1 Ndinapangana ndi maso anga,
potero ndipenyerenji namwali?
2 Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba,
ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m’mwambamo nchiyani?
3 Si ndizo chionongeko cha wosalungama,
ndi tsoka la ochita mphulupulu?
4 Nanga sapenya njira zanga,
ndi kuwerenga moponda mwanga monse?
5 Ngati ndinayanjana nalo bodza,
ndi phazi langa linathamangira chinyengo;
6 andiyese ndi muyeso wolingana,
kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.
7 Ngati phazi langa linapatuka m’njira,
ndi mtima wanga unatsata maso anga?
Ngati chilema chamamatira manja anga?
8 Ndibzale ine nadye wina,
ndi zondimerera ine zizulidwe.
9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,
ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,
10 mkazi wanga aperere wina;
wina namuike kumbuyo.
11 Pakuti icho ndi choipitsitsa,
ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.
12 Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko,
ndi chakuzula zipatso zanga zonse.
13 Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga,
kapena wa mdzakazi wanga,
potsutsana nane iwo,
14 ndidzatani ponyamuka Mulungu?
Ndipo pondizonda Iye ndidzamnyankha chiyani?
15 Kodi Iye amene anandilenga ine m’mimba
sanamlenge iyenso?
Sindiye mmodzi anatiumba m’mimba?
16 Ngati ndakaniza aumphawi chifuniro chao,
kapena kutopetsa maso a amasiye,
17 kapena kudya nthongo yanga ndekha,
osadyako mwana wamasiye;
18 (pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa
ndi ine monga ndi atate;
ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.)
19 Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda chovala,
kapena kuti wosowa alibe chofunda;
20 ngati ziuno zake sizinandiyamike,
ngati sanafunde ubweya wa nkhosa zanga;
21 ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,
popeza ndinaona thandizo langa kuchipata;
22 libanthuke phewa langa paphalo,
ndi dzanja langa liduke pagwangwa.
23 Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa,
ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.
24 Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa,
ndi kunena ndi golide woyengetsa,
ndiwe chikhazikitso changa;
25 ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu,
ndi dzanja langa lapeza zochuluka;
26 ngati ndalambira dzuwa lilikuwala,
kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;
27 ndi mtima wanga wakopeka m’tseri,
ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;
28 ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza
kunena mlandu wake;
pakuti ndikadakana Mulungu ali m’mwamba.
29 Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,
kapena kudzitukula pompeza choipa;
30 ndithu sindinalole m’kamwa mwanga muchimwe,
kupempha motemberera moyo wake.
31 Ngati amuna a m’hema mwanga sanati,
ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?
32 Mlendo sakagona pakhwalala,
koma ndinatsegulira wam’njira pakhomo panga.
33 Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu,
ndi kubisa mphulupulu yanga m’chifuwa mwanga;
34 popeza ndinaopa unyinji waukulu,
ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa;
potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga.
35 Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera,
chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe;
mwenzi ntakhala nao mau akundineneza
analemberawo mdani wanga!
36 Ndithu ndikadawasenza paphewa panga,
ndi kudzimangirira awa ngati korona.
37 Ndikadamfotokozera chiwerengo cha mopondamo mwanga,
ndikadamsenderera Iye ngati kalonga.
38 Ngati minda yanga ifuula monditsutsa,
ndi nthumbira zake zilira pamodzi;
39 ngati ndadya zipatso zake wopanda ndalama.
Kapena kutayitsa eni ake moyo wao;
40 imere minga m’malo mwa tirigu,
ndi dawi m’malo mwa barele.
Mau a Yobu atha.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/31-b4d82b61b735a2c350eea6591b10e9dd.mp3?version_id=1068—