Categories
YOBU

YOBU 30

1 Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka,

iwo amene atate ao ndikadawapeputsa,

osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.

2 Mphamvunso ya m’manja mwao ndikadapindulanji nayo?

Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha,

3 atsala mafupa okhaokha ndi kusowa ndi njala;

akungudza nthaka youma kuli mdima wa m’chipululu chopasuka.

4 Atchera therere lokolera kuzitsamba,

ndi chakudya chao ndicho mizu ya dinde.

5 Anawapirikitsa pakati pa anthu,

awafuulira ngati kutsata mbala.

6 Azikhala m’zigwa za chizirezire,

m’maenje a m’nthaka ndi m’mapanga.

7 Pakati pa zitsamba alira ngati bulu,

pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.

8 Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;

anawaingitsa kuwachotsa m’dziko.

9 Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo,

nandiyesa chitonzo.

10 Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine,

saleka kuthira malovu pankhope panga.

11 Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza;

anataya chomangira m’kamwa mwao pamaso panga.

12 Kudzanja langa lamanja anauka oluluka,

akankha mapazi anga,

andiundira njira zao zakundiononga.

13 Aipsa njira yanga,

athandizana ndi tsoka langa;

ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.

14 Akudza ngati opitira pogamuka linga papakulu,

pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine.

15 Anditembenuzira zondiopsa,

auluza ulemu wanga ngati mphepo;

ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.

16 Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m’kati mwanga;

masiku akuzunza andigwira.

17 Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine,

ndi zowawa zondikungudza sizipuma.

18 Mwa mphamvu yaikulu ya nthenda yanga

chovala changa chinasandulika,

chindithina ngati pakhosi pa malaya anga.

19 Iye anandiponya m’matope,

ndipo ndafanana ndi fumbi ndi phulusa.

20 Ndifuula kwa Inu, koma simundiyankha;

ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.

21 Mwasandulika kundichitira nkharwe;

ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.

22 Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo;

ndipo mundisungunula mumkuntho.

23 Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,

ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.

24 Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lake kodi?

Akati aonongeke, safuulako kodi?

25 Kodi sindinamlirire misozi wakulawa zowawa?

Kodi moyo wanga sunachitire chisoni osowa?

26 Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa,

ndipo polindira kuunika unadza mdima.

27 M’kati mwanga mupweteka mosapuma,

masiku a mazunzo andidzera.

28 Ndiyenda ndili wothimbirira osati ndi dzuwa ai;

ndinyamuka mumsonkhano ndi kufuula.

29 Ndili mbale wao wa ankhandwe,

ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.

30 Khungu langa lada, nilindifundukira;

ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.

31 Chifukwa chake zeze wanga wasandulika wa maliro,

ndi chitoliro changa cha mau a olira misozi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/30-67d2b39b09e0b82ceb31f255ca7e2ec1.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *