa mulawa chakudya.

4 Tidzisankhire choyeneracho,

tidziwe mwa tokha chokomacho.

5 Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,

ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine

6 Kodi ndidzinamizire?

Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwe.

7 Wakunga Yobu ndani,

wakumwa mwano ngati madzi?

8 Wakutsagana nao ochita mphulupulu,

nayendayenda nao anthu oipa.

9 Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako

kuvomerezana naye Mulungu.

10 Chifukwa chake mundimvere ine, eni nzeru inu,

nkutali ndi Mulungu kuchita choipa,

ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.

11 Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake,

napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake.

12 Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa,

ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.

13 Anamuikiza dziko lapansi ndani?

Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?

14 Akadzikumbukira yekha mumtima mwake,

akadzisonkhanitsira yekha mzimu wake ndi mpweya wake,

15 zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,

ndi munthu adzabwerera kufumbi.

16 Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ichi,

Tcherera khutu kunena kwanga.

17 Kodi munthu woipidwa nacho chiweruzo adzalamulira?

Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?

18 Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pake iwe,

kapena kwa akalonga, Oipa inu?

19 Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga,

wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka?

Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.

20 M’kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku,

anthu agwedezeka, napita,

amphamvu achotsedwa opanda dzanja lakuwachotsa.

21 Pakuti maso ake ali panjira ya munthu aliyense,

napenya moponda mwake monse.

22 Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa,

kuti ochita zopanda pake abisaleko.

23 Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu,

kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa.

24 Aphwanya eni mphamvu osatulutsa kubwalo mlandu wao,

naika ena m’malo mwao.

25 Pakuti asamalira ntchito zao,

nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.

26 Awakantha ngati oipa,

poyera pamaso pa anthu,

27 popeza anapatuka, naleka kumtsata,

osasamalira njira zake zilizonse.

28 M’mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka;

ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika.

29 Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani?

Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani?

Chikachitika pa mtundu wa anthu,

kapena pa munthu, nchimodzimodzi;

30 kuti munthu wonyoza Mulungu asachite ufumu,

ndi anthu asakodwe mumsampha.

31 Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu,

ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwe?

32 Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu,

ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.

33 Kodi chilango cha Mulungu chikhale

monga muchifuna inu, pakuti muchikana?

Musankhe ndi inu, ine ai;

m’mwemo monga mudziwa, nenani.

34 Anthu ozindikira adzanena nane,

inde anthu anzeru onse akundimva adzati,

35 Yobu alankhula wopanda kudziwa,

ndi mau ake alibe nzeru.

36 Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha,

chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu.

37 Pakuti pa kuchimwa kwake aonjeza kupikisana ndi Mulungu,

asansa manja pakati pa ife,

nachulukitsa maneno ake pa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/34-6b3962972c96bad768116d55d4bd9aa8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *